Kuletsa Mliri wa Kusalingana Ufulu
Mlengi posachedwapa adzabweretsa ufulu wolingana umene anthu akulakalaka. Kufikira nthaŵiyo, tingathe pamlingo wina wake kuchitapo kanthu kuletsa mliri wa kusalingana ufulu umene umatikhudza ifeyo ndi mabanja athu. Monga momwe Nelson Mandela, pulezidenti wakale wa South Africa, ananenera, “zimene zimatisiyanitsa ndi anthu ena si zimene timapatsidwa, koma mmene timagwiritsira ntchito zinthu zomwe tili nazo.”
MBIRI imachitira umboni mawu ameneŵa. Pali amuna ndi akazi ochuluka omwe anapatsidwa zochepa pakubadwa kwawo, koma pogwiritsa ntchito bwino zimene anali nazo, anapambana nasiyana ndi mabwenzi awo omwe mwinamwake anali ndi mphatso zapadera. Komabe, anthu ena omwe anali ndi mwayi waukulu chibadwireni anasakaza zomwe anali nazo nalephera kugwiritsa bwino ntchito mphatso zawo zonse.
Gwiritsani Bwino Ntchito Zomwe Muli Nazo!
Mboni za Yehova zimafunitsitsa kuthandiza anthu kupeza chidziŵitso cha zifuno za Mulungu mwa kuphunzira nawo Baibulo. Komanso zimazindikira kuti, kuti anthu apindule mokwanira ndi uthenga wa m’Baibulo, ayenera kukhala odziŵa kuŵerenga ndi kulemba. Pachifukwa chimenechi, Mboni za Yehova zaphunzitsa anthu zikwi makumi ambiri kuŵerenga ndi kulemba, kuphatikizapo anthu 23,000 (chapakati pa ma 1990) m’dziko limodzi lokha ku West Africa. Ponena za utumiki wapadera wothandiza anthu umene Mboni za Yehova zimachita, San Francisco Examiner inati: “Mungawaone ngati nzika zachitsanzo chabwino. Ali ndi khama lopereka msonkho, amasamalira odwala, ndiponso amalimbana ndi kusaphunzira.”
Kuwonjezera apo, chifukwa cha kosi yopitirizabe yophunzitsa kulankhula poyera, Mboni za Yehova zaphunzitsa anthu mazana zikwi zambiri kukhala alankhuli abwino, okhoza kulankhula poyera. Ena a amenewa anali kuvutika kwambiri kulankhula. Mwachitsanzo mwamuna wina ku South Africa analemba kuti: “Chibwibwi linali vuto langa lalikulu moti ndinakhala wamanyazi kulankhula, ndipo nthaŵi zambiri ndinkadalira munthu wina kundilankhulira. . . . Koma pamene ndinaloŵa Sukulu ya Utumiki Wateokalase, anandipatsa kuŵerenga Baibulo kwa anthu ochepa . . . , chibwibwi chinandigwira koopsa moti ndinalephera kumaliza nkhani yangayo panthaŵi yake. Pambuyo pa msonkhano [phungu] anandipatsa uphungu wothandiza. Anandiuza kuti ndidziyesera kuŵerenga mokweza pandekha. Ndinachitadi zimenezi tsiku ndi tsiku, kuŵerenga mokweza Baibulo ndi magazini a Nsanja ya Olonda.” Mwamuna ameneyu anapita patsogolo kwambiri moti pano amalankhula nkhani poyera kwa anthu mazana ngakhale zikwi.
Kusangalala ndi Ufulu Wolingana Pakati pa Abale
Ponena za mkhalidwe wa maphunziro, zaumoyo, zachuma ndi zakakhalidwe ka anthu, Mboni za Yehova n’zosiyana kwambiri wina ndi mnzake. Kusiyana kumeneku kumangosonyeza kupanda ungwiro kwa mikhalidwe ya dziko lomwe tikukhalamo. Koma mosiyana ndi zipembedzo zina, izo zathetsa pakati pawo mbali yaikulu ya tsankho lokhalapo chifukwa cha mtundu, chikhalidwe, ndi chuma.
Zakwaniritsa zimenezi mwa kuyesetsa kutsatira zimene zaphunzira m’Baibulo. Zimayamikira kwambiri mapulinsipulo a Baibulo monga akuti: “Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”—Aroma 12:17, 18; onaninso 1 Timoteo 6:17-19; Yakobo 2:5, 9.
Chifukwa chotsatira mosamalitsa mapulinsipulo a Baibulo amenewa omwe amalimbikitsa umodzi, Mboni za Yehova sizilekerera tsankho lamtundu uliwonse pakati pawo kaya likhale chifukwa chosiyana mtundu, khalidwe, kapena chuma. Mwachitsanzo, zinthu ngati zimenezi samaziganizira pofuna kupatsa munthu udindo wautumiki mumpingo wachikristu. Maudindo monga kuphunzitsa ndi uyang’aniro, zimaperekedwa malinga ndi ziyeneretso zauzimu zimene munthuyo wakwaniritsa basi.—1 Timoteo 3:1-13; Tito 1:5-9.
Kwa anthu amene avutika ndi tsankho la dzikoli, n’kotsitsimula bwanji kukhala ndi ena amene amawaona ngati abale ndi alongo, amene Mlengi wawo amawaona chimodzimodzi! Martina akuvomereza zimenezi. Pamene atate ake ananyanyala banja lawo, iye anakulira m’banja laumphaŵi la kholo limodzi. Kaŵirikaŵiri anzake anali kum’thaŵa, analibe chidaliro, ndipo zinali zovuta kumvana ndi ena. Anakhala wamphwayi pa zilizonse. Komabe, zinthu zinasintha pamene anayamba kuphunzira Baibulo nakhala wa Mboni za Yehova. Iye akuti: “Ndikulimbanabe ndi maganizo anga amphwayi, koma tsopano nditha kulimbana bwino lomwe ndi vutoli. Ulemu wanga wakula ndipo ndimalankhula molimba mtima. Choonadi chandipatsa nzeru yauchikulire. Tsopano ndazindikira kuti Yehova amandikonda ndi kuti moyo uli wosangalatsa kwambiri.”
Monga gulu la Akristu lapadziko lonse, Mboni za Yehova m’mayiko oposa 230 zimasangalala ndi ufulu wolingana ndithu umene uli wapaderadera m’dziko lamakonoli. Kodi pali gulu linanso la chipembedzo limene linganene zofananazi ndi kuzitsimikiza mwa ntchito zawo?
Inde, Mboni za Yehova zimaona mmene zinthu zilili. Izo zimavomereza kuti pokhala mbadwa za dziko lopanda ungwiro, sizingachotseretu vuto la kusalingana kwa ufulu wa anthu monga momwenso ena alepherera atayesa kwa zaka mazana ambiri. Komabe, zikusangalala kuti zachita zambiri ndithu poyesa kuletsa mliri wakupha umenewu. Ndipo ndi chikhulupiriro cholimba pa lonjezo la Mulungu, zikuyembekeza mwachidwi dziko latsopano lolungama limene kusalingana ufulu kudzakhala zinthu zakale kosatha.
Inde, anthu onse omvera posachedwapa adzapatsidwanso “ulemu komanso ufulu” wawo wolingana umene Mlengi wawo anafuna kuti asangalale nawo pachiyambi. Lingaliro limeneli sikukoma kwake! Ndiponso panthaŵiyo zidzakhala zenizeni!
[Chithunzi patsamba 7]
Mboni za Yehova zimalimbana ndi umbuli mwa kuphunzitsa anthu zikwi makumi ambiri kulemba ndi kuŵerenga
[Chithunzi patsamba 8]
Choonadi cha Baibulo chimathandiza kuchotsa tsankho la utundu, chikhalidwe ndi zachuma