Sangalalani ndi “Moyo Weniweni”
YEHOVA MULUNGU anaika mwa munthu maganizo ofuna kukhala ndi moyo kwamuyaya. (Mlaliki 3:11) N’chifukwa chake anthu amadzimva kukhala opanda mphamvu iliyonse pa imfa koma, panthaŵi imodzimodziyo, chikhumbo chosagonja chofuna kukhalabe amoyo chimabuka mwa iwo.
Baibulo Loyera, Mawu ouziridwa a Mulungu, amatipatsa ife chiyembekezo. (2 Timoteo 3:16) Yehova, yemwe ndi gwero lenileni la chikondi, sakanapanga munthu, ndi kum’patsa lingaliro la umuyaya m’maganizo mwake, kenako n’kum’lamula kuti azingokhala zaka zochepa zokha. Umunthu wa Mulungu ukutsutsana ndi lingaliro lakuti anatilenga kuti tizunzike ndi njira ya moyo wathu. Sitinalengedwe ngati “zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuwonongedwa.”—2 Petro 2:12.
Polenga Adamu ndi Hava, ndi kuwapatsa lingaliro lachibadwa lofuna kukhala ndi moyo kosatha, Yehova Mulungu anapanga kanthu kena ‘kabwino kwambiri’; iye anaŵapanga ndi kuthekera konse kokhala ndi moyo wosatha. (Genesis 1:31) Koma n’zachisoni kuti banja loyambali linagwiritsa ntchito ufulu wodzisankhira molakwa, posamvera chiletso chachindunji chochokera kwa Mlengi, ndipo anataya ungwiro wawo wapoyamba. Zotsatira zake, iwo anafa, napatsiranso mbadwa zawo zonse kupanda ungwiro ndi imfa.—Genesis 2:17; 3:1-24; Aroma 5:12.
Baibulo limavumbula poyera cholinga cha moyo ndi chimene imfa imatanthauza. Ilo limati pa imfa “palibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa ngakhale nzeru” ndi kutinso akufa “sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5, 10) Mwa mawu ena, akufa ndi akufa basi. Chiphunzitso cha kusafa kwa mzimu sichichokera m’Baibulo, choncho palibe chinsinsi chilichonse chofuna kuchivumbula ponena za mkhalidwe wa akufa.—Genesis 3:19; Salmo 146:4; Mlaliki 3:19, 20; Ezekieli 18:4.a
Mulungu anali ndi cholinga; sanalilenga dziko “mwachabe.” Iye analiumba “akhalemo anthu” angwiro, mumkhalidwe wa paradaiso ndipo Mulungu sanasinthe chifuno chake chimenechi. (Yesaya 45:18; Malaki 3:6) Pofuna kukwaniritsa chifuno chake chimenecho, anatumiza Mwana wake padziko lapansi. Nayenso Yesu Kristu, mwakukhalabe wokhulupirika kufikira imfa, anapereka njira yowombolera mtundu wa anthu ku uchimo ndi imfa. Ndi iko komwe, Yesu iye mwiniyo anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Kalero, Mulungu analonjeza kuti adzalenga “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” (Yesaya 65:17; 2 Petro 3:13) Zimenezo zikuphatikizamo kusankha kagulu ka Akristu okhulupirika opita kumwamba. Limodzi ndi Yesu Kristu, apanga maziko aboma. Baibulo limafotokoza bomalo kukhala “Ufumu wa kumwamba,” kapena kuti “Ufumu wa Mulungu,” womwe udzakonzanso “zinthu zonse padziko lapansi.” (Mateyu 4:17; 12:28; Aefeso 1:10; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3) Atatha kuwononga zonyansa zonse zili m’dziko ndi kulikonzanso, Mulungu adzakhazikitsa mtundu watsopano wa anthu olungama, kapena kuti “dziko latsopano.” Ichi chidzaphatikizapo anthu omwe Mulungu adzawateteza pamene adzawononga dongosolo la zinthu loipali posachedwapa. (Mateyu 24:3, 7-14, 21; Chivumbulutso 7:9, 13, 14) Adzakhalira limodzi ndi omwe adzaukitsidwire kumoyo kudzera m’lonjezo la kuukitsa akufa.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
“Moyo Weniweni” Panthaŵiyo
Potsimikizira za malongosoledwe okondweretsa ameneŵa onena za moyo wosatha m’dziko latsopano la Paradaiso, Mulungu anati: “Taonani! Ndichita zonse zikhale zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5) N’kosatheka kuti malingaliro a munthu afike pomvetsetsa za ntchito zodabwitsa zimene Mulungu adzachitira mtundu wa anthu. Mulungu adzalenga paradaiso padziko lonse lapansi, wonga uja anali mu Edeni. (Luke 23:43) Monga mu Edeni, maonekedwe a zinthu okongola, kuimba kosangalatsa, ndi zakudya zokoma zidzakhala zochuluka. Umphaŵi ndi kusoŵa chakudya sizidzakhalako, chifukwa ponena za nthaŵiyo Baibulo limati: “Zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4; Salmo 72:16) Palibe yemwe adzati, “Ine ndidwala,” pakuti matenda adzathetsedwa. (Yesaya 33:24) Inde, zoŵaŵitsa zonse zidzatha, kuphatikizanso mdani, wamkulu wa mtundu wa anthu, Imfa. (1 Akorinto 15:26) M’masomphenya ozizwitsa “adziko latsopano,” gulu latsopano la anthu pansi pa ulamuliro wa Kristu, mtumwi Yohane anamva mawu aakulu akunena kuti: “[Mulungu] . . . adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.” N’chiyaninso chingadzetse chitonthozo chachikulu chomwechi ndi chimwemwe chochuluka, kuposa malonjezo ochokera kwa Mulungu ameneŵa?
Polongosola za moyo wam’tsogolo, Baibulo limafotokoza motsimikiza mikhalidwe yomwe idzakhutiritsa zokhumba za munthu, zamakhalidwe komanso zauzimu. Zabwino zonse zimene mtundu wa anthu wayesayesa kuti uzipeze koma mosaphula kanthu kufikira tsopano, zidzapezeka m’nthaŵiyo. (Mateyu 6:10) Zina mwa zimenezi ndi chilakolako cha chilungamo, chimene mpaka pano chikusoŵa chifukwa chakuti munthu wakhala akuzunzidwa ndi anthu ankhanza omwe apweteka anzawo ochepa mphamvu, poŵalamulira mosayenera. (Mlaliki 8:9) Wamasalmo analosera momwe zinthu zidzakhalira mu ulamuliro wa Kristu pamene analemba kuti: “Masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka.”—Salmo 72:7.
Ufulu wachibadwidwe n’chokhumba china chimene ambiri achivutikira. Pamene “adzalenganso,” Mulungu adzathetsa tsankho. (Mateyu 19:28) Onse adzasangalala ndi ulemerero wofanana. Umenewu sudzakhala ufulu wolamulidwa ndi boma lankhanza. M’malo mwake, mikhalidwe yochititsa tsankho idzathetsedwa, kuphatikizapo dyera ndi kunyada zomwe zimachititsa anthu kulamulira anzawo mwankhanza kapena kudzikundikira chuma chambiri. Yesaya analosera kuti: “Ndipo iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka ndi wina kudya.”—Yesaya 65:21, 22.
Anthu avutika zedi chifukwa chakuphana pakati pa anthu wamba ndi kwa pankhondo zazikulu! Zimenezi zakhala zikuchitika kuyambira pakuphedwa kwa Abele kufikira m’nkhondo zamakono. Anthu ayembekezera ndi kudikiriradi kwa nthaŵi yaitali, kuti pakhale mtendere, koma mosaphulabe kanthu! M’paradaiso wobwezeretsedwa, anthu onse adzakhala amtendere ndi ofatsa; “adzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:11.
Yesaya 11:9 amati: “Dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” Mwa zina, chifukwa cha choloŵa cha kupanda ungwiro, n’kosatheka kwa ife lerolino kumvetsa cholinga chonse cha mawu ameneŵa. Chidziŵitso cha Mulungu changwiro chidzatigwirizanitsa ndi iye ndipo chimenecho chidzatidzetsera chimwemwe chochuluka, chomwe takhala tikuchiphunzirachi. Koma poti Malemba amanena kuti Yehova ndi Mulungu wamphamvu zodabwitsa, wanzeru, wachilungamo, ndi chikondi chochuluka, tingakhale wotsimikizira kuti adzamva mapemphero onse a anthu okhala “m’dziko lapansi latsopano.”
“Moyo Weniweni” Ndiwotsimikizirika—Ugwiritsitseni Mwakhama!
Kwa anthu ambiri, nkhani ya moyo wosatha m’dziko labwino imamveka ngati loto chabe kapena nkhambakamwa. Komabe, kwa omwe amakhulupiliradi malonjezo a m’Baibulo, chiyembekezo chimenechi n’chotsimikizirika. Chili ngati nangula wa miyoyo yawo. (Ahebri 6:19) Monga momwe nangula amagwiritsa zolimba chombo kuti chikhazikike malo amodzi osayendayenda, chiyembekezo cha moyo wosatha chimalimbitsa anthu kuti akhazikike ndi kuwapatsa chidaliro ndiponso chimaŵapangitsa kuyang’anizana ndi mavuto m’moyo ndi kuthana nawo.
Tingakhale otsimikizira kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake. Iye wafikira potsimikizira mwa lumbiro, choŵinda chosasinthika. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa oloŵa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analoŵa pakati ndi lumbiro; kuti mwa zinthu ziŵiri zosasinthika, m’mene Mulungu sakhoza kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathaŵira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu.” (Ahebri 6:17, 18) “Zinthu ziŵiri zosasinthika” zomwe Mulungu sangazisinthe ndi malonjezo ake komanso lumbiro lake, momwe ife timazika chiyembekezo chathu.
Kukhulupirira malonjezo a Mulungu kumakhala kotonthoza ndi kolimbikitsa mwauzimu. Yoswa, amene anatsogolera Aisrayeli, analinso ndi chikhulupiriro choterocho. Pamene Yoswa analankhula mawu otsazikira kwa Aisrayeli, anali wokalamba ndipo anadziŵa kuti imfa yake inali pafupi. Komabe, iye anasonyezabe chikhulupiriro champhamvu ndi cholimba, chochokera m’kukhulupirira kwake kwathunthu malonjezo a Mulungu. Atatha kunena kuti akumuka “njira ya dziko lonse lapansi,” njira imene imatsogolera mtundu wonse wa anthu ku imfa, Yoswa anati: “Ndipo mudziŵa m’mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anaŵanena za inu sanagwa padera mawu amodzi. Onse anachitikira inu. Sanasoŵapo mawu amodzi.” Inde, katatu konse Yoswa anabwereza kunena kuti Mulungu amasunga malonjezo ake onse nthaŵi zonse.—Yoswa 23:14.
Nanunso mungakhale ndi chikhulupiriro ngati chimenecho m’malonjezo a Mulungu a dziko latsopano lomwe likukhazikitsidwa posachedwapa. Mwa kuphunzira Baibulo ndi mtima wonse, mudzam’zindikira Yehova ndi chifukwa chake iye ali woyenerera kuti mum’khulupirire kwathunthu. (Chivumbulutso 4:11) Abrahamu, Sara, Isake, Yakobo, ndi okhulupirika ena akale anali ndi chikhulupiriro chosasweka, chozikidwa pa chidziŵitso chakuya cha Mulungu woona Yehova. Anakhalabe olimba m’chiyembekezo, ngakhale kuti iwo “sanalandire malonjezano” pamene anali moyo. Komabe, “adawaona ndi kuwalankhula kutali.”—Ahebri 11:13.
Mwa kumvetsetsa maulosi a Baibulo, tsopano tikutha kuona kuyandikira kwa “tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,” pamene kuipa konse kudzathetsedwa padziko lapansi. (Chivumbulutso 16:14, 16) Monga amuna okhulupirika akalewo, tiyenera kukhala ndi chidaliro pa chiyembekezo cha zomwe zidzachitika m’tsogolo, mosonkhezeredwa ndi chikhulupiriro, limodzinso ndi kukonda kwathu Mulungu ndi “moyo weniweni.” Pamene dziko latsopano likuyandikira, anthu amene ali okhulupirika kwa Yehova ndipo amam’konda, akusonkhezereka mwamphamvu. Kukhulupirika ndi chikondi za mtunduwu ziyenera kulimbikitsidwa kuti tipeze chiyanjo ndi chitetezo kwa Mulungu pamene tsiku lake lalikulu lifika.—Zefaniya 2:3; 2 Atesalonika 1:3; Ahebri 10:37-39.
Chotero, kodi inu m’maukonda moyo? Ndipo kodi mumakhumba kwambiri, “moyo weniweni”—moyo monga mtumiki wovomerezeka wa Mulungu, ndi chiyembekezo cha moyo wam’tsogolo wachimwemwe, inde, ndi moyo wosatha woyembekezeredwawo? Ngati chimenecho chili chikhumbo chanu, labadirani chilimbikitso cha mtumwi Paulo, yemwe analemba kuti tiyenera ‘kusayembekezera chuma chosadziŵika kukhala kwake koma mwa Mulungu.’ Paulo anapitiriza kuti: “Nachuluke ndi ntchito zabwino” zomwe zimalemekeza Mulungu, kuti “akagwire moyo weniweniwo.”—1 Timoteo 6:17-19.
Mwa kuvomera kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, mungapeze chidziŵitso chotsogolera ‘kumoyo wosatha.’ (Yohane 17:3) Chiitano chachikondi chimene timachipeza m’Baibulo chakuti: “Mwananga, usaiŵale malamulo anga; mtima wako usunge malangizo anga; pakuti adzakuwonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.”—Miyambo 3:1, 2.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri pankhaniyi, onani bolosha lakuti What Happens to Us When We Die?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.