Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Popeza tsopano akuti ngati utafuna n’kotheka kutsegulitsa utatsata njira yolera yotseketsa, kodi Mkristu angatsate njira yakulera imeneyo?
Kutseketsa ndiko kwakhala njira yofala kwambiri ya kulera. Anthu ambiri amalola kapena kukana njirayo malinga ndi kumene anakulira ndi maphunziro awo, komanso chipembedzo. Nkhani ya chipembedzo ndi imene imakhudza Mboni za Yehova, zimene zili ndi chikhumbo chonga cha wamasalmo chakuti: “Mundiphunzitse njira yanu, Yehova, munditsogolere pa njira yachidikha [“yowongoka,” NW].” (Salmo 27:11) Kodi kutseka kumachitidwa motani?
Kwa amuna, njira yolera ya kutseketsa imatchedwa kuti vasectomy. Njira ziŵiri za ubwamuna m’machende amazidula ndi kuzitseka. Amatha kuchita zimenezi m’njira zosiyana zachipatala, koma cholinga chake chimakhala kutsekereza ubwamuna kuti usadutse kuchokera m’machende. Kwa akazi, kutseka kumatchedwa tubal ligation. Nthaŵi zambiri amachita zimenezi mwa kudula ndi kumanga (kapena, kuwotcha) njira yodzera mazira mmene mumadutsa mazira kuchokera kumene amapangikira kupita ku chibelekero.
Kuyambira kalekale njira zimenezi zinali kuonedwa kuti n’zachikhalire—kuti ukatseketsa sungatsegulitsenso. Koma amuna ndi akazi ena, pochita chisoni ndi njira imene anatsatayo kapena chifukwa cha kusintha kwa zinthu, afunafuna chithandizo cha zachipatala kuti atsegulitsenso. Ndi kudza kwa zipangizo zochitira ntchitoyo komanso maopaleshoni a ziwalo zing’onozing’ono, kuyesa kutsegulanso anthu otsekedwa kwayamba kutheka kwambiri. N’kofala kuŵerenga kuti mwa anthu osankhidwa pangakhale 50 mpaka 70 peresenti ya amuna amene anatha kuwatsegulanso mwa kulumikizanso njira za ubwamunazo. Ena akunena kuti 60 mpaka 80 peresenti ya akazi amatsegulidwanso bwino lomwe. Ena amene amva nkhani imeneyi akuona kuti kutseketsa sikuyenera kuonedwanso ngati kosabwezeka. Mwina amakhulupirira kuti mwamuna kapena mkazi akatsekedwa n’chimodzimodzi n’kuti akugwiritsa ntchito njira zolera za mapilisi, makondomu, ndi ma diaphragm—njira zimene angalekeze ngati akufuna kukhala ndi mwana. Komabe, mbali zina zofunika kwambiri siziyenera kunyalanyazidwa.
Mfundo imodzi ndi yakuti chiyembekezo choti munthu n’kutsegulidwanso chingakhudzidwe kwambiri ndi zinthu monga mlingo wa kuwonongedwa kwa njirazo, utali wa mtsempha umene unachotsedwa kapena kuwonongedwa, zaka zimene zapitapo kuchokera pamene munthuyo anatsekedwa, ndipo kwa amuna, kaya maselo opha ubwamuna anapangika kapena ayi. Komanso mfundo ina imene siyenera kunyalanyazidwa ndi yakuti kumalo ochuluka kungakhale kulibe zipangizo zochitira opaleshoni ya ziwalo zing’onozing’ono, kapena mtengo wake ungakhale wapamwamba kwambiri. Chotero, ochuluka amene anatseketsa amene angafune kutsegulitsa mwina sangakwanitse kutero. Kwa iwo n’zosatheka kusinthanso.a Chotero ziŵerengero zimene zatchulidwazo zangokhala nkhambakamwa, osati zimene munthu angadalire.
Mfundo zinanso n’zofunika kuziganizira. Nkhani ina yofalitsidwa ku United States yonena za kutsegulitsa mwa amuna inanena kuti pambuyo pa opaleshoni ya $12,000, “63 peresenti yokha ya amunawo ndi amene angathe kupatsa akazi awo mimba.” Koma ndi 6 peresenti yokha ya amuna amene amatseketsa amene pambuyo pake amafuna kutsegulitsa.” M’kafukufuku wina wa ku Germany wofufuza chigawo chapakati cha Ulaya, amuna ngati 3 peresenti amene anasankha kutsekedwa anafuna kutsegulitsa pambuyo pake. Ngakhale kuti theka la ofuna kutsegulitsawo anatsegulitsadi, zimenezo zingatanthauze kuti kwa 98.5 peresenti ya amuna, sangatsegulitsenso atatseketsa. Ndipo chiŵerengero chimenecho n’chachikulu m’mayiko mmene mulibe madokotala ambiri ochita opaleshoni ya ziwalo zing’onozing’ono kapena mmene mulibiretu madokotalawo.
Chotero si kwanzeru kuona kutseketsa kwa amuna kapena akazi mopepuka, monga kuti ndi njira yosakhalitsa ya kulera. Ndipo kwa Akristu oona mtima, palinso mbali zina zofuna kuziganizira.
Mfundo yaikulu ndi yakuti mphamvu zoberekera ndi mphatso yochokera kwa Mlengi wathu. Chifuno chake choyambirira chinaphatikizapo kubalana kwa anthu angwiro, amene anayenera ‘kudzaza dziko lapansi, kuligonjetsa.’ (Genesis 1:28) Chigumula chitachepetsa chiŵerengero cha anthu padziko lapansi kukhala anthu asanu ndi atatu, Mulungu anabwerezanso malangizo aakulu amenewo. (Genesis 9:1) Mulungu sanabwereze lamulo limeneli ku mtundu wa Israyeli, koma Aisrayeli ankaona kukhala ndi ana ngati chinthu chosiririka kwabasi.—1 Samueli 1:1-11; Salmo 128:3.
Chilamulo cha Mulungu kwa Aisrayeli chinkasonyeza kuti iye amalemekeza mphamvu ya kubala ya anthu. Mwachitsanzo, ngati mwamuna wokwatira anamwalira wopanda mwana wamwamuna woti apitirize mzere wake, mbale wake anayenera kubala mwana wamwamuna mwa ukwati wapachilamu. (Deuteronomo 25:5) Lofunika kwambiri linali lamulo lonena za mkazi amene anafuna kuthandiza mwamuna wake pandewu. Ngati anagwira ziŵalo zoberekera za mwamuna amene akumenyana ndi mwamuna wake, dzanja lake linayenera kudulidwa; chochititsa chidwi n’chakuti Mulungu sanafune malipiro a diso kulipa diso pa ziwalo zobalira za mkaziyo kapena za mwamuna wake. (Deuteronomo 25:11, 12) Ndithudi lamulo limeneli linawapangitsa kulemekeza ziwalo zoberekera; sizinayenere kuwonongedwa mwachisawawa.b
Tikudziŵa kuti Akristu sakutsatira Chilamulo cha Aisrayeli, chotero lamulo la pa Deuteronomo 25:11, 12 siligwira ntchito pa iwo. Yesu sanalamule kapena kutanthauza kuti ophunzira ake akwatire ndi kukhala ndi ana ambirimbiri, mfundo imene ambiri ailingalirapo posankha kuti kaya azigwiritsa ntchito njira ina yolera kapena ayi. (Mateyu 19:10-12) Mtumwi Paulo analimbikitsadi kuti “akwatiwe amasiye aang’ono [otentha mtima], nabale ana.” (1 Timoteo 5:11-14) Iye sanatchulepo za kutseka kwachikhalire kwa Akristu—kupereka mphamvu zawo za kubereka.
Akristu amachita bwino kupenda mfundo zimenezi zosonyeza kuti Mulungu amalemekeza mphamvu zawo za kubereka. Okwatirana alionse ayenera kudziŵa ngati adzagwiritsa ntchito njira zoyenerera za kulera komanso pamene adzatero. Inde, chosankha chawo chingakhale chofunika kwambiri makamaka ngati pali umboni wonse wakuchipatala wakuti mayi kapena mwana angadzakhale ndi mavuto aakulu akuthupi, mwinanso kufa kumene, ngati mayiyo atakhala ndi pakati. Ena mumkhalidwe umenewo atseketsa monyinyirika mwa njira zomwe zafotokozedwa poyambapo pofuna kuonetsetsa kuti mayi asakhale ndi pathupi pamene pangaike moyo wake pangozi (komanso mayiyo angakhale ali kale ndi ana ena) kapena moyo wa mwana amene angadzabadwe ndi vuto loika moyo pavuto lalikulu.
Koma Akristu amene sali pangozi yaikulu ndi yapadera ngati imeneyi angafunikiredi kugwiritsa ntchito ‘kudziletsa’ ndi kuumba maganizo ndi zochita zawo mogwirizana ndi ulemu wa Mulungu wa mphamvu zoberekera. (1 Timoteo 3:2; Tito 1:8; 2:2, 5-8) Zimenezi zingasonyeze kusamala mwauchikulire mfundo zosonyezedwa m’Malemba. Nangano bwanji zitadziŵika kwa anthu kuti Mkristu wina ananyalanyaza miyezo ya Mulungu mopanda mantha? Kodi ena sangakayikire zakuti iye ndi chitsanzo chabwino, wokhala ndi mbiri yopanga zosankha zogwirizana ndi Baibulo? Ndithudi, mbiri yoipa ngati imeneyo ingakhudze ziyeneretso za mtumiki za maudindo apadera, ngakhale kuti sizingakhale motero ngati munthu anatenga njira imeneyo mosadziŵa.—1 Timoteo 3:7.
[Mawu a M’munsi]
a “Maopaleshoni olumikizanso [njira za ubwamuna], 40 peresenti mwa iwo amayenda bwino, ndipo pali umboni wosonyeza kuti ambiri adzayenda bwino njira zochitira maopaleshoni a ziwalo zing’onozing’ono zikamawongokera. Komabe, kutseketsa mwa amuna kuyenera kutengedwa kuti n’kwachikhalire.” (Encyclopædia Britannica) “Kutseketsa kuyenera kuonedwa kukhala kwachikhalire. Mosasamala kanthu kuti wotseketsayo wamvapo zotani ponena za kutsegulitsa, kulumikizanso njira zomwe zinadulidwa n’kodula, ndipo sungatsimikizire kuti kudzayenda bwino. Kwa akazi amene amakatsegulitsa, pamakhala ngozi yaikulu yakuti mimba n’kukhala m’malo olakwika.”—Contemporary OB/GYN, June 1998.
b Lamulo lina limene lingaoneke kukhala latanthauzo linanena kuti mwamuna aliyense amene ziwalo zake zobalira zinawonongedwa kwambiri asaloŵe mumsonkhano wa Mulungu. (Deuteronomo 23:1) Komabe, Insight on the Scriptures imanena kuti lamulolo “linali kunena za kudzipundula dala ndi zolinga zakhalidwe loipa, monga kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha.” Chotero, lamulo limenelo silinali kunena za kufula kapena njira zolera za panthawiyo. Insight imanenanso kuti: “Motonthoza Yehova ananeneratu za nthaŵi pamene mifule idzalandiridwa ndi iye monga atumiki ake ndi kukhala ndi dzina loposa la ana aamuna ndi aakazi, ngati idzakhala yomvera. Chilamulocho chitathetsedwa ndi Yesu Kristu, anthu onse okhulupirira, mosasamala kanthu za zimene anali kuchita poyamba kapena mmene alili, anatha kukhala ana auzimu a Mulungu. Zinthu zakuthupi zosiyanitsa anthu zinachotsedwapo.—Yesaya 56:4, 5; Yohane 1:12.”