Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 10/1 tsamba 16-17
  • Anathandiza Kuti Kuunika ‘Kufike Kumalekezero a Dziko Lapansi’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anathandiza Kuti Kuunika ‘Kufike Kumalekezero a Dziko Lapansi’
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Tinkachitira Zinthu Limodzi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Sekerani mwa Yehova Ndipo Kondwerani
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Yehova Amakokera Anthu Odzichepetsa ku Choonadi
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Mumavutika Kwambiri ndi Nkhawa?
    Galamukani!—2020
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 10/1 tsamba 16-17

Anathandiza Kuti Kuunika ‘Kufike Kumalekezero a Dziko Lapansi’

MTUMWI Paulo anagwiritsidwa ntchito pofalitsa kuunika kwauzimu “kufikira kumalekezero a dziko.” Zotsatira zake zinali zakuti, “anakhulupira onse amene anaikidwiratu ku moyo wosatha.”​—Machitidwe 13:47, 48; Yesaya 49:6.

Chikhumbo chachikulu chofalitsa kuunika kwauzimu chinali kuonekanso m’moyo wodzipereka ndi kuyesetsa kosatopa m’ntchito zauzimu kwa William Lloyd Barry, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Mbale Barry anamwalira pa July 2, 1999, pamene anali pa pologalamu ya msonkhano wachigawo ku Hawaii.

Lloyd Barry anabadwira ku New Zealand pa December 20, 1916. Mayi ndi bambo ake anali okangalika m’choonadi cha Baibulo cholembedwa m’zofalitsa za C. T. Russell, kale kwambiri, zofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society. Choncho, Mbale Barry anakulira m’banja la Akristu odzipereka zedi.

Ngakhale kuti anali wokonda maseŵero ndi maphunziro, ndipo anapeza digiri ya sayansi, Mbale Barry anapitirizabe kukhala wachidwi ndi zinthu zauzimu. Tsono, pa January 1, 1939, anayamba utumiki wa nthaŵi zonse, nakhala wa banja la Beteli ku ofesi ya nthambi ya Sosaite ku Australia. Boma litaletsa ntchito za Sosaite mu 1941, Mbale Barry anagwira ntchito ya muofesi. Nthaŵi zina ankamupatsa ntchito yolemba nkhani zolimbikitsa okhulupirira anzake. Anasonyezanso chitsanzo chabwino mwa kutsogolera mu ulaliki wapoyera.

Mu February 1942, Mbale Barry anakwatira mtumiki mnzake wanthaŵi zonse. Mkazi wake wachikondi, Melba, wagwira naye ntchito mokhulupirika m’zaka zonsezi m’madera ambiri a dziko lapansi. Anapita patsogolo mu utumiki wawo wokatumikira ku mayiko ena pamene anakaphunzira nawo m’kalasi la 11 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ku United States. Kumene anawatumizako ena anganene kuti ndiko ‘kumalekezero a dziko’​—ku Japan. Atafika kumeneko mu November 1949, anayamba kutumikira ngati amishonale mu mzinda wa kudoko la Kobe. Panthaŵiyo, munali alaliki a uthenga wabwino 12 okha mu Japan. Mbale Barry anaphunzira chinenero ndi moyo wa kwawo kwatsopanoku, ndipo anakonda anthu a ku Japan kwambiri, moti anatumikira nawo limodzi kwa zaka 25. Chikondi chake pa amene “anaikidwiratu ku moyo wosatha” chinaonekeratu pa ubale wachikristu womakulawo mu Japan, chomwe chinam’thandiza kutsogolera bwino nthambiyo kwa zaka zambiri.

M’katikati mwa chaka cha 1975, pamene munali Mboni 30,000 mu Japan, mbale ndi mlongo Barry anawasamutsira ku Brooklyn, New York. Monga Mkristu wodzozedwa ndi mzimu, Mbale Barry anaitanidwa kuti akatumikire m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. (Aroma 8:16, 17) Luso lake lolemba linathandiza kwambiri pa ntchito yake yatsopanoyo, m’Dipatimenti Yolemba. Ndiponso anali atatumikira kwa nthaŵi yaitali pa nthambi komanso m’mayiko ena. Zimenezi zinam’konzekeretsa kuti akhale wothandiza kwambiri m’komiti Yofalitsa ya Bungwe Lolamulira.

M’zaka zonsezi, Mbale Barry ankakondabe mayiko ndi anthu a Kum’mawa. Ophunzira pa Sukulu ya Gileadi ngakhalenso a m’banja la Beteli anatsimikiza kuti nkhani ndi ndemanga zake zinkasonyeza nkhani zokhudza mtima za ambiri omwe anachita utumiki wa umishonale. Ntchito yolalikira Ufumu ‘kumalekezero a dziko’ inagwirikadi monga momwe Mbale Barry analongosolera mwa chisangalalo zomwe iye anakumana nazo. Zina mwa izo zinanenedwa m’mbiri yake yomwe inafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya Chingelezi ya September 15, 1960.

Tili ndi chikhulupiriro kuti monga ‘woloŵa nyumba mnzake wa Kristu,’ chidwi cha Mbale Barry pa omwe “anaikidwiratu ku moyo wosatha” chipitirizabe. Ndithudi, onse amene anali kum’dziŵa ndi kum’konda monga munthu wauzimu, wodzipereka kotheratu kwa Yehova ndi wachikondi chakuya kwa anthu a Mulungu, adzam’sowa kwambiri. Komabe, tikusangalala kuti Mbale Barry anapirira mwa chikhulupiriro kufikira mapeto a moyo wake wa padziko lapansi.​—Chivumbulutso 2:10.

[Chithunzi patsamba 16]

Lloyd Barry ndi John Barr pamene “Insight on the Scriptures” linatulutsidwa mu 1988

[Chithunzi patsamba 16]

Omaliza maphunziro a kalasi la 11 la Gileadi, akumana ku Japan pambuyo pa zaka 40

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena