Olengeza Ufumu Akusimba
“M’Bwalo la Malonda Masiku Onse”
MTUMWI Paulo anagwiritsira ntchito mpata uliwonse kulalikira uthenga wa Ufumu. Pofuna kupeza oyenerera, iye anatsutsana “ndi Ayuda m’sunagoge . . . ndi m’bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nawo.”—Machitidwe 17:17.
Changu chotere chakhala chizindikiro cha olambira oona a Yehova chiyambire m’zaka za zana loyamba C.E. (Mateyu 28:19, 20) Lerolino, Mboni za Yehova zikugwiritsiranso ntchito njira zosiyanasiyana pothandiza mwachangu anthu amaganizo abwino kuti akhale ndi chidziŵitso cholongosoka cha choonadi. (1 Timoteo 2:3, 4) Chokumana nacho chotsatirachi chochokera ku Australia chikusonyeza zimenezi.
Masiku asanu mlungu uliwonse, Sid ndi Harold amalandirana kugaŵira zofalitsa zozikidwa pa Baibulo pakathandala ka pafupi ndi malo okwerera sitima zapamtunda ku Sydney. Iwo akhala akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’njira imeneyi kwa zaka pafupifupi zisanu tsopano. Sid, amene ali ndi zaka 95 zakubadwa, anafotokoza kuti: “Nditakwanitsa zaka 87, ndinayamba kulephera kuyendetsa galimoto. Zimenezi zinandikhumudwitsa chifukwa chakuti ndinkakonda ntchito yochitira umboni wapoyera. Tsiku lina pamene ndinali pafupi ndi malo otchuka okopa alendo otchedwa Echo Point ku Katoomba, ndinaona mmisiri wina akugulitsa zithunzi zojambulidwa ndi utoto zosonyeza malo osiyanasiyana. Zojambulazo ndinazionetsetsa ndipo kenaka ndinadzilankhulira kuti, ‘ndili ndi zithunzi zabwino kuposa zimenezi m’chola changa chochitira umbonichi—ndipo nzotsika mtengo kusiyana ndi zimenezi!’ Choncho, ndinaganiza zomanga kathandala, kukaika pamalo opezeka alendo ambiri, ndi kumagaŵira zofalitsa zozikidwa pa Baibulo zokhala ndi zithunzi zooneka bwino zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
“Zaka zinayi zapitazo, ndinasamutsira kathandalako ku Sydney, ndipo Harold anatsagana nane. Timalandirana kukhala pakathandalapo ndiponso kugwira ntchito ndi mipingo yathu.” Harold, amene tsopano ali ndi zaka 83 zakubadwa, anati: “Kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu panyumba pamakhala anthu ochepa kwambiri. Choncho, kulalikira uthenga wa Ufumu m’njira imeneyi kumatithandiza kufikira anthu kumene amapezeka. Ndithudi, zotsatirapo zake nzosangalatsa. Ntchito yathu yogaŵira mabukuyi njodziŵika bwino m’dziko muno.”
“Ngakhale kuti takhala tikugaŵira mabukuŵa m’malo anayi kapena asanu osiyanasiyana kwa zaka zambiri,” anatero Sid, “anthu sachedwa kutizindikira. Anthu ena amafika kudzagula mabuku. Ena amakhala ndi mafunso ofunika kuyankhidwa. Ndipo ena amangofuna kucheza nafe kwa nthaŵi yochepa. Imeneyi ndiyo nthaŵi yokha imene maulendo anga obwereza amafika kwa ine,” iye anatero kwinaku akumwetulira.
“Kunena zoona, anthu ambiri amasangalatsidwa ndi Baibulo,” anawonjezera motero Harold. “Mwezi umodzi wokha anthu anayi anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni chifukwa cha mabuku amene analandira kwa ife ndiponso chifukwa cha mayankho a m’Baibulo amene tinawapatsa pamene anatifunsa. Zochitika zonga zimenezi zimatilimbikitsa kwambiri.”
Mofanana ndi Sid ndi Harold—ndiponso mofanana ndi mtumwi Paulo—Mboni za Yehova kulikonse zimagwiritsira ntchito njira zosiyanasiyana monga momwe zingathere polalikira uthenga wawo wofunika kwambiri. Choncho, ‘uthenga wabwino’ ukupitirizabe kulalikidwa “padziko lonse lapansi.”—Mateyu 24:14.