Dziko Lapansi—Kodi Linakhaliraponji?
Pali funso limene muyenera kulingalirapo: Kodi pulaneti lathu lokongolali linalengedwa ndi Mlengi wanzeru amene ali ndi chifuno chokhudza dziko lapansi ndi anthu amene akukhalamo? Kufotokoza nkhani imeneyo mokukhutiritsani kungakuthandizeni kuona tsogolo la pulaneti lathu.
ASAYANSI ambiri amene aphunzira kwambiri za chilengedwe chonse ndi dziko lathu lapansi aona maumboni osonyeza kuti kuli Mlengi, kuti Mulungu ndiye anazilenga. Talingalirani za ndemanga za mmodzi yekha:
Profesa Paul Davies analemba m’buku lotchedwa The Mind of God (Malingaliro a Mulungu) kuti: “Kukhalapo kwa chilengedwe cholongosoka, chogwirizana ndiponso chokhala ndi zinthu zokhazikika, zolinganizidwa bwino, ndiponso zocholoŵana kumafuna malamulo ndi mikhalidwe ya mtundu wina wapadera kwambiri.”
Atafotokoza za “zinthu zochitika mwamwayi” zingapo zimene anthu odziŵa za kapangidwe ka zinthu zakuthambo ndi ena aona, Profesa Davies anawonjezera kuti: “Zonse pamodzi, zikusonyeza umboni wochititsa chidwi wakuti moyo womwe timadziŵawu umadalira kwambiri pa malamulo a zinthu zachilengedwe, ndi pa zinthu zimene zikuoneka monga kuti zinachitika mwamwayi pamlingo woyenerera wa kulemera kwa zinthuzo, nyonga yake, ndi zina zotero, zimene chilengedwe chinasankha. . . . Tinene kuti ifeyo titakhala Mulungu, ndi kusankha mlingo wa zinthuzo mwa kutchuna mabatani angapo mosaganizira bwino, tingapeze kuti mmene tatchunira mabatani onsewo chilengedwe chonse sichingakhale ndi zamoyo. Nthaŵi zina zimaoneka monga kuti mabatani onsewo ayenera kutchunidwa bwino ndendende pamlingo woyenerera kuti chilengedwe chonse chikhale ndi zamoyo. . . . Nzochititsa nthumanzi kuona kuti ngakhale kusintha kwakung’ono zedi kwa zinthu zachilengedwe kungalepheretse munthu kudziŵa za chilengedwe chonse.”
Zimene ena amatengapo pamenepa nzakuti dziko lathu lapansi, pamodzi ndi chilengedwe china chonse, zinapangidwa ndi Mlengi wokhala ndi chifuno. Ngati zili motero, tiyenera tidziŵe kaye chifukwa chimene analilengera dziko lapansi. Tiyeneranso kudziŵa, ngati tingathe, chifuno chake chokhudza dziko lapansi. Pamenepa pamaonekera kusagwirizana kodabwitsa kwa zochita. Ngakhale kuti anthu okana Mulungu ali kulikonse, anthu ochuluka amakhulupirirabe mwa Mlengi wanzeru. Matchalitchi ambiri a Dziko Lachikristu amangonena pakamwa za Mulungu wamphamvuyonse amene alinso Mlengi wa chilengedwe chathu chonse. Komabe, palibe tchalitchi chilichonse mwa matchalitchi ameneŵa chimene nthaŵi zonse chimanena mwachidaliro ndiponso motsimikiza za chifuno cha Mulungu chokhudza tsogolo la dziko lapansi.
Kodi Baibulo Limati Bwanji?
Kudalira magwero achidziŵitso amene anthu ambiri amati ngochokera kwa Mlengi nkomveka. Magwero amenewo ndiwo Baibulo. Amodzi mwa mawu ake olunjika koposa ndiponso osavuta kumva mpang’ono pomwe onena za tsogolo la dziko lathu lapansi amapezeka pa Mlaliki 1:4. Timaŵerenga kuti: “Mbadwo wina upita, ndipo mbadwo wina ufika: koma dziko lapansi likhalapo kosatha.” (King James Version) Baibulo limafotokoza momveka chifukwa chimene Yehova Mulungu analengera dziko lapansi. Limasonyezanso kuti analiika pamalo oyenera kwambiri m’thambo ndiponso pamtunda wabwino ndi dzuŵa lathu kuti m’dziko mukhale zamoyo. Mulungu Wamphamvuyonse anauzira mneneri wakale Yesaya kuti alembe kuti: “Atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.”—Yesaya 45:18.
Komano bwanji zakuti munthu akupeza njira zowonongera chamoyo chilichonse padziko lapansi? Mwa nzeru zake zosayerekezereka, Mulungu akulengeza kuti iye adzaloŵererapo anthu asanawononge chamoyo chilichonse papulaneti lathu. Tamvani lonjezo lotsimikiza limeneli lopezeka m’buku lomaliza la m’Baibulo, Chivumbulutso: “Amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthaŵi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, aang’ono ndi aakulu; ndi kuwononga iwo akuwononga dziko.”—Chivumbulutso 11:18.
Yehova akutiuza chimene chinali chifuno chake choyambirira polenga dziko lapansi, ngale ya mumlengalengayi monga momwe wopita kuthambo wina anafotokozera pozungulira dziko lapansi. Chifuno cha Mulungu chinali chakuti lonse likhale paradaiso, lodzaza anthu pamlingo woyenera—amuna ndi akazi—onse okhala mumtendere ndi umodzi. Analinganiza kuti pang’onopang’ono pulanetili lidzaze anthu mwa kulola anthu aŵiri oyambawo kubala ana. Kuti anthu aŵiri oyambawo azisangalala ndi kukondwera, Yehova anapanga chigawo chaching’ono cha dziko lapansi kukhala paradaiso. Pamene mabanja a anthu anali kudzapitiriza kubalana m’kupita kwa zaka ndiponso zaka mazana, munda wa Edene unayenera kufutukuka pang’onopang’ono mpaka Genesis 1:28 atakwaniritsidwa: “Mulungu . . . adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.”
Tsopano pamene tikuona mkhalidwe wochititsa chisoni wa dziko lapansi ndi okhalamo ake, kodi zikutanthauza kuti chifuno choyambirira cha Mulungu chokhudza dziko lapansi chalephera? Kapena kodi wasintha chifuno chake ndi kugamula kuti chifukwa cha kupanduka kwa anthu, adzalekerera dziko lapansi kuti liwonongekeretu ndi kuyambanso lina, kunena kwake titero? Iyayi, ndife otsimikiza kuti zonse ziŵirizo si zoona. Baibulo limatiuza kuti chilichonse chimene Yehova wafuna kuchichita chimadzachitikabe m’kupita kwa nthaŵi, kuti palibe chosankha chake chimene chingatsekerezedwe ndi munthu aliyense kapena ngakhale ndi chochitika chamwadzidzidzi. Iye akutitsimikizira kuti: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”—Yesaya 55:11.
Chifuno cha Mulungu Chidukizidwa, Osati Kusinthidwa
Adamu ndi Hava atapanduka ndipo atachotsedwa m’munda wa Edene, zinali zoonekeratu kuti chifuno cha Mulungu chopanga dziko lapansi kukhala paradaiso chidzakwaniritsidwa popanda iwo. Komabe, nthaŵi yomweyo Yehova anasonyeza kuti ena a ana awo adzakwaniritsa lamulo lake loyambalo. Nzoona kuti zimenezo zinali kudzatenga nthaŵi yaitali, ngakhale zaka mazana ambiri, koma palibe pomwe pakusonyeza nthaŵi imene ikanapitapo kuti lamulo lake loyamba likwaniritsidwe ngakhale onse aŵiri Adamu ndi Hava atati anapitirizabe kukhala angwiro. Choonadi nchakuti podzafika kumapeto kwa Ulamuliro wa Kristu Yesu wa Zaka Chikwi—kuposapo pang’ono pazaka chikwi kuyambira tsopano—mkhalidwe wa Edene wa Paradaiso udzakuta dziko lonse lapansi ndipo pulaneti la Dziko Lapansi lidzadzala ndi anthu amtendere ndiponso achimwemwe amene ali mbadwa za anthu aŵiri oyambawo. Ndithudi, mphamvu ya Yehova monga Wachifuno wosalephera idzatsimikizidwa kwamuyaya!
Pamenepo maulosi osangalatsa amene Mulungu analosera kalekale adzakwaniritsidwa. Malembawo monga Yesaya 11:6-9 adzakwaniritsidwa mwaulemerero: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chilombo zidzadya pamodzi; ndipo ana awo aang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzaseŵera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’funkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”
Thanzi lofooka ndi matenda osachiritsika zidzakhala zinthu zakale, monga momwe idzakhalira imfa yeniyeniyo. Mawu opezeka m’buku lomaliza la m’Baibulo ngolunjika ndiponso ngomveka mosavuta. Iwo amati: “Chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Inde, tiyeni tikhale ndi chidaliro—pulaneti lathu lokongolali la Dziko Lapansi lidzakhalapobe. Ukhaletu mwayi wanu wopulumuka mapeto a dongosolo la zinthu loipali, ndi ntchito zake zonse zowononga dziko lapansi. Dziko loyera latsopano lokonzedwa ndi Mulungu lili pafupi kwambiri tsopano. Ndipo okondedwa ambiri adzaukitsidwa kwa akufa mwa chozizwitsa cha chiukiriro. (Yohane 5:28, 29) Ndithudi, dziko lathu lapansi lidzakhalapobe, ndipo tingakhale nalo pamodzi ndi kusangalala nalo.