Nthaŵi ndi Umuyaya—Kodi Timadziŵa Zotani pa Zinthu Zimenezi?
“ZIKUKHALA ngati nthaŵi n’njovuta kwambiri kuti anthu aimvetsetse,” inatero insaikulopediya ina yake. Inde, tinganenedi kuti kuyesa kumasulira nthaŵi mwa mawu osavuta n’kosatheka. Timanena kuti nthaŵi “imatha,” “imapita,” “imathamanga,” inde, timanenanso kuti ifeyo tikuyenda “ndi nthaŵi.” Koma tikamatero, sitidziŵa kwenikweni zimene tikunena.
Nthaŵi yamasuliridwa kuti ndiyo “mtunda umene uli pakati pa zochitika ziŵiri.” Koma malinga ndi zimene tikudziŵa, zikukhala ngati nthaŵi sidalira zochitika; imaoneka kuti imangopitirira kaya chinachake chichitike kapena chisachitike. Wafilosofi wina amakhulupirira kuti kulibe nthaŵi ayi koma kuti yangokhala chinthu chimene anthu amangochiganizira. Kodi n’zoona kuti chinthu chimene moyo wathu umadalira kwambiri choncho chingakhale chongoganizira?
Zimene Baibulo Limanena pa za Nthaŵi
Baibulo silimasulira nthaŵi mwanjira iliyonse, ndipo zimenezi mwina zimaonetsa kuti munthu sangathe kuimvetsa nthaŵi. Ili ngati miyamba yopanda malireyo, imenenso imativuta kumvetsa. Mwachionekere, nthaŵi ndi chimodzi mwa zinthu zimene ndi Mulungu yekha amazimvetsa, pakuti iye yekha ndiye amene ‘ayambira kunthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha.’—Salmo 90:2.
Ngakhale kuti Baibulo silimasulira nthaŵi, limanenabe kuti nthaŵi ndi yeniyeni. Poyamba, Baibulo limatiuza kuti Mulungu analenga “zounikira”—dzuŵa, mwezi, ndi nyenyezi—monga zizindikiro za nthaŵi, “zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka.” Zochitika zambiri zolembedwa m’Baibulo zili ndi nthaŵi yakeyake. (Genesis 1:14; 5:3-32; 7:11, 12; 11:10-32; Eksodo 12:40, 41) Ponena za nthaŵi, Baibulo limanenanso kuti tiyenera kuigwiritsa ntchito mwanzeru kuti tikalandire madalitso a Mulungu a umuyaya—chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha.—Aefeso 5:15, 16.
Moyo Wosatha—Kodi n’Zomveka?
Monga kulili kovuta kumvetsa kuti nthaŵi ndi chiyani, anthu ambiri zimawavutanso kwambiri kumvetsa lingaliro lakuti kuli moyo wosatha, kapena kuti anthu adzakhala ndi moyo kosatha. Chochititsa zimenezi chingakhale chakuti nthaŵi zonse ife timaona nthaŵi malinga ndi moyo wa munthu kuchokera pa kubadwa kwake, kukula, ukalamba, ndi imfa. Choncho, kwa ifeyo kukalamba kwa munthu n’kumene kumatiuza mmene nthaŵi ikuyendera. Kwa ambiri, kuganiza zosiyana ndi zimenezi kungaoneke ngati kutsutsana ndi mmene nthaŵi taidziŵira. Iwo angafunse kuti, ‘Kodi anthu angasiyane bwanji ndi zolengedwa zina zonse zamoyo zimenenso zimakalamba?’
Zimene iwo nthaŵi zambiri amaiŵala poganiza zimenezi n’zakuti anthu ali kale osiyana m’njira zambiri ndi zolengedwa zina. Mwachitsanzo, nyama zilibe nzeru zimene anthu ali nazo. Ngakhale ngati ena anganene zina, nyama sizitha kuchita mwaluso kuposa pamene nzeru zake zachibadwa zimafika. Zilibe mphatso yokhala ndi maluso osiyanasiyana kapena mphamvu yoonetsa chikondi ndi yomvetsa zinthu imene anthu ali nayo. Ngati anthu anapatsidwa mikhalidwe ndi maluso ambiri chonchi amene amapangitsa moyo kukhala watanthauzo, kodi zingakhale zotheka bwanji kuti asapatsidwenso nthaŵi yochuluka ya moyo weniweniwo?
Komanso, kodi si zodabwitsa kuti mitengo, imene siganiza, nthaŵi zina imakhala zaka zikwi zambiri, pamene anthu anzeru amangokhala zaka 70 kapena 80? Kodi sizikudabwitsani kuti akamba, amene alibe nzeru kapena maluso osiyanasiyana, angakhale zaka zoposa 200, pamene anthu, amene ali ndi maluso amenewo ochuluka, satha kukhala ndi moyo ngakhale theka la zakazo?
Ngakhale kuti anthu satha kumvetsa nthaŵi ndi umuyaya, lonjezo la moyo wosatha lidakali chiyembekezo cholimba cha m’Baibulo. Mmenemo, mawu akuti “moyo wosatha” amapezeka pafupifupi nthaŵi 40. Komano ngati cholinga cha Mulungu n’chakuti anthu akhale ndi moyo wosatha, n’chifukwa chiyani sanachikwaniritse cholingacho? Funso limeneli lidzayankhidwa m’nkhani yotsatira.