Kutsatira Chitsogozo cha Yehova Mosangalala
YOSIMBIDWA NDI ULYSSES V. GLASS
Chinali chochitika chapadera kwambiri. Kalasi la omaliza maphunziro linali ndi ophunzira 127 okha, koma odzapenyerera chochitikacho anali odzazidwa ndi chisangalalo okwana 126,387, ochokera ku mayiko osiyanasiyana. Unali mwambo womaliza maphunziro a kalasi la 21 la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower ya Baibulo, umene unachitikira ku Yankee Stadium mumzinda wa New York pa July 19, 1953. N’chifukwa chiyani chimenecho chinali chochitika chapadera m’moyo wanga? Ndiloleni ndifotokoze chiyambi chake.
INDINABADWIRA ku Vincennes, Indiana, United States, pa February 17, 1912, pafupifupi zaka ziŵiri Ufumu wa Umesiya usanabadwe, monga momwe aufotokozera pa Chivumbulutso 12:1-5. Chaka chambuyomo, makolo anga anali atayamba kuphunzira Baibulo limodzi ndi mabuku otchedwa Studies in the Scriptures. M’maŵa ulionse Lamlungu, abambo athu ankatiŵerengera mawu ochokera m’limodzi la mabuku ameneŵa ndipo pambuyo pake tinali kukambirana.
Mayi ankagwiritsa ntchito zomwe anali kuphunzira kuthandiza ana awo kukula ndi maganizo abwino. Anali munthu wabwino kwabasi—wachikondi, wofunitsitsa kuthandiza. Ngakhale kuti m’banja lathu munali ana anayi, chikondi cha amayi athu chinali kusefukira kwa ana am’mabanja oyandikana nawo. Ankakonda kumacheza nafe. Ankasangalalano kumatisimbira nkhani za m’Baibulo, ndi kumaimba nafe nyimbo.
Analinso kuitanira kunyumba anthu osiyanasiyana amene anali kuchita utumiki wanthaŵi zonse. Tinkakhala nawo kwa tsiku limodzi kapena aŵiri, ndipo kaŵirikaŵiri anali kuchititsa misonkhano ndi kukamba nkhani m’nyumba mwathu. Kwenikweni tinkakonda kwambiri amene anali kugwiritsa ntchito mafanizo ndi kutisimbira nkhani. Pachochitika china mu 1919, patangopita pafupifupi chaka chimodzi nkhondo yoyamba yadziko lonse itatha, mbale wina amene anadzatichezera analunjikitsa ndemanga zakezo kwenikweni kwa ife ana. Anakamba za kudzipereka—kumene lerolino timatcha molondola kwambiri kuti kudzipatulira—ndipo anatithandiza kuzindikira mmene kumakhudzira miyoyo yathu. Pambuyo pake usiku womwewo nditapita kukagona, ndinapemphera kwa atate wanga wakumwamba kumuuza kuti ndikufunitsitsa kumutumikira nthaŵi zonse.
Komabe, chaka cha 1922 chitadutsa zokhumba zina zinkafuna kupondereza chosankha chimenechi. Sitinali okhazikika malo amodzi ndipo sitinali kugwirizana ndi mpingo uliwonse wa anthu a Yehova. Atate anali kutali kumene ankagwira ntchito yawo yapanjanje. Phunziro lathu la Baibulo linali losakhazikika. Ndinapanga makosi a sukulu ndicholinga chofuna kudzakhala wa zamalonda, ndipo ndinkakonzekera zopita ku yunivesite yapamwamba kwambiri.
Kusintha Chifuno m’Moyo Wanga
M’katikati mwa ma 1930 dziko linayang’anizananso ndi nkhondo ina yadziko lonse lapansi. Tinali kukhala mu Cleveland, Ohio, pamene wa Mboni za Yehova anafika pakhomo pathu. Tinayamba kuganiza mosamalitsa zimene ankatiphunzitsa tikali ana. Mkulu wanga Russell, ndiye anazilingalira mwamphamvu kwambiri, ndipo anali woyamba kubatizidwa. Ndinali wozengereza, komabe pa February 3, 1936 nanenso ndinabatizidwa. Kuyamikira kwanga pa zomwe kudzipatulira kwa Yehova kumatanthauza kunayamba kukula, ndipo ndinkaphunzira kutsatira chitsogozo cha Yehova. Chaka chomwecho, achemwali anga aŵiri, Kathryn ndi Gertrude nawonso anabatizidwa. Tonse tinayamba utumiki wanthaŵi zonse waupainiya.
Komabe ichi sichinatanthauze kuti sitinali kuganiza za zinthu zina. Mtima wanga unagunda pamene mlamu wanga ankandiuza za mtsikana wokongola kwambiri wotchedwa Ann yemwe “anali wachangu m’zinthu zauzimu” chimvereni za choonadi, ndipo anati azisonkhana nafe kunyumba kwathu. Panthaŵiyo Ann anali kugwira ntchito ngati mlembi mu ofesi ya boma yoona zamalamulo, ndipo m’kati mwa chaka chomwecho anabatizidwa. Panthaŵiyo ndinalibe maganizo ofuna kukwatira, koma zinali zoonekeratu kuti Ann anadzipereka kwathunthu pa choonadi. Anafuna kum’tumikira Yehova nthaŵi zonse. Sanali munthu wofunsa kuti, “Kodi ndikwanitsa?” Kwake kunali kufunsa kuti “Ndingatani kuti ndichite bwino koposa?” Ndipo anali wofunitsitsa kutsatira zomwe wauzidwazo. Ndinaona maganizo ake abwinowo. Pambali pa zimenezo, anali chiphadzuŵa, ndipo adakaŵalabe kwambiri. Ndinamanga naye banja ndipo ndi bwenzi lomwe ndikutumikira nalo limodzi muutumiki waupainiya
Maphunziro Opindulitsa Aupainiya
Monga apainiya, tinaphunzira chinsinsi cha momwe tingakhalire okhutira ndi zochepa kapena zochuluka zomwe tili nazo. (Afilipi 4:11-13) Tsiku lina pamene kunali kuda, tinalibe chakudya. Tinali ndi ndalama zokwana masenti asanu okha basi. Titapita m’butchale, tinapempha wogulitsayo ngati akanatha kutigulitsa nyama ya ndalama zokwana masenti asanu. Anatiyang’ana ndipo kenako anadula nthuli zinayi. Ndikukhulupirira kuti mtengo wa nyamayo unaposa masenti asanu, ndipo tinadyadi bwino.
Sichinali chachilendo kwa ife kukumana ndi anthu otsutsa ntchito yathu ya utumiki. M’tauni ina yapafupi ndi Syracuse, mu New York tinali kugaŵira mahandibilu mumsewu titadzikoloŵeka zikwangwani zokopa anthu ku msonkhano wapadera. Panafika amuna aŵiri omwe mwadzidzidzi anandigwira mwamphamvu. Mmodzi wa iwo anali wapolisi, yemwe panthaŵiyo anali asanavale yunifolomu, ndipo nditam’funsa kuti andionetse chiphaso chake, anakana. Nthaŵi yomweyo Grant Suiter wochokera ku Beteli ya Brooklyn anafika pafupi ndi kunena kuti tipite kupolisi kuti tikakambirane nkhaniyo. Pambuyo pake anaimbira telefoni ku ofesi ya Sosaite ku Brooklyn, ndipo tonse aŵiri anatilangiza kuti tiyenera kupitanso m’misewu tsiku lomwelo titatenganso mahandibilu ndi kudzikoloŵeka zikwangwani zija kuti pakhale umboni kaamba ka m’tsogolo. Mwachionekere, tinamangidwa. Komabe, apolisiwo anatimasula pamene tinawauza kuti tiwasumira chifukwa chotimanga molakwira lamulo.
Tsiku lotsatira gulu la achinyamata achiwawa linafika pa malo athu osonkhanira litasonkhezeredwa ndi wansembe, ndipo apolisi sanabwerepo. Anyamata achiwawa amenewo anali kumenyetsa zipangizo zoseŵerera baseball pansi poyalidwa matabwa, ndikukankhira pansi omvetsera kuchokera pamabenchi, ndi kukwera papulatifomu, pomwepo ananyamula m’mwamba mbendera ya America akumatilamula mofuula kuti, “Perekani sawatcha ku mbendera! Perekani sawatcha ku mbendera!” Kenaka anayamba kuimba nyimbo yotchedwa “Beer Berrel Polka.” Anasokonezeratu msonkhano wathu. Tinadzionera tokha zimene Yesu ananeneratu kuti: “Koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.”—Yohane 15:19.
Nkhani yapoyera inali yojambulidwa imene inaperekedwa ndi J. F. Rutherford, yemwe panthaŵiyo anali pulezidenti wa Watch Tower Society. Ine ndi Ann tinakhala m’tauni yomweyo kwa masiku ochepa kuti tilankhule ndi anthu, ndikuŵapatsa mpata womvera nkhani imeneyo m’nyumba zawo. Angapo anavomera.
Kudzipereka Kukatumikira ku Mayiko Ena
M’kupita kwa nthaŵi, mwayi watsopano wa utumiki unatseguka. Mbale wanga Russell, limodzi ndi mkazi wake Dorothy, anaŵaitana ku Sukulu ya Gileadi mu 1943, ndipo pambuyo pake anaŵatumiza monga amishonale ku Cuba. Mchemwali wanga Kathryn n’kuti ali m’kalasi lachinayi panthaŵiyi. Nayenso anamutumiza ku Cuba. Pambuyo pake anadzamutumiza ku Dominican Republic, ndiyeno ku Puerto Rico. Bwanji ponena za Ann ndi ine?
Mmene tinamva za Sukulu ya Gileadi ndi kuti Sosaite ikufuna kutumiza amishonale ambiri ku mayiko ena, tinali ofunitsitsa zedi kudzipereka pa utumiki umenewu. Poyamba tinkaganiza zopita patokha, mwina ku Mexico. Kenako tinalingalira kuti ndibwino kuyembekezera kuti Sosaite idzatitumize pambuyo pa maphunziro ku Sukulu ya Gileadi. Tinazindikira kuti kameneka kanali kakonzedwe kamene Yehova anali kugwiritsa ntchito.
Anatiitanira ku kalasi lachinayi la Sukulu ya Gileadi. Koma patangotsala pang’ono kuti kalasilo liyambe, N. H. Knorr, yemwe anali pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, anazindikira kuti Ann sakanatha kukatumikira ku dziko lina, chifukwa cha kulumala kochititsidwa ndi poliyo imene anadwala akali mwana. Anandifotokozera za nkhaniyi ndipo ndinalingalira kuti sichikanakhaladi chanzeru kuti atitumize kukatumikira kudziko lina.
Patapita zaka pafupifupi ziŵiri, pamene ndinali kugwira ntchito yokonzekera misonkhano, Mbale Knorr anakambirananso nane nandifunsa ngati tidakali ndi chidwi chofuna kupita kusukulu ya Gileadi. Anandiuza kuti sadzatitumiza ku dziko lina; anatikonzera kanthu kena. Choncho pamene kalasi lachisanu ndi chinayi linali kulembetsa mayina awo pa February 26, 1947, ife anatiika m’gulu la ophunzira limeneli.
Masiku amene tinali ku Gileadi n’ngosaiŵalikadi. Maphunziro ake anali olemeretsa mwauzimu. Tinapanga mabwenzi amoyo wathu wonse. Ndipo kutenga mbali kwanga m’sukulu kunapyola pamenepo.
Pakati pa Washington ndi Gileadi
Sukulu ya Gileadi inali yatsopano. Boma la United States silinkadziŵa bwino cholinga chenicheni cha sukuluyi, chotero pamafunsidwa mafunso ambiri. Panafunika woimira Sosaite mu Washington, D.C. N’kumene anatitumiza patadutsa miyezi yochepa kuchokera pamene tinamaliza maphunziro athu ku Gileadi. Ndinali kukathandiza kupeza maviza a oitanidwa ku Gileadi oloŵera m’dzikomo pochokera ku mayiko ena, ndi kupeza zikalata zotumizira amishonale ku mayiko ena. Akuluakulu ena am’maofesi anali amaganizo abwino ndi othandiza. Ena anali otsutsa Mboni kwambiri. Enanso amene anali ndi malingaliro andale anatitsutsa mwamphamvu akumaganiza kuti timagwirizana ndi magulu omwe amaŵalingalira kukhala osafunikira.
Mwamuna wina yemwe ndinam’peza mu ofesi yake anatitsutsa mwamphamvu chifukwa chakuti sitiperekera sawatcha ku mbendera kapena kupita kunkhondo. Atalalata kwakanthaŵi ndinati: “Ndikufuna kuti mudziŵe ndipo mukudziŵa kuti Mboni za Yehova sizimenya nawo nkhondo kulikonse padziko lapansi. Sitimadziloŵetsa m’machitachita adziko. Sitimenya nawo nkhondo kapena kuloŵa m’ndale. Sititenga mbali iliyonse m’zandale. Tinathetsa kale mavuto amene inu mukulimbana nawo; muli mgwirizano m’gulu lathuli. . . Tsono mukufuna kuti tichitenji? Kodi mukufuna tibwerere ku njira zanu zakalezo, ndi kusiya zathuzi?” Sananenepo kalikonse pambuyo pake.
Tinapatula masiku aŵiri mlungu uliwonse opita ku maofesi aboma. Komanso tinali kutumikira monga apainiya apadera. M’buyomu chimenecho chinatanthauza kuti panafunikira maola 175 a mu utumiki wakumunda (pambuyo pake anaŵasintha kukhala maola 140), choncho nthaŵi zambiri timakhala mu utumiki kufikira madzulo. Tinali kukhala ndi nthaŵi yabwino kwambiri. Tinayambitsa maphunziro a Baibulo ambiri m’mabanja osiyanasiyana, ndipo iwo anapita patsogolo bwino lomwe. Ngakhale kuti Ann ndi ine tinagwirizana kuti tisakhale ndi ana, koma mwauzimu tinali osati ndi ana okha, komanso zidzukulu ndi zidzukulutuvi. Timasangalala nawo kwabasi!
Kumapeto kwa chaka cha 1948, anandipatsa ntchito ina. Mbale Knorr anandifotokozera kuti Mbale Schroeder, yemwe anali wosunga kaundula komanso m’modzi wa alangizi pa Sukulu ya Gileadi, azikhala wotanganidwa ndi ntchito zina zofunika kwambiri, motero ndinapemphedwa kuti nthaŵi zina ndizithandiza kuphunzitsa makalasi a Gileadi. Ndili ndi mantha, ndinabwereranso ku Gileadi ku South Lansing mu New York, limodzi ndi Ann pa December 18. Poyamba tinkakhala ku Gileadi kwa milungu yochepa kenako, n’kubwereranso ku Washington. Pang’ono ndi pang’ono tinayamba kuthera nthaŵi yambiri ku Gileadi poyerekeza ndi ku Washington.
Inali nthaŵi imeneyi monga ndafotokozera poyamba paja kuti mwambo wa omaliza maphunziro a kalasi la 21 la Gileadi unachitikira ku Yankee Stadium mu New York. Choncho monga mmodzi wa alangizi ndinali wamwayi kutengapo mbali m’kakonzedwe ka mwambo wa omaliza maphunziro umenewu.
Kutumikira ku Likulu la Dziko Lonse Lapansi
Pa February 12,1955, utumiki wina unayambika. Tinakhala a m’banja la Beteli pa likulu la padziko lonse la gulu looneka la Yehova. Zimenezo zinaphatikizaponji? Kwenikweni kukhala ofunitsitsa kuchita ntchito iliyonse yoperekedwa kwa ife, kutenga nawo mbali m’ntchito yofunika kugwira mothandizana ndi ena. Ngakhale kuti tinazichita zimenezo m’buyomu, koma tsopano tikakhala m’banja lalikulu kwambiri—banja la Beteli la kulikulu. Tinalandira ntchito yatsopano imeneyi mwachisangalalo monga umboni wakuti tikutsogozedwa ndi Yehova.
Mbali yaikulu ya ntchito yanga inali kukhudzana ndi nkhani zofalitsidwa. Chifukwa chakuti olemba manyuzipepala ena ankafuna nkhani zokopa anthu, ndiponso anali kutenga nkhani zawo m’zofalitsa zatsankho, manyuzipepala awo ankalemba zinthu zachipongwe ponena za Mboni za Yehova. Tinalingalira zothetsa mchitidwe umenewo.
Mbale Knorr anafuna kuti tonse tikhale otanganidwa nthaŵi zonse, choncho anatipatsanso ntchito zina. Ina mwa ntchito imene ndinkagwira imadalira kwambiri pa luso langa monga wa zamalonda. Zina zinali zokhudza siteshoni ya wailesi ya Sosaite, yotchedwa WBBR. Kunali ntchito yokhudzana ndi zithunzi zakanema zojambulidwa ndi Sosaite. Mbiri yateokalase inali mbali ya maphunziro ku Gileadi, koma tsopano, ntchito zosiyanasiyana zinayamba ndi cholinga chodziŵitsa anthu a Yehova komanso anthu ena onse zochuluka zokhudza tsatanetsatane wa mbiri ya gulu lateokalase lamakonoli. Mbali ina ya maphunziro a Gileadi inaphatikizapo luso la kulankhula ndi ntchito imene ikufunikira kuti abale m’mipingo adziŵe maziko enieni a kulankhula mwaluso. Choncho panali zambiri zoti tichite.
Kukhazikika ku Gileadi
Cholinga chofuna kuphunzitsa oyang’anira oyendayenda ndi oyang’anira nthambi m’tsogolo, chinaŵachititsa kusamutsira Sukulu ya Gileadi ku Brooklyn kumene kuli maofesi akuluakulu a Watch Tower Society mu 1961. Kachiŵirinso ndinabwerera m’kalasi—tsopano osatinso ngati mlangizi wapadera ayi koma ngati membala wokhazikika wa bungwe la aphunzitsi. Linali dalitso lalikulu kwabasi! Ndine wokhutira kuti Sukulu ya Gileadi ndi mphatso yochokera kwa Yehova, mphatso yomwe gulu lake lonse looneka lapindula nayo.
M’makalasi a Gileadi a ku Brooklyn, ophunzira anali ndi mwayi woposa ophunzira a m’mbuyomo. Kunali aphunzitsi ambiri achilendo ndipo anayanjana kwambiri ndi Bungwe Lolamulira, komanso panali mayanjano athithithi ndi banja la Beteli la kulikulu. Kunalinso kotheka kwa iwo kuphunzira ntchito za mu ofesi, ntchito za m’nyumba ya Beteli ndi ntchito zina za m’mafakitale.
M’kupita kwa zaka, chiŵerengero cha ophunzira chakhala chikusintha monga mmene zakhalira ndi chiŵerengero cha alangizi. Sukulu imeneyinso yakhala ikusamutsidwira malo osiyanasiyana. Ndipo tsopano ili pamalo okongola kwambiri ku Patterson, mu New York.
Kugwira Ntchito Limodzi ndi Ophunzira
Chakhala chosangalatsa zedi kuphunzitsa makalasi amenewa! Ndaona achinyamata amene alibe chidwi chofuna zinthu za m’dongosolo lakale lazinthu lino. Anasiya mabanja awo, mabwenzi awo, nyumba zawo, ndi anthu amene amatha kulankhula nawo chinenero chimodzi. Nyengo, chakudya—ndi zina zonse zimakhala zachilendo kwa iwo. Komanso samadziŵa ngakhale dziko limene akupitako, iwo cholinga chawo ndicho kukhala amishonale basi. Simufunikira kuchita kusonkhezera anthu amtundu umenewu.
Pamene ndiloŵa m’chipinda chophunziriramo, chinali cholinga changa nthaŵi zonse kuŵapangitsa ophunzirawo kukhala omasuka. Palibe angaphunzire bwino ngati ali womangika ndi wodandaula. N’zoona kuti ndinali mlangizi, koma ndinadziŵanso mmene kukhala wophunzira kuliri. Ndinakhalapo wophunzira nthaŵi ina. Ngakhale kuti anali akhama pa maphunziro awo, ndipo ankaphunzira zochuluka, ndinafunanso kuti asangalale ndi nthaŵi yakukhala kwawo pa Gileadi.
Ndinadziŵa kuti pamene akupita ku utumiki wawo, kukakhala zina zimene akafune kuti apambane. Anafunikira chikhulupiriro champhamvu. Anafunikira kukhala odzichepetsa—inde, kudzichepetsa kwambiri. Anafunikira kuphunzira mmene angakhalire ndi ena, kuzoloŵerana ndi mikhalidwe yovuta, kukhululukirana mwaufulu. Anafunikiranso kupitiriza kukulitsa zipatso za mzimu. Anafunikiranso kumakonda anthu ndi ntchito imene apatsidwa kukaigwira. Zimenezo ndi zomwe ndakhala ndikuwatsimikizira ophunzira mobwerezabwereza pamene anali pa Gileadi.
Sindikudziŵa kuti ndiangati omwe ndinawaphunzitsa. Komabe ndimadziŵa kuti ndimawakonda kwambiri. Ndinazoloŵerana nawo kwambiri pambuyo pokhala nawo m’kalasi kwa miyezi isanu. Ndipo pamene ndinaŵaona akupita pa pulatifomu kukalandira madipuloma awo pa tsiku lomaliza maphunziro awo, ndinadziŵa kuti amalizadi maphunziro awo mwachipambano ndipo posakhalitsa adzachoka. Zimakhala ngati ena am’banja langa ndalekana nawo. N’kulekeranji kukonda anthu onga awa, anthu ofunitsitsa kudzipereka kotheratu ndi kugwira ntchito yomwe achinyamata amenewa aziigwira?
Zaka zambiri pambuyo pake, akamabwera kudzacheza, ndimamva akukamba za chimwemwe chomwe alinacho mu utumiki wawo, ndipo ndikudziŵa kuti akupitirizabe kutumikira ndi kutsatira zimene anaphunzira. Mukudziŵa mmene ndimadzimvera? Kunena zoona, n’zokondweretsa zedi.
Kuyang’ana M’tsogolo
Maso anga sathanso kuona bwino tsopano, ndipo izi zandidzetsera mavuto ambiri m’moyo wanga. Sindilinso wokhoza kuphunzitsa makalasi a Gileadi. Poyamba, ndinachiona kukhala chinthu chovuta kuzoloŵerana ndi mkhalidwewu, komabe m’moyo wanga wonse ndaphunzira kupirira mikhalidwe ngati imeneyi. Kaŵirikaŵiri ndimalingalira za mtumwi Paulo ndi “munga m’thupi” mwake. Katatu konse, Paulo anapempherera thandizo ku mavuto amenewo, koma Ambuye anamuuza kuti: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m’ufoko.” (2 Akorinto 12:7-10) Paulo anapitirizabe kukhala nawo munga uja. Ngati iye anapirira, inenso ndikufuna ndiyese. Ngakhale kuti sindingathenso kuphunzitsa, ndine wosangalala kuti ndimathabe kuona ophunzira akubwera ndi kupita tsiku ndi tsiku. Nthaŵi zina ndimatha kulankhulana nawo, ndipo chimabweretsa chimwemwe m’mtima mwanga ndikaganizira za mzimu wabwino umene amasonyeza.
Tikuyembekezera m’tsogolo mwa chimwemwe. Maziko ake akuyalidwa tsopano. Gileadi yachita mbali yofunika kwambiri pa maziko ameneŵa. Pambuyo pa chisautso chachikulu, pamene mabuku ofotokozedwa pa Chivumbulutso 20:12 adzatsegulidwa, padzakhala zaka chikwi za kuphunzira mozama njira za Yehova. (Yesaya 11:9) Komabe amenewo sadzakhala mapeto. Chidzangokhala chiyambi chabe. Ku nthaŵi yomka muyaya, kudzakhala zochuluka zoti tiphunzire ponena za Yehova komanso zambiri zochita pamene zifuno zake zikavumbulidwa. Ndili ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake, ndipo ndikufunitsitsa kudzapezekapo ndi kulandira nawo choloŵa cha kulola kwathu kutsogozedwa ndi Yehova
[Chithunzi patsamba 26]
Kumaliza maphunziro a Gileadi ku New York, pa Stadium ya Yankee mu 1953
[Chithunzi patsamba 26]
Gertrude, Ine, Kathryn, ndi Russell
[Chithunzi patsamba 26]
Kugwira ntchito limodzi ndi N. H. Knorr (kumanzere) ndi M. G. Henschel kulinganiza msonkhano
[Chithunzi patsamba 26]
M’nyumba ya wailesi ya WBBR
[Chithunzi patsamba 29]
M’kalasi la Gileadi
[Chithunzi patsamba 31]
Ndi Ann, osati kale kwambiri