Mavuto Apadera a M’mabanja a Ana Opeza
NDI KOTHEKA KUKHALA NDI MABANJA A ANA OPEZA ACHIMWEMWE! MOTANI?
Mabanja a ana opeza akuchuluka m’madera ambiri a dziko lapansi. Komatu, m’mabanja a ana opeza muli mavuto apadera. Mosakayikira vuto lalikulu kwambiri ndi kulera ana. Komabe, monga momwe nkhani ziŵiri zotsatirazi zidzalongosolera, ana opeza mungawalere bwinobwino.
MALINGA NDI MWAMBO, ABAMBO NDI AMAYI AMENE AMAPEZAMO ANA KALE M’BANJA amanenezedwa zambiri. Mwina ambiri a ife tinamvapo nthano ina yake mu imene mwana anali kuzunzidwa kwambiri ndi kholo lake lomulera, monga nthano ya Cinderella. Ana a ku Ulaya amaphunziranso nthano yotchedwa Snow White and the Seven Dwarfs. Amayi ake omulera a Snow White anadzakhala mfiti mapeto!
Kodi nthano zoterezi zimapereka chithunzi cholondola cha mabanja a ana opeza? Kodi makolo onse amene amapeza m’banja muli ana kale ndi oipadi? Ayi. Ambiri a iwo amawafunira zabwino kwambiri ana amene anawapeza mwa kukwatira, kapena kukwatiwa ndi, kholo lawolo. Koma amayang’anizana ndi mavuto ena amene amakhala m’banja lotereli.
Mavuto a Kulera Ana
Pamene banja loyamba litha, kaŵirikaŵiri zimakhala chifukwa chakuti okwatiranawo anali adakali ana. Pamene akwatiranso kaya kukwatiwanso, kusamalira anawo kungawononge unansi wawo. Akaundula ena amasonyeza kuti mwa mabanja 10 a ana opeza, oposa 4 amasudzulana m’zaka zisanu zoyambirira.
Okwatirana kumenewo sangazindikire nsautso ya m’maganizo, kusadziŵa wom’khulupirira, nsanje ndi kukwiya kumene kholo lobweralo limayambitsa mwa ana opeza. Iwo angalingalire kuti kholo lawo lowabalalo tsopano likukonda kwambiri kholo lobweralo kusiyana ndi iwowo. Ndiponso, kholo lowabala limene linasiyidwa silingamvetse chifukwa chimene anawo amakonderabe munthu amene anali mnzake wa mu ukwati. Mnyamata wina anayesa kufotokoza mmene ankakhalira bwino ndi atate ake womubala, akumati, “Amayi, ndikudziŵa kuti Atate ankakuvutani, koma ine ndikukhala nawo bwinobwino!” Mawu oterowo, ngakhale ali oona, angachititse mayi kunyasidwa kwambiri ndi atate ake a mwanayo.
Bambo wina anavomereza kuti: “Sindinalidi wokonzeka kuthetsa mavuto onse okhudza kulera ana anga opeza. Ndinayamba banja ndili ndi maganizo akuti tsopano popeza kuti ndakwatira amayi awo, ndiye kuti ndine bambo wawo. Zinali zosavuta! Sindinadziŵe mmene anawo anali kukondera atate awo owabala, ndipo ndinali kuchita zinthu zolakwika.”
Pangakhale kusemphana malingaliro makamaka popereka chilango. Ana amafunika kuwalanga mwachikondi, koma kaŵirikaŵiri amadana nacho chilango ngakhale chitaperekedwa ndi kholo lowabala. Ndi kovutadi kwambiri kuchilandira kuchokera kwa kholo lopeza! Kaŵirikaŵiri, pamene wapatsidwa chilango choterocho, mwana wopeza anganene mawu ngati akuti, “Sindinutu bambo wanga!” Mawuwa angakhaledi okhumudwitsa kwambiri kwa kholo lopeza limene limafunira mwanayo zabwino!
Kodi ana opeza angaleredwe bwinobwino? Kodi makolo amene amapezamo ana kale m’banja angachite zinthu m’njira yabwino kuti banjalo lizikhala bwino? Yankho la mafunso onse aŵiri ndi lakuti inde ngati aliyense m’banjamo angamatsatire malangizo omwe ali m’Mawu ouziridwa a Mulungu, Baibulo.
[Chithunzi patsamba 3]
“Sindinutu bambo wanga!”