Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 10/1 tsamba 3-4
  • N’chifukwa Chiyani Nthaŵi Imachepa Chonchi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Nthaŵi Imachepa Chonchi?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nthaŵi Yochuluka
  • Nthaŵi Ikucheperachepera
  • Sitokhafe Tili ndi Nthaŵi Yochepa
  • Kugwiritsa Ntchito Mwanzeru Nthaŵi Yomwe Tilinayo Panopa
  • Yehova Amatidziŵitsa Kuŵerenga Masiku Athu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Nthaŵi ndi Umuyaya—Kodi Timadziŵa Zotani pa Zinthu Zimenezi?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kuyenda ndi Mulungu—Tikumadikira Umuyaya
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Tamandani Mfumu Yamuyaya!
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 10/1 tsamba 3-4

N’chifukwa Chiyani Nthaŵi Imachepa Chonchi?

NTHAŴI. Kungakhale kovuta kuti tilongosole liwulo mwatsatanetsatane, koma tikudziŵa kuti nthaŵi zambiri sitimakhala ndi nthaŵi yokwanira. Timadziŵanso kuti imafulumira. Kunena zoona, timadandaula kaŵirikaŵiri kuti, “Nthaŵi ikuthamanga.”

Komatu, wandakatulo wachingelezi Austin Dobson ananenadi zoona pamene mu 1877 ananena kuti: “Mukunena kuti, nthaŵi imatha? Ayi, sizoona! Kalanga ine, Nthaŵi imatsala, timatha ndife.” Kuchokera pamene Dobson anamwalira mu 1921, iye wakhala palibe kwa zaka pafupifupi 80 tsopano; nthaŵi ikupitirirabe.

Nthaŵi Yochuluka

Ponena za Mlengi wa anthu, Baibulo limatiuza kuti: “Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha, Inu ndinu Mulungu.” (Salmo 90:2) Kapena malinga ndi The New Jerusalem Bible, “kuyambira umuyaya kufikira umuyaya inu ndinu Mulungu.” Choncho nthaŵi idzakhalako mpaka kalekale monga momwe Mulungu mwini adzakhalira​—kosatha!

Mosiyana kwambiri ndi Mulungu, amene ali ndi umuyaya wa nthaŵi, timaŵerenga za anthu kuti: “Pakuti masiku athu onse apitirira m’ukali wanu; titsiriza moyo wathu ngati lingaliro. Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikakhala nayo mphamvu ndi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.”​—Salmo 90:9, 10.

N’chifukwa chiyani moyo uli waufupi choncho lerolino, pamene Baibulo limatiphunzitsa momveka bwino kuti cholinga cha Mulungu n’chakuti munthu akhale ndi moyo kosatha? (Genesis 1:27, 28; Salmo 37:29) M’malo mokhala ndi moyo wopanda malire mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu, n’chifukwa chiyani anthu, ngati zonse zawayendera bwino, pa avareji amakhala masiku osaposera 30,000? N’chifukwa chiyani anthu ali ndi nthaŵi yochepa chonchi? Ndani kapena n’chiyani chimachititsa mkhalidwe womvetsa chisoni umenewu? Baibulo limapereka mayankho omveka bwino ndi okhutiritsa.a

Nthaŵi Ikucheperachepera

Anthu achikulire angavomereze kuti m’zaka zaposachedwapa zochitika m’moyo zakhala zofulumira kwambiri. Mtolankhani wina wamkazi, Dr. Sybille Fritsch, ananena kuti m’zaka 200 zapitazo nthaŵi imene anthu amagwira ntchito pa mlungu yatsika kuchokera pa maola 80 kufika pa maola 38, “komabe zimenezi sizinathetse kudandaula kwathu ponena za kuchepa kwa nthaŵi.” Iye analongosola kuti: “Palibe nthaŵi yokwanira; nthaŵi ndi ndalama; kufuna nthaŵi momwe timafunira kupuma; moyo n’ngwotanganidwa.”

Njira zatsopano zochitira zinthu zatsegula mipata yochita zinthu zimene anthu a mibadwo yam’mbuyomo sanalingalirepo n’komwe. Koma pamene mipata yochita zinthu zochuluka iwonjezeka, m’pamenenso anthu akugwiritsidwa mwala chifukwa cha kuchepa kwa nthaŵi yopangira zinthu zimenezo. Masiku ano, m’madera ambiri a dziko lapansi, anthu ali ndi nthaŵi yochepa yochitira zinthu, kuchoka pa ntchito ina kupita pa ina. Abambo ayenera kupita kuntchito nthaŵi ya 7:00 a.m., Amayi apite ndi ana kusukulu pa 8:30 a.m., Agogo aamuna ayenera kuonana ndi dokotala pa 9:40 a.m., ndipo tonsefe tikonzekere msonkhano wofunika kwambiri pa 7:30 p.m. Poyesayesa kuchita zinthu zonse panthaŵi yake, pamakhala nthaŵi yochepa yoti n’kupumula. Ndipo timadandaula za ntchito yosakondweretsa ndi yotopetsa ya tsiku ndi tsiku, ndiponso za kufulumira kwa nthaŵi.

Sitokhafe Tili ndi Nthaŵi Yochepa

Mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, amene chiwembu chake chinachititsa kuti mtundu wa anthu ukhale ndi moyo waufupi, tsopano akuzunzika chifukwa cha kuipa kwake. (Yerekezani ndi Agalatiya 6:7, 8.) Ponenapo za kubadwa kwa Ufumu Waumesiya kumwamba, Chivumbulutso 12:12 chimatipatsa chiyembekezo pamene chimati: ‘Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kam’tsalira kanthaŵi.’

Malinga ndi mmene Baibulo limalongosolera nthaŵi ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi ake, tsopano tikukhala kumapeto a “kanthaŵi” kameneko. Ndi chosangalatsatu kudziŵa kuti nthaŵi yeniyeni ya Satana itha posachedwapa! Atachotsedwapo, anthu omvera adzabwezeretsedwa kukhalanso angwiro, ndipo adzalandira moyo wosatha umene Yehova anawalinganizira pachiyambi. (Chivumbulutso 21:1-4) Sipadzakhalanso vuto la kuchepa kwa nthaŵi.

Kodi mutha kuyerekezera tanthauzo la kukhala ndi moyo wosatha​—kukhala ndi moyo wamuyaya? Simudzavutikanso maganizo ndi zinthu zimene simunachite. Ngati mukufuna nthaŵi yambiri, mudzaipeza maŵa, kapena mlungu wamaŵa, kapena chaka chamaŵa​—ndithudi, muli ndi nthaŵi yamuyaya wonse yochita ntchitoyo!

Kugwiritsa Ntchito Mwanzeru Nthaŵi Yomwe Tilinayo Panopa

Podziŵa kuti nthaŵi yake yosonkhezera anthu yatsala pang’ono kutha, Satana akuyesayesa kutanganitsa anthu kwambiri moti alibe nthaŵi yomvetsera uthenga wabwino wa Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu. Choncho, tidzachita bwino kumvera chenjezo la Mulungu lakuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵitsani chifuniro cha Ambuye n’chiyani.”​—Aefeso 5:15-17.

N’kofunika kuti tigwiritse ntchito nthaŵi yathu pazinthu zofunika kwambiri m’malo moithera pazochita zopanda pake zimene sizingatibweretsere phindu lamuyaya! Tiyenera kukulitsa mzimu umene Mose anasonyeza pamene anapempha Yehova m’mawu ochokera pansi pa mtima aŵa kuti: “Mutidziŵitse kuŵerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.”​—Salmo 90:12.

Zoonadi, aliyense m’dziko lerolino ndi wotanganidwa. Komabe, Mboni za Yehova zikukulimbikitsani kuchokera pansi pa mtima kutherako ina mwa nthaŵi yanu ya mtengo wapataliyo kuphunzira zofuna za Mulungu zopezera moyo wosatha muulamuliro wa Ufumu wake. Kuphunzira Baibulo mwadongosolo kwa ola limodzi pa mlungu, ‘kudziŵa chifuniro cha Ambuye n’chiyani,’ kungakupangitseni kudzaona ndi maso anu kukwaniritsidwa kwa mawu aŵa akuti: “Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthaŵi zonse. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:27, 29.

[Mawu a M’munsi]

a Onani buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, mutu 6, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena