Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 11/15 tsamba 4-7
  • Baibulo Limayankha Mafunso Ofunika a M’tsiku Lathu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Baibulo Limayankha Mafunso Ofunika a M’tsiku Lathu
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuvutika?
  • Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?
  • Zimene Mulungu Amafuna kwa Ife
  • Kuunika Kodalirika kwa Panjira Pathu
  • Chifuno Chenicheni cha Moyo
    Galamukani!—1992
  • Moyo Uli ndi Chifuno Chachikulu
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
  • Kodi Cholinga cha Mulungu Ndi Choti Tikhale Ndi Moyo Wotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
    Kodi Kuli Mulungu Amene Amasamala?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 11/15 tsamba 4-7

Baibulo Limayankha Mafunso Ofunika a M’tsiku Lathu

KODI Baibulo n’lothandiza lerolino? Kuti yankho likhale lakuti inde, ndithudi buku lakale limeneli linayenera kupereka kwa oŵerenga ake chitsogozo pankhani zochititsa chidwi zomwe zafala posachedwapa komanso zofunika. Kodi Baibulo limapereka uphungu wopindulitsa pa nkhani zofunika kwambiri m’dziko lamakonoli?

Tatiyeni tione nkhani ziŵiri zomwe zafala zedi. Mwa kuchita zimenezo, tidzapenda zomwe Baibulo limakamba pa nkhani zimenezi.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuvutika?

Poona mkhalidwe wa zinthu m’dziko lerolino, limodzi la mafunso omwe amafunsidwa kaŵirikaŵiri n’lakuti: N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu osalakwa azivutika? Funso limeneli n’loyenera, chifukwa chakuti anthu ambiri akuvutika zedi ndi ziwawa, katangale, kupululutsa fuko, tsoka lokantha munthu payekha, ndi zina zotero.

Mwachitsanzo, mu June 1998, sitima inagwa pa mlato kumpoto kwa Germany ndi kupha anthu oposa 100 amene anali m’sitimayo. Ngakhale akatswiri a zamankhwala ndi ozimitsa moto amene anakathandiza ovulalawo ndi kutenga anthu akufawo anachita mantha poona mmene anthu anafera. Bishopu wina wa tchalitchi cha Evangelical Church anafunsa kuti: “Mulungu wokondedwa, n’chifukwa chiyani izi zachitika?” Bishopuyo sanathe kuyankha funsolo.

Zochitika zasonyeza kuti pamene anthu osalakwa akuvutika popanda kudziŵa chomwe chikuchititsa, nthaŵi zina amakwiya kwambiri. Pamenepo m’pomwe Baibulo lingathandize, chifukwa limalongosola chifukwa chake anthu osalakwa amakumana ndi kuipa komanso mavuto.

Pamene Yehova Mulungu anali kulenga dziko lapansi ndi zonse zili m’mwemo, sanafune kuti mtundu wa anthu udzizunzika ndi kuipa ndiponso mavuto. Kodi tingatsimikize bwanji zimenezo? Chifukwa atamaliza kulenga, “anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” (Genesis 1:31) Dzifunseni kuti, ‘Nditaona chinthu chinachake choipa, kodi ndinganene kuti “n’chabwino ndithu”?’ Ndithudi ayi! Mofananamo, pamene Mulungu ananena kuti zonse ndi “zabwino ndithu,” panalibe choipa chilichonse padziko lapansi. Tsono kuipaku kunayamba liti, ndipo kunayamba motani?

Atangolengedwa makolo athu oyambawo Adamu ndi Hava, cholengedwa chauzimu champhamvu chinafikira mkazi ndi kutsutsa choonadi cha uchifumu wa Yehova ndi kuyenera kwake. (Genesis 3:1-5) Cholengedwa chimenechi, Satana Mdyerekezi, pambuyo pake ananena mwanjiru kuti anthu sangakhale okhulupirika kwa Mulungu ngati akusautsidwa. (Yobu 2:1-5) Kodi Yehova anachitanji pa nkhaniyi? Analola nthaŵi kudutsa kuti pakhale umboni wokwanira wakuti anthu sangalongosole mapazi awo mwachipambano popanda chitsogozo chake. (Yeremiya 10:23) Ngati zolengedwa zichita mosemphana ndi malamulo ndi malangizo achikhalidwe a Mulungu, chotsatira chake ndi tchimo, lomwe limabala mikhalidwe yovulaza kwambiri. (Mlaliki 8:9; 1 Yohane 3:4) Komabe, Yehova anadziŵa kuti anthu ena adzakhalabe okhulupirika kwa iye, mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta imeneyi.

Kuchokera pamene upandu umenewo unachitika mu Edene, papita zaka 6,000. Kodi imeneyi ndi nthaŵi yaitali? Yehova akanatha kuwononga Satana ndi om’tsatira zaka mazana apitawo. Koma kodi sikoyenera kudikira, kufikira kukayikira kulikonse ponena za kuyenera kwa uchifumu wa Yehova, ndi kukhulupirika kwa anthu kwa iye kwathetsedwa? Kodi si zofanana ndi dongosolo la zamalamulo lamakono, kuti mlandu wa m’khoti umatenga zaka zambiri kuti apeze wolakwa ndi wosalakwa?

Poona kufunika kwa nkhani zokhudza Yehova ndi mtundu wa anthu, zomwe ndi ulamuliro wa chilengedwe chonse ndi kukhulupirika kwa anthu, Mulungu anasonyezadi nzeru zakuya zedi mwa kulola nthaŵi kudutsa! Tsopano tikuona bwino lomwe zomwe zimachitika pamene anthu anyalanyaza malamulo a Mulungu ndi kuchita zofuna zawo. Zotsatira zake ndi kuipa komwe kwafalaku. Ndipo chimenecho ndicho chifukwa chake anthu ambirimbiri osalakwa akuvutika lerolino.

Koma mwamwayi, Mawu a Mulungu amasonyeza kuti kuipa sikudzapitirira kunthaŵi zonse. Kunena zoona, Yehova posachedwapa adzathetsa kuipa ndi kuwononga onse amene amakuchititsa. “Koma oipa,” imatero Miyambo 2:22, “adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.” Komanso, omwe ali okhulupirika kwa Mulungu angayembekezere nthaŵi, yomwe tsopano yayandikira, pamene “sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”​—Chivumbulutso 21:4.

Choncho, Baibulo likulongosola bwino chifukwa chimene osalakwa akuvutikira. Likutitsimikiziranso kuti kuipa ndi mavuto zitha posachedwapa. Komabe, pamene tikukumana ndi mikwingwirima m’moyo uno, tikufunabe yankho la funso lina lofunikanso.

Kodi Cholinga cha Moyo N’chiyani?

Mwinamwake tsopano lino kuposa nthaŵi ina iliyonse m’mbiri ya mtundu wa anthu, anthu akuyesa kupeza chimene moyo umatanthauza. Ambiri amadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani ndili ndi moyo? Ndingapeze bwanji tanthauzo m’moyo wanga?’ Mikhalidwe yosiyanasiyana imawasonkhezera kudzutsa mafunso ameneŵa.

Moyo wa munthu ungawonongedwe ndi tsoka limene angakumane nalo. Mwachitsanzo, kuchiyambiyambi kwa 1998, msungwana wa zaka 12 wa ku Bavaria m’dziko la Germany, anabedwa ndi kuphedwa mwaumbanda. Chaka chimodzi chitadutsa, amayi ake anavomereza kuti amafufuza cholinga cha moyo tsiku lililonse, koma mosaphula kanthu. Achinyamata ena amadabwa ponena za tanthauzo la moyo. Amafunafuna chisungiko, kukhutiritsidwa, ndi unansi wathithithi, koma m’malo mwake amataya mtima chifukwa cha chinyengo ndi katangale yemwe wafalayu. Anthu ena amadalira kwambiri ntchito yawo, koma amaona kuti mphamvu, kutchuka, ndi chuma zimalephera kukhutiritsa chikhumbo chawo chamkati chofuna kupeza chifukwa chokhalira ndi moyo.

Mosasamala kanthu za china chilichonse chimene cham’sonkhezera munthu kufufuza za cholinga cha moyo, funso limeneli limafuna yankho lamphamvu ndi lokhutiritsa. Kachiŵirinso, Baibulo lingakhale lopindulitsa kwabasi. Limam’fotokoza Yehova monga Mulungu wa cholinga, yemwe ali ndi zifukwa zomveka pa chilichonse chomwe achita. Tingafunse kuti, Kodi mungamange nyumba popanda chifukwa china chilichonse? Mwachionekere ayi, chifukwa chakuti kumanga nyumba kumafuna ndalama zambiri ndipo mungatenge miyezi kapena zaka kuti mumalize. Mumamanga nyumba kuti inuyo kapena winawake azikhalamo. Zilinso chimodzimodzi ndi Yehova. Iye sanadzivutitse ndi ntchito yolenga dziko lapansi ndi zamoyo zonse zokhalamo popanda chifukwa, cholinga. (Yerekezani ndi Ahebri 3:4.) Kodi cholinga chake cha dziko lapansi n’chotani?

Ulosi wa Yesaya ukunena za Yehova kuti ndi “Mulungu [woona, NW], amene anaumba dziko lapansi, nalipanga.” Ndithudi iye ndi amene “analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Inde, chilengedwere dziko lapansi, cholinga cha Yehova n’chakuti likhalidwe ndi anthu. Salmo 115:16 limati: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” Choncho Baibulo limasonyeza kuti Yehova analenga dziko lapansi kuti anthu omvera omwe angathe kulisamala akhalemo.​—Genesis 1:27, 28.

Kodi kupanduka kwa Adamu ndi Hava kunapangitsa Yehova kusintha cholinga chake? Ayi. Tikutsimikiza bwanji zimenezo? Chabwino, lingalirani mfundo iyi: Baibulo linalembedwa zaka zikwi zambiri pambuyo pa kupandukako mu Edene. Ngati Mulungu wasiya cholinga chake choyambacho, bwanji nanga zimenezo sizinalembedwe m’Baibulo? Mfundo yachionekere n’njakuti cholinga chake cha dziko lapansi ndi mtundu wa anthu sichinasinthe.

Kuwonjezera pamenepo, cholinga cha Yehova sichilephera. Kudzera mwa Yesaya, Mulungu anapereka chilimbikitso ichi: “Monga mvula imagwa pansi ndi matalala, kuchokera kumwamba yosabwerera komweko, koma ikhamiza nthaka ndi kuibalitsa, ndi kuiphukitsa, ndi kuipatsitsa mbewu kwa wobzala, ndi chakudya kwa wakudya; momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”​—Yesaya 55:10, 11.

Zimene Mulungu Amafuna kwa Ife

Mwachionekere, tsopano, tingakhale ndi chidaliro m’kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Mulungu chakuti dziko lapansi lidzakhalidwe kosatha ndi anthu omvera. Ngati tikufuna kukhala m’gulu la odalitsidwa amenewo, odzakhala padziko lapansi kosatha, tiyenera kuchita zomwe Mfumu yanzeruyo Solomo inanena: “Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”​—Mlaliki 12:13; Yohane 17:3.

Kukhala mogwirizana ndi cholinga cha Yehova ku mtundu wa anthu kumatanthauza kum’dziŵa Mulungu woona ndi kutsatira zofunika zake zolembedwa m’Malemba Opatulika. Ngati tichita zimenezi tsopano lino, tingakhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso, momwe sitidzaleka kuphunzira zinthu zatsopano za Mulungu ndi chilengedwe chake chodabwitsa. (Luka 23:43) N’chiyembekezo chokondweretsa kwabasi!

Ambiri amene akufunafuna cholinga m’moyo, akutembenukira ku Baibulo ndi kupeza chimwemwe chochuluka tsopano lino. Mwachitsanzo, mnyamata wina wotchedwa Alfred analephera kupeza tanthauzo la moyo. Kuloŵerera m’nkhondo kwa chipembedzo ananyansidwa nako, ndipo anakhumudwa ndi chinyengo ndi katangale m’ndale. Alfred anakachezera Amwenye a ku North America, akumayembekezera kuti akaunikiridwa za cholinga cha moyo, koma m’malo mwake anabwerera ku Europe atalephera kupeza kalikonse. Anataya mtima ndipo anayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi kumvera nyimbo zoipa. Komabe, kusanthula Baibulo mosamalitsa nthaŵi ndi nthaŵi pambuyo pake kunam’thandiza Alfred kuzindikira cholinga chenicheni cha moyo ndi kupeza chikhutiro.

Kuunika Kodalirika kwa Panjira Pathu

N’chiyani nanga chimene tinganene pa Baibulo? Kodi n’lothandiza lerolino? Ndithudi, n’lothandiza, chifukwa limapereka chitsogozo pankhani zamakono. Baibulo limalongosola kuti sicholinga cha Mulungu kuti kuipa kuzichitika ndipo limatithandiza kupeza cholinga cha moyo chokhutiritsa. Komanso, Baibulo limafotokoza zochuluka pankhani zomwe zafala kwambiri lerolino. Nkhani monga za ukwati, kulera ana, ubwenzi wa anthu, ndi chiyembekezo cha omwe anamwalira, zafotokozedwa m’Mawu a Mulungu.

Ngati simunaŵerengepo zolembedwa m’Baibulo, chonde teroni tsopano lino. Mukazindikira kufunika kwake kwenikweni kwa zitsogozo zake m’moyo, mudzamva monga momwe anamvera wamasalmo yemwe anayang’ana kwa Yehova Mulungu kaamba ka chitsogozo ndi kuimba kuti: “Mawu anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.”​—Salmo 119:105.

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi mukudziŵa chifukwa chake Mulungu walolera kuti anthu osalakwa azizunzika?

[Chithunzi patsamba 7]

Mungasangalale ndi moyo wokhala ndi cholinga

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena