Kusalingana Ufulu—Kodi Mulungu Anafuna Zimenezi?
Yankho lake m’liwu limodzi n’lakuti ayi. Tiyeni tione chifukwa chake.
MULUNGU anafuna kuti anthu onse akhale ndi mwayi wolingana wosangalala ndi moyo ndi chimwemwe. Ponena za kulengedwa kwa munthu, timaŵerenga kuti: “Anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu, alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwaŵa zonse zakukwaŵa pa dziko lapansi.” Atamaliza kulenga zonse za padziko lapansi, “anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”—Genesis 1:26, 31.
Kodi Mulungu anganene m’khalidwe woipa wamakono wosalingana ufulu kuti “zabwino ndithu”? Kutalitali, pakuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Amati iye ‘sasamalira nkhope za anthu’ ndi kuti “ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 10:17; 32:4; yerekezani ndi Yobu 34:19.) Ndipo mtumwi Petro anavomereza kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu, koma m’mitundu yonse wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Machitidwe 10:34, 35.
Popeza kuti Mulungu ali wachikondi, alibe tsankho, n’ngwolungama, komanso wolunjika, akanalenga bwanji anthu osakhala ndi ufulu wachibadwidwe wolingana wokhala ndi chimwemwe? Kulola tsankho pakati pa anthu ndi kuwapatsa ufulu wosalingana kungakhale kosemphaniranatu ndi umunthu wake. Iye anafuna kuti anthu onse “abadwe aufulu komanso ndi ulemu wolingana.” Koma mwachionekere, lero zinthu sizili choncho. Chifukwa?
Muzu wa Kusalingana Ufulu
Pamene Mulungu analenga anthu onse kuti akhale olingana, sizitanthauza kuti anafuna kuti onse akhale olingana pa chilichonse. Iwo angasiyane maluso awo, zokonda zawo, ndiponso maumunthu. Angasiyanenso maudindo kapena mphamvu ya ulamuliro. Mwachitsanzo mwamuna ndi mkazi sali olingana mbali zonse, koma Mulungu analenga mkazi monga “wom’thangatira” mwamuna. (Genesis 2:18) Mwachionekere makolo ndi ana ali osiyana ulamuliro. Komabe mosasamala kanthu za kusiyana kumeneku, onse—amuna, akazi, ndi ana omwe—anafunikira kukhala ndi mipata yolingana yochitira zonse zofunika kuti akhale ndi chimwemwe, ndipo umenewo ndi ufulu wachibadwidwe umene Mulungu anawapatsa. Onse akayenera kukhala ndi ulemu wawo wolingana komanso akayenera kukhala ndi mbiri yofanana pamaso pa Mulungu.
Chimodzimodzinso ana auzimu a Mulungu, amene analengedwa anthu asanalengedwe, anaŵapatsa ntchito ndi maudindo osiyanasiyana. (Genesis 3:24; 16:7-11; Yesaya 6:6; Yuda 9) Komabe, malinga ndi malire a zomwe anawapatsa, onse amasangalala ndi mphatso ya Mulungu ya moyo ndi chimwemwe kumlingo wofanana. Choncho iwo anaonetsa m’njira yodabwitsa kupanda tsankho kwa Mulungu.
N’zachisoni kuti wina mwa zolengedwa zauzimu sanakhutire ndi makonzedwe opanda tsankho a Mulungu. Anafuna zambiri kuposa zomwe Mulungu anam’patsa, ndiye anakhumbitsa malo aulemu, apamwamba kwambiri. Mwa kukulitsa chikhumbo chake choipa chimenechi, anayamba kutsutsana ndi Yehova, amene pokhala Mlengi ali wamkulukulu pa zonse. Pambuyo pake, mwana wauzimu wopanduka ameneyu wa Mulungu anasonkhezera anthu kunena kuti Mulungu anayenera kuwapatsa zinanso zoposa zomwe anawapatsa. (Genesis 3:1-6; yerekezerani ndi Yesaya 14:12-14.) Choncho, makonzedwe a Yehova akuti anthu akhale ndi moyo ndi chimwemwe anakhala ngati asokonezeka. Wopanduka wauzimu ameneyu, amene Chivumbulutso 20:2 chimatcha “Mdyerekezi ndi Satana,” anakhala munthu woipa woyambitsa vuto la kusalingana kwa ufulu wa anthu.
Kodi Zinthu Zidzasinthadi?
Yankho lake m’liwu limodzi n’lakuti inde!
Koma kodi ndani adzabweretsa kusintha kofunika kumeneku? Atsogoleri aumunthu, ena moona mtima ndithu, ayesetsa kuchita zimenezi kwa zaka mazana ambiri. Koma zotsatira zake zakhala zosakhutiritsa, ndipo zachititsa anthu ambiri kunena kuti n’zosathandiza kuganiza kuti vuto la kusalingana kwa ufulu wa anthu lidzatha. Komabe, malingaliro a Mulungu pankhaniyi alembedwa pa Yesaya 55:10, 11 kuti: “Monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhathamiza nthaka ndi kuibalitsa ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbewu kwa wobzala ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”
N’kotonthoza kwambiri kudziŵa kuti Yehova Mulungu wanena yekha poyera kuti adzakwaniritsa chifuno chake choyamba, chopatsa anthu onse mwayi wolingana wokhala ndi moyo komanso chimwemwe! Monga Mulungu wa choonadi, wadzitengera yekha udindo wokwaniritsa zimene walonjeza. Ubwino wake n’ngwoti iye ali wofunitsitsa kuchita zimenezi komanso ali ndi mphamvu yochitira zimenezi. Kodi zimenezi adzachita motani?
Yankho lake ndi Ufumu umene Yesu Kristu anaphunzitsa otsatira ake onse kuupempherera kuti: “Atate wathu wa Kumwamba, . . . Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Inde, Ufumu wa Mulungu ndiwo njira yomwe Yehova adzagwiritsa ntchito ‘kudzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [amene alipo tsopano]. Nudzakhala chikhalire.’—Danieli 2:44.
Mu ulamuliro wa Ufumu wakumwamba, mtundu watsopano wa anthu udzaonekera. Pankhani imeneyi, mtumwi Yohane analemba m’buku lomaliza la Baibulo la Chivumbulutso kuti: “Ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka.” (Chivumbulutso 21:1) Zotsatira zake zonse zoipa za kusoŵa ufulu wolingana—umphaŵi, matenda, umbuli, tsankho, ndi mavuto ena onse osautsa anthu—sizidzakhalako.a
Kwa zaka zoposa zana limodzi, Mboni za Yehova zakhala zikuuza anthu za Ufumu umenewu. (Mateyu 24:14) Mwa kufalitsa mabuku komanso kuthandiza munthu aliyense payekha, izo zachita khama ndithu kuthandiza anthu kupeza chidziŵitso cha chifuno cha Mulungu cholembedwera m’Baibulo. Komabe, ntchito yawo yophunzitsa ya padziko lonse, sinangowapatsa anthu chiyembekezo chokhala ndi ufulu wolingana ndi chimwemwe m’tsogolo, komanso yathandiza ngakhale lero kuletsa mliri wa kusalingana ufulu. Tiyeni tione kuti zatheka motani.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna kudziŵa zambiri za mmene Ufumu wa Mulungu udzabweretsera ufulu wolingana kwa anthu onse, chonde ŵerengani mitu 10 ndi 11 m’buku lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Mulungu anafuna kuti anthu onse akhale ndi mwayi wolingana wokhala ndi moyo ndi chimwemwe