Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 4/15 tsamba 3-4
  • Kodi Tsogolo Lathu Linalembedweratu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tsogolo Lathu Linalembedweratu?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu Anaikiratu za Mtsogolo Mwathu?
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Kufunafuna Tsogolo la Munthu
    Galamukani!—1999
  • Kodi Kukhulupirira Kuikidwiratu Kumalamulira Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi N’chikonzero cha Mulungu Kapena Zangochitika?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 4/15 tsamba 3-4

Kodi Tsogolo Lathu Linalembedweratu?

MKRISTU, Msilamu, Myuda, Mhindu, kapena munthu wachipembedzo china​—anthu a zikhulupiriro zosiyanasiyana amakumana ndi ngozi ndipo amamva chisoni kwambiri ndi zimenezo.

Mwachitsanzo, pa December 6, 1997, mumzinda wa ku Siberia wotchedwa Irkutsk munachitika ngozi yoopsa kwambiri. Ndege yonyamula katundu ya AN-124 inali itangoyamba kumene kuuluka ndipo kenaka ziŵiri mwa injini zake zinazima. Ndegeyo, imene inali ndi mafuta ambiri, inagwera panyumba zolumikizanalumikizana. Nyumba zingapo zinayaka moto, umene unapha ndi kuvulaza eni nyumba ambiri osoŵa chochitawo, kuphatikizapo ana osadziŵa kanthu.

M’dera limene ngozi imeneyi inachitikira ku Siberia, mosakayika konse kuli anthu a zikhulupiriro zosiyanasiyana za chipembedzo. Mwina ena anganene kuti ndi Akristu, komatu angalingalirebe kuti ngozi imeneyo inalembedweratu. Iwo pamodzi ndi anthu enanso mwina analingalira kuti, ‘Chinali Chifuniro cha Mulungu, ndipo chikhala kuti anthu amene anaphedwawo sanafe m’njira imeneyi, iwo akanafa m’njira ina​—zinaikidwiratu kuti adzatero.’

Malingaliro amenewo, kaya olankhulidwa kapena ayi, amasonyeza chikhulupiriro chimene chimapezeka m’zipembedzo zambiri padziko lapansi​—chikhulupiriro cha choikidwiratu. Anthu ambiri amakhulupirira kuti tsogolo lathu linalembedweratu kuyambira tsiku limene tinabadwa mpaka tsiku limene tidzafe.

Kukhulupirira choikidwiratu kumachitika m’njira zosiyanasiyana, zimene zimapangitsa kuti kukhale kovuta kutchula tanthauzo lake lenileni. Kwenikweni mawu akuti choikidwiratu amapereka lingaliro lakuti chochitika chilichonse, ntchito iliyonse, mkhalidwe uliwonse​—kaya chikhale choipa kapena chabwino​—nchosapeŵeka; chiyenera kuchitika basi popeza kuti chinalinganizidwa kale ndi mphamvu ina yaikulu kwambiri yoti munthu sangaipeŵe. Kupenda nyenyezi, chiphunzitso cha Ahindu ndi Abuda cha karma, ndiponso chiphunzitso cha m’Dziko Lachikristu cha kuikiratu zamtsogolo, zimasonyeza chikhulupiriro chimodzimodzicho. Kalelo mu Babulo wakale, anthu anali kukhulupirira kuti milungu ndiyo imapanga zoikidwiratu ndi tsogolo ndipo inalemba zimenezi m’mabuku. Anali kulingalira kuti mulungu aliyense amene amalemba “mabuku ameneŵa a choikidwiratu” angalinganize zoikidwiratu zodzachitikira anthu, maufumu, ndipo ngakhale milungu yomweyo.

Okhulupirira ambiri amati mwa chosankha chaumulungu chochitika munthu asanabadwe, Mulungu amasankhiratu zonse zimene zidzachitikira anthu, kuphatikizapo utali wa moyo wawo, kaya adzakhala aamuna kapena aakazi, olemera kapena osauka, achisoni kapena achimwemwe. Iwo amati zonsezi nzimene Mulungu amalingalira kapena kuti anazilemba m’buku zisanachitike. Choncho, ngati kwagwa tsoka, kaŵirikaŵiri wokhulupirira amati “mektoub,”​—kwalembedwa! Iwo amalingalira kuti popeza kuti Mulungu amadziŵiratu chilichonse chisanachitike, ayeneranso kuti amalinganiziratu amene adzamumvera ndi amene sadzamumvera. Choncho anthu ambiri ochirikiza chikhulupiriro chimenechi amakhulupirira kuti ngakhale munthu asanabadwe, Mulungu amakhala atalinganiziratu kuti kaya adzakhala ndi chimwemwe chosatha m’Paradaiso kapena adzalandira chiweruzo chosatha.

Mwina mungalingalire kuti zimenezi nzofanana kwambiri ndi chiphunzitso cha choikidwiratu chimene amaphunzitsa m’matchalitchi ena a m’Dziko Lachikristu. Munthu wachiprotesitanti amene anachirikiza kwambiri chiphunzitso cha choikidwiratu anali John Calvin, Mfalansa Wokozanso zinthu amene anakhalako m’zaka za zana la 16. Iye anatanthauzira mawu akuti choikidwiratu kuti ndi “chosankha chosatha cha Mulungu, mmene analinganiziratu zimene iye afuna kuchita ndi munthu aliyense. Si onse amene analengedwa mumkhalidwe wofanana, koma ena analinganizidwiratu kuti adzakhala ndi moyo wosatha ndipo ena adzalangidwa kosatha.” Calvin anafotokozanso kuti: “Mulungu sanangodziŵiratu chabe za kulephera kwa munthu woyamba, ndiponso chiwonongeko cha mibadwo yamtsogolo kudzera mwa iye; koma chinalinso chikonzero chake.”

Komabe, si anthu onse a m’zipembedzo zimene zimaphunzitsa za choikidwiratu kapena za tsoka loikidwiratu amene amakhulupirira zimenezo. Ena amanena molondola kuti zolemba zachipembedzo zimanena kuti munthu ali ndi ufulu wa kusankha. Ndithudi, pakhala mikangano yaikulu yokhudza ntchito za munthu, kuti kaya zilidi zinthu zochitika mwa kusankha kwaufulu kwa munthuyo kapena zinalinganizidwiratu ndi Mulungu. Mwachitsanzo, ena amanena kuti munthu ayenera kukhala ndi ufulu wa kusankha ndi kuchita chilichonse, popeza kuti Mulungu, amene ali wolungama, amati munthu aliyense adzadziŵerengera mlandu wa ntchito zake. Ena amanena kuti Mulungu anakonzeratu ntchito za munthu ndipo munthuyo “amangokhala” nazo ndipo amayenera kuzisamalira. Komabe, ambiri amanena kuti chochitika chilichonse, chachikulu kapena chaching’ono, m’moyo wathu watsiku ndi tsiku chinalinganizidwiratu ndi Mulungu.

Kodi inuyo mumakhulupirira chiyani? Kodi Mulungu analinganiziratu mmene tsogolo lanu lidzakhalira? Kodi anthu alidi ndi ufulu, ufulu wokhoza kupanga zosankha za moyo wawo wamtsogolo? Kodi tsogolo lathu limasonkhezeredwa ndi zochita zathu kufikira pati? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

SEL/​Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena