Kukanganirana Malo “Opatulika”
PA July 15, 1099, Nkhondo ya Mtanda Yoyamba, imene inalamulidwa ndi papa wa ku Rome, inakwaniritsa cholinga chake cholanda mzinda wa Yerusalemu. Kuphedwa kwa anthu kunali komvetsa chisoni kwambiri! Nzika zomwe zinapulumuka zinali bwanamkubwa ndi wom’yang’anira wake basi, chifukwa choti anapereka chiphuphu. Mtsogoleri wachipembedzo Antony Bridge m’buku lake lotchedwa The Crusades, akufotokoza zomwe zinachitika kwa Asilamu ndi Ayuda ena onse okhala m’mzindawu: “Pamene omenya Nkhondo ya Mtanda anapatsidwa ufulu wochita chomwe afuna mu mzindawu, sanadziletse mpaka atakhetsa mwazi. . . . Anapha mwamuna, mkazi, ndi mwana aliyense wopezeka m’mzindawu . . . Atasoŵa oti aphe, onse pamodzi anayenda . . . kupita ku Tchalitchi cha Holy Sepulchre kukayamika Mulungu.”
Kuyambira pamene omenya nkhondo ya mtanda anapambana, Dziko Lachikristu ladzala mikangano yokhayokha chifukwa cha matchalitchi ake ku Yerusalemu a Roma Katolika, Eastern Orthodox, ndi zipembedzo zina zachikristu zimene zikukangana. M’chaka cha 1850 mkangano wa atsogoleri a zipembedzo zosiyanasiyana wokanganirana malo opatulika a m’Yerusalemu ndi zinthu zina za pamaloŵa kwenikweni ndizo zinayambitsa Nkhondo ya Crimea. Dziko la England, France, ndi Ottoman State linamenyana ndi dziko la Russia ndipo anthu okwanira theka la miliyoni anaphedwa.
Nkhondoyi sinathetse mkangano wa Dziko Lachikristu wokanganira Yerusalemu ndi malo ake opatulika. Panthaŵiyi Aottoman, amene anali kulamulira dziko, anayesa kukhazikitsa mtendere mwa kugaŵa malo opatulikawa kwa zipembedzo zosiyanasiyana. “Njira imeneyi,” akufotokoza motere Dr. Menashe Har-el m’buku lake lotchedwa This Is Jerusalem, kuti, “inavomerezedwa . . . ndi United Nations m’chikalata cha Partition Resolution cha m’November 1947. Chotero ndi lamulo la dziko lonse.” Choncho, Tchalitchi cha Holy Sepulchre chili cha a Roma Katolika, Greek Orthodox, Armenia, Asuriya, ndi Copt. Pomalizira pake, Aitiopiya amati tchalitchichi ndi chawo chotero anamanga nyumba pamwamba pa tchalitchichi kuti mamembala awo ena azikhalamo. Ambiri amaona Tchalitchi cha Holy Sepulchre kukhala malo opatulika kwambiri m’Dziko Lachikristu. Muli akachisi ndi mafano ambiri zedi. Gordon’s Calvary, ndi malo ena otchedwa opatulika, amene Aprotesitanti amawalemekeza chifukwa amati ndi malo amene Yesu anafera ndiponso kuikidwa m’manda.
Kalekale Yesu anauza mkazi amene anali kukhulupirira malo opatulika kuti: “Ikudza nthaŵi, imene simudzalambira Atate kapena m’phiri ili, kapena m’Yerusalemu. . . . Olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:21-24) Choncho, Akristu oona salambira malo opatulika. Kuwonongedwa kwa Yerusalemu wosakhulupirika ndi magulu ankhondo a Roma mu 70.C.E., ndi chenjezo ku Dziko Lachikristu. Kupembedza mafano, magaŵano, ndi mlandu wake wa mwazi sizigwirizana n’kudzinenera kwake kukhala lachikristu. Chotero, lidzaona tsoka limene Mulungu waneneratu limene lidzagwera zipembedzo zonse za Babulo Wamkulu.—Chivumbulutso 18:2-8.