Buku la Nzeru Lokhala ndi Uthenga Wothandiza Lerolino
“THUMBA lodzaza nzeru ndi lamtengo wapamwamba kuposa thumba lodzaza ngale,” linatero kholo lamakedzana Yobu, limene mosakayikira linali mmodzi mwa anthu achuma koposa m’nthaŵi yake. (Yobu 1:3; 28:18, NW; 42:12) Zoonadi, nzeru ndi yamtengo wapamwamba kwambiri kuposa chuma chakuthupi pothandiza munthu kukhala ndi moyo wabwino. Mfumu Solomo yanzeruyo inati: “Nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.”—Mlaliki 7:12.
Koma kodi nzeru imeneyo ingapezeke kuti lerolino? Anthu amapempha thandizo kwa aphungu a m’manyuzipepala, akatswiri odziŵa za maganizo a munthu, madokotala a matenda okhudza maganizo, ngakhale okonza tsitsi ndi oyendetsa galimoto zonyamula anthu, kuti awathandize pamavuto awo. Ndiponso pali akatswiri osaŵerengeka amene amapereka uphungu pafupifupi pankhani iliyonse—pamtengo wakutiwakuti. Koma nthaŵi zambiri, mawu “anzeru” amenewo angowagwiritsa mwala anthuwo, ngakhale kuwaloŵetsa m’tsoka. Ndiye nzeru yeniyeni tingaipeze motani?
Yesu Kristu, amene anali kudziŵa bwino zochitika za anthu, panthaŵi ina anati: “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Tiyeni tione ena mwa mavuto ofala pamoyo wa anthu ndi kuona mawu anzeru amene awathandizadi ndiponso amene apezeka kukhala a mtengo wapatali kwambiri kwa iwo kuposa “thumba lodzaza ngale.” Mwina inunso mungapeze “thumba lodzaza nzeru” limeneli ndi kupindula nalo.
Kodi Ndinu Wopsinjika Maganizo?
“Ngati zaka za zana la 20 zinayambitsa Nyengo ya Nkhaŵa, kutha kwake kukuyambitsa Nyengo ya Kupsinjika Maganizo,” inatero International Herald Tribune ya ku London. Inawonjezera kuti “kafukufuku woyamba kuchitika m’mayiko osiyanasiyana wa anthu opsinjika maganizo kwambiri akusonyeza kuti vutoli likuwonjezeka ndithu padziko lonse lapansi. M’mayiko okhala ndi anthu amitundumitundu monga Taiwan, Lebanon ndi New Zealand mbadwo uliwonse wotsatira ukumavutika kwambiri ndi vutoli.” Akuti amene anabadwa pambuyo pa 1955 ali pangozi yoŵirikiza katatu ya kupsinjika maganizo kwambiri, kuposa agogo awo.
Ndi zimene zinachitikira Tomoe, amene anali wopsinjika maganizo kwambiri ndipo anali kungogona masiku ambiri. Popeza sanathe kusamalira mwana wake wa zaka ziŵiri zakubadwa, anabwerera kwa makolo ake. Posapita nthaŵi, mnansi wake amene anali ndi mwana wa zaka zolingana ndi za mwana wa Tomoe anapalana naye ubwenzi. Tomoe atauza mnansi wakeyo kuti akudzimva kukhala wopanda pake, mnansi wakeyo anamusonyeza mawu a m’buku linalake. Mawuwo anati: “Ndipo diso silingathe kunena kwa dzanja, Sindikufuna iwe, kapenanso mutu kwa mapazi, Sindikufunani inu. Koma makamakatu ziŵalozo zoyesedwa zofooka m’thupi, zifunika.”a Maso a Tomoe anadzaza misozi pozindikira kuti aliyense ali ndi malo ake padziko lapansi ndipo n’ngwofunika.
Mnansi wakeyo anamuuza kuti zingakhale bwino ataŵerenga buku limene lili ndi mawu amenewo. Tomoe anavomera ndi mutu, ngakhale kuti mpaka nthaŵiyo iye sankatha kuchita kalikonse, ngakhale kupanga lonjezo wamba. Mnansi wakeyo anamuthandizanso kugula zinthu, ndipo anali kuphikira limodzi ndi Tomoe masiku onse. Patapita mwezi umodzi Tomoe anayamba kudzuka mmaŵa tsiku lililonse, kuchapa zovala, kuyeretsa m’nyumba, kupita kokagula zofunikira, ndi kukonza chakudya chamadzulo, monga momwe mkazi wina aliyense wokwatiwa amachitira. Analimbana ndi zovuta zambiri, koma ananena kuti, “Ndinali wotsimikizira kuti ndikangotsatira mawu anzeru amene ndapeza, ndidzakhala bwino.”
Mwa kugwiritsa ntchito mawu anzeru amene anapeza, Tomoe anathetsa masiku ake a kupsinjika maganizo. Tomoe tsopano akugwira ntchito ya nthaŵi zonse yothandiza ena kutsatira mawu amodzimodziwo amene anamuthandiza kupirira mavuto ake. Mawu anzeru amenewo ali m’buku lina lakale limene lili ndi uthenga wothandiza kwa anthu onse lerolino.
Kodi Muli ndi Mavuto a Pabanja?
Padziko lonse lapansi chiŵerengero cha zisudzulo chikukwera. Mavuto a pabanja akuwonjezeka ngakhale kumayiko a Kummaŵa, kumene kale anthu ankanyadira mabanja awo ogwirizana mwathithithi. Kodi n’kuti kumene tingapeze chitsogozo chanzeru chothandiza m’banja?
Talingalirani za Shugo ndi Mihoko, mwamuna ndi mkazi wake amene anali ndi mavuto osatha a pabanja. Nthaŵi zonse ankakangana pankhani zopanda phindu. Shugo anali wamtima wapachala, ndipo Mihoko anali kuyankha mwansontho nthaŵi zonse mwamuna wakeyu akamuimba mlandu. Mihoko anafika polingalira kuti, ‘N’zosatheka kugwirizana pa kalikonse.’
Tsiku lina mkazi wina anachezera Mihoko ndi kumuŵerengera mawu awa m’buku linalake: “Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.”b Ngakhale kuti sanali kukonda zachipembedzo, Mihoko anavomera kuphunzira buku limene linali ndi mawu amenewo. Iye anali kufuna kuwongolera moyo wake wa pabanja. Choncho ataitanidwa kuti apezeke pamsonkhano pamene buku lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe linali kuphunziridwa, Mihoko—ndi mwamuna wake—anavomera ndi mtima wonse.c
Ali pamsonkhanopo, Shugo anaona kuti anthu amene analipo anali kutsatiradi zimene anali kuphunzira ndi kuti anaoneka kukhala anthu achimwemwe kwambiri. Anaganiza zoŵerenga buku limene mkazi wake anali kuphunzira. Posapita nthaŵi, mawu ena anamukopa chidwi: “Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.”d Ngakhale kuti zinamutengera nthaŵi kuti atsatire pulinsipulo limeneli m’moyo wake, kusintha kwake kwapang’onopang’onoko kunaonekera kwa anthu okhala naye pafupi, kuphatikizapo mkazi wake.
Ataona kuti mwamuna wake akusintha, Mihoko nayenso anayamba kutsatira zimene anali kuphunzira. Lamulo lina limene linamuthandiza kwambiri linali lakuti: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa.”e Chotero Mihoko ndi mwamuna wake anati azikambirana za zinthu zabwino zimene amachita ndi mmene angawongolere zinthu m’malo moimbana mlandu. Chotsatirapo chake? Mihoko akukumbukira kuti: “Zandipatsa chimwemwe chachikulu. Takhala tikuchita zimenezi pachakudya chamadzulo masiku onse. Ngakhale mwana wathu wa zaka zitatu zakubadwa amayankhulapo. Zimatitsitsimula zedi!”
Banja limeneli litatsatira uphungu wothandiza umene linalandira, linathetsa mavuto amene anali atawononga unansi wawo kwadzaoneni. Kodi zimenezo si zamtengo wapatali kuposa thumba lodzaza ngale?
Kodi Mukufuna Kukhala ndi Moyo Wabwino?
Kwa ambiri lerolino, cholinga chawo m’moyo ndicho kukhala ndi chuma. Koma wamalonda wina wolemera wa ku United States amene wapereka madola mamiliyoni mazana ambiri kuti athandize anthu osauka anati nthaŵi inayake: “Anthu ena amakonda kwambiri ndalama, koma palibe amene panthaŵi imodzi angavale nsapato ziŵiri kumwendo umodzi.” Ndi ochepa amene amavomereza mfundo imeneyi ndipo ndi ochepa kwambiri amene amaleka kulondola chuma.
Hitoshi anakulira mu umphaŵi, choncho ankakhumba kwambiri kukhala wolemera. Ataona mmene anthu okongoza ena ndalama amadyerera ena, anaganiza kuti: “Wokhala ndi ndalama zambiri ndiye wopambana.” Hitoshi ankakhulupirira kwambiri m’mphamvu ya ndalama moti ankaganiza kuti ngakhale moyo wa anthu ungagulidwe ndi ndalama. Kuti apeze chuma, analimbikira kwambiri pamalonda ake okonza mipope ndipo anali kugwira ntchito chaka chonse, osakhalapo ndi tsiku lopuma. Pamene anali kugwiritsa ntchito motero, Hitoshi posapita nthaŵi anazindikira kuti iye, wopatsidwa ntchito ndi makampani ena, sangathe kukhala wamphamvu monga eni makampani omupatsa ntchitowo. Tsiku ndi tsiku anali kukhumudwa ndipo anali kuopa kuti ndalama zimuthera.
Ndiyeno mwamuna wina anafika pakhomo la Hitoshi ndi kumufunsa ngati akudziŵa kuti Yesu Kristu anamufera. Popeza kuti Hitoshi ankalingalira kuti palibe amene angafere munthu monga iyeyo, anachita chidwi ndipo anavomera kuti adzakambiranenso zina. Mlungu wotsatira, anakamvetsera nkhani inayake ndipo anadabwa kwambiri kumva uphungu wonena za ‘kukhala ndi diso lakumodzi.’ Wokamba nkhaniyo anafotokoza kuti diso “lakumodzi” ndi diso loona patali ndi lolunjikitsidwa pa zinthu zauzimu; koma diso “loipa,” kapena kuti “lakaduka,” ndi lolunjikitsidwa pa zikhumbo zathupi zofunika nthaŵi yomweyo ndipo siliona patali. Uphungu wakuti, “Kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso,” unam’khudza kwambiri.f Pali chinachake chofunika kwambiri kuposa kupeza chuma! Anali asanamvepo mawu ngati amenewo.
Atachita chidwi, anayamba kutsatira zimene anali kuphunzira. M’malo mosaukira ndalama, iye anayamba kuika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo wake. Anakhalanso ndi nthaŵi yosamalira banja lake mwauzimu. Mwachidziŵikire, zimenezo zinatanthauza nthaŵi yochepa yogwira ntchito yake, koma malonda ake anayamba kuyenda bwino. Chifukwa chiyani?
Umunthu wake waukali unasintha kukhala wodekha ndi waubwenzi pamene anayamba kutsatira uphungu umene anapatsidwa. Anachita chidwi kwambiri ndi uphungu wakuti: “Tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka mkamwa mwanu: musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye.”g Kutsatira uphungu umenewu sikunamupatse chuma, koma ‘umunthu wake watsopano’ unapatsa makasitomala ake chithunzi chabwino ndipo anayamba kumukhulupirira ndi kumudalira. Inde, mawu anzeru amene anapeza anamuthandiza kukhala ndi moyo wabwino. Kwa iye, mawuwo anali a mtengo wapatali kwambiri m’lingaliro lenileni kuposa thumba lodzaza ngale, kapena kuti ndalama.
Kodi Mudzalitsegula Thumbalo?
Kodi mwalidziŵa thumba lodzaza nzerulo limene lathandiza kwambiri anthu otchulidwa m’zitsanzo zapamwambazo? Ndiyo nzeru yopezeka m’Baibulo, buku lofalitsidwa koposa ndiponso lopezeka kuposa buku lina lililonse padziko lapansi. Mwinanso muli nalo kapena mukhoza kulipeza mosavuta. Komabe, kungokhala ndi thumba lodzaza ngale za mtengo wapatali koma osazigwiritsa ntchito sikungam’pindulitse mwini wake, nakonso kungokhala nalo basi Baibulo sikungakupindulitseni. Bwanji osalitsegula thumbalo, kunena kwake titero, ndi kutsatira uphungu wanzeru wa m’Baibulo ndi mawu ake a panthaŵi yake ndi kuona mmene lingakuthandizireni kulaka mavuto a m’moyo?
Mutapatsidwa thumba lodzaza ngale, kodi simungakondwere ndi kuyesa kudziŵa munthu amene wakupatsaniyo kuti mum’thokoze? Kodi Wopatsa amene anapereka Baibuloyo mukum’dziŵa?
Baibulo limatchula Gwero la nzeru imene ikupezeka mmenemo pamene limati: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.” (2 Timoteo 3:16) Limatiuzanso kuti “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Ndiye chifukwa chake mawu anzeru opezeka m’Baibulo n’ngapanthaŵi yake ndiponso othandiza kwa ife lerolino. Mboni za Yehova n’zofunitsitsa kukuthandizani kuphunzira zambiri ponena za Wopatsa wooloŵa manja ameneyu, Yehova Mulungu, kuti mukhale ndi chiyembekezo chopindula ndi “thumba lodzaza nzeru” limene lili m’Baibulo—buku la nzeru lokhala ndi uthenga wothandiza kwa anthu lerolino.
[Mawu a M’munsi]
a Mawuwa ndi a pa 1 Akorinto 12:21, 22.
c Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
f Mateyu 6:21-23; NW, mawu a mtsinde.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 4]
Mawu Anzeru Othandiza Kukhala Wokhazikika Maganizo
“Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.”—Salmo 130:3, 4.
“Mtima wokondwa usekeretsa nkhope; koma moyo umasweka ndi zoŵaŵa za m’mtima.”—Miyambo 15:13.
“Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?”—Mlaliki 7:16.
“Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
“Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.”—Aefeso 4:26.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 5]
Mawu Anzeru Othandiza Kukhala ndi Moyo wa Banja Wachimwemwe
“Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.”—Miyambo 15:22.
“Mtima wa wozindikira umaphunzira; khutu la anzeru lifunitsa kudziŵa.”—Miyambo 18:15.
“Mawu oyenera a panthaŵi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.”—Miyambo 25:11.
“[Pitirizani] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”—Akolose 3:13, 14.
“Mudziŵa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.”—Yakobo 1:19.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 6]
Mawu Anzeru Othandiza Kukhala ndi Moyo Wabwino
“Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu um’sekeretsa.”—Miyambo 11:1.
“Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.”—Miyambo 16:18.
“Wosalamulira mtima wake akunga mudzi wopasuka wopanda linga.”—Miyambo 25:28.
“Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m’chifuŵa cha zitsiru.”—Mlaliki 7:9.
“Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri.”—Mlaliki 11:1.
“Nkhani yonse yovunda isatuluke mkamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.”—Aefeso 4:29.
[Chithunzi patsamba 7]
Kuphunzira Baibulo ndiko sitepe loyamba kuti mupindule ndi “thumba lodzaza nzeru”