Mliri Wamakono wa Kusalingana Ufulu
“Tikhulupirira kuti mfundo zoona zimenezi n’zodziŵika, kuti anthu onse analengedwa olingana, kuti Mlengi wawo anawapatsa Maufulu Achibadwidwe osatheka kuwalanda, ena a iwo ndiwo Moyo, Ufulu Wosaponderezedwa, ndi wokhala ndi Chimwemwe.”—Chikalata cha ufulu wodzilamulira cha Declaration of Independence, chokhazikitsidwa ndi United States mu 1776.
“Anthu onse amabadwa aufulu komanso ndi ufulu wolingana.”—Chikalata cha ufulu wachibadwidwe wa munthu ndi nzika cha Declaration of the Rights of Man and of the Citizen, chokhazikitsidwa ndi Nyumba ya Malamulo ya ku France mu 1789.
“Anthu onse amabadwa aufulu komanso ndi ulemu ndi ufulu wolingana.”—Chikalata cha mfundo za ufulu wachibadwidwe cha Universal Declaration of Human Rights, chokhazikitsidwa ndi United Nations General Assembly mu 1948.
SITINGAKAYIKE za zimenezi. Anthu kulikonse amafuna ufulu wolingana. Komabe chomvetsa chisoni n’chakuti, kubwerezedwabwerezedwa kwa nkhaniyi yokhudzana ndi kulingana kwa ufulu wa anthu kwasonyeza kuti mpaka pano mtundu wa anthu walephera kupeza ufuluwo.
Kodi pali aliyense amene anganene moona mtima kuti kumapeto kwa zaka za zana la 20 lino zinthu zasintha mwabwinopo? Kodi nzika zonse za ku United States ndi France, kapenanso za lililonse la mayiko 185 omwe ndi mamembala a United Nations, zimasangalaladi ndi ufulu wolingana umene amati zinabadwa nawo?
Ngakhale mfundo yakuti anthu onse ali ndi ufulu wolingana ingakhale “yodziŵika,” maufulu achibadwidwe monga wokhala ndi “Moyo, Wosaponderezedwa ndi wopeza Chimwemwe” sali olingana konse kwa anthu onse. Mwachitsanzo, pali kufanana kotani pa ufulu wokhala ndi moyo kwa khanda la ku Afirika losamaliridwa ndi dokotala mmodzi amene amasamalira anthu enanso 2,569, poyerekeza ndi khanda la ku Ulaya losamaliridwa ndi dokotala amene amasamalira anthu ena 289 okha? Kapena ndi kulingana kotani kwa ufulu wosaponderezedwa ndi wopeza chimwemwe komwe kulipo kwa ana a ku India amene mwa anyamata atatu alionse mmodzi amakula wosaphunzira ndiponso mwa asungwana atatu alionse aŵiri amakula osaphunzira, poyerekeza ndi m’mayiko ngati Japan, Germany ndi Great Britain komwe mwana aliyense amalandira maphunziro?
Kodi anthu a m’mayiko a ku Central America omwe malipiro awo ndi $1,380 angasangalale ndi “ulemu ndi ufulu wachibadwidwe” m’moyo wofanana ndi anzawo a ku France, amene malipiro awo ndi $24,990? Nanga pali kufanana kotani kwa ufulu pakati pa khanda lachikazi longobadwa kumene ku Afirika loyembekeza kukhala ndi moyo zaka 56 zokha poyerekeza ndi khanda lachikazi la ku North America limene limayembekeza kukhala ndi moyo zaka 79?
Kusalingana kwa ufulu kuli ndi mbali zambiri, zonsezo n’zoipa zokhazokha. Kusalingana pa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wa munthu komanso pa mwayi wa zachipatala, kudzanso maphunziro zili zina mwa izo. Nthaŵi zina kusiyana pa ndale, fuko kapena chipembedzo zathandiza kwambiri kulanda anthu ulemu wawo ndi ufulu wawo wosaponderezedwa. Mosasamala kanthu za zimene zikukambidwa ponena za kulingana kwa ufulu, tikukhala m’dziko la tsankho. Mofanana ndi mliri—“matenda aakulu ofala,” malinga ndi tanthauzo la liwulo—vuto loona ngati ufulu wa anthu sulingana limakhudza anthu amtundu uliwonse. Mavuto omwe umadzetsa monga ngati umphawi, matenda, umbuli, ulova, ndiponso tsankho zimapweteka kwambiri.
“Anthu onse analengedwa olingana.” Ati kukoma kwake lingaliro limeneli! Koma n’zachisoni bwanji kuti zinthu sizili chomwechi!
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
UN PHOTO 152113/SHELLEY ROTNER