Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 11/15 tsamba 8-12
  • Kupatulira Likulu la Maphunziro a Watchtower—Madyerero a Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupatulira Likulu la Maphunziro a Watchtower—Madyerero a Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoonetsa Alendo Zipereka Phunziro
  • Pologalamu ya Kupatulira Igogomezera Maphunziro Aumulungu
  • Tikuphunzitsidwa ndi Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Malikulu a Maphunziro a Watchtower Atumiza Amishonale
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Sekerani mwa Yehova Ndipo Kondwerani
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kuphunzitsa Atumiki a Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 11/15 tsamba 8-12

Kupatulira Likulu la Maphunziro a Watchtower​—Madyerero a Yehova

KUYAMBIRA kale, madyerero okondweretsa akhala mbali ya kulambira koona. Madyerero ena omwe ankachitika m’Israyeli wakale ankatha masiku ochulukirapo ndipo kunkasonkhana mazanamazana a olambira a Yehova. Kuperekedwa kwa kachisi wa Solomo kunatenga masiku asanu ndi aŵiri ndipo mlungu wonse wotsatira panachitikanso Madyerero a Misasa. Zochitika zimenezi zinapatsa mwayi Aisrayeli wosinkhasinkha ponena za zodabwitsa zomwe Yehova wawachitira. Anabwerera kunyumba ali “osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachita.”​—1 Mafumu 8:66.

Zomwe zinachitika ku Likulu la Maphunziro a Watchtower ku Patterson, New York, U.S.A., pa May 17-22, 1999, zinakumbutsa alendo za madyerero okondweretsa akalewo. Umenewu unali mlungu wa chochitika chapadera, chokhudza kupatulira nyumba 28 zomwe anazimanga ndi cholinga chopititsa patsogolo maphunziro a Baibulo padziko lonse lapansi. M’kati mwa mlungu wosaiŵalika umenewo, anthu onse okwana 5,400 omwe akutumikira kulikulu ku Brooklyn, ku Wallkill, ndi ku Patterson, anawayendetsa ndi kuwaonetsa zinthu zosiyanasiyana ku Patterson. Ena mwa alendoŵa anali mamembala akale oposa 500 omwe anathandiza nawo pantchito yomanga likulu lamaphunziro limeneli, oimira nthambi 23 za Watch Tower Society, ndi enanso ochokera m’mipingo yapafupi ndi malowo. Onse pamodzi anali ngati 8,100.

Zoonetsa Alendo Zipereka Phunziro

Zionetsero zapadera, mavidiyo oonetsa zitsanzo zophunzitsa, ndiponso makonzedwe apadera oti alendowo ayendere malowo paokha, zinalinganizidwa ndi cholinga chakuti alendowo adziŵe bwinobwino likulu lamaphunziro limenelo. M’chipinda chachikulu cholandiriramo alendo, alendoŵa anachita chidwi kwambiri ndi chifanizo cha kachisi yemwe anali m’Yerusalemu m’nthaŵi ya utumiki wa Yesu wapadziko lapansi. Zionetsero zina zinasonyeza mbiri ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, misonkhano yosaiŵalika, misonkhano yampingo, mmene miyandamiyanda ya maphunziro a Baibulo apanyumba ochitidwa mlungu uliwonse amayambira masiku ano, komanso ntchito imene Dipatimenti ya Zamalamulo ikugwira kuti njira ya zochitika zimenezo ikhalebe yotseguka mwa kumvera lamulo la Yesu.​—Mateyu 28:19, 20.

M’nyumba yosonkhanira yomwe ili chapafupi pomwepo, mmene mungakhale anthu 1,700 motakasuka, obwera kumadyerero a kupatulirako, anaonera vidiyo yamphindi 33 yakuti “Not by Power​—By My Spirit!” (Ndi Mphamvu Ayi​—Ndi Mzimu Wanga!) Vidiyo imeneyi inaonetsa chiyambi cha Likulu la Maphunziro a Watchtower limeneli. Mayankho a abale omwe ankafunsidwa, anavumbula zochitika zomwe zinasonyeza bwino lomwe kuti Yehova anali kuwatsogolera ndi kuŵadalitsa pakuyesetsa kumaliza ntchito ya zaka 15 imeneyi mwachipambano. Zikwizikwi za anthu zinathandiza nawo ntchito yomangayo. Panthaŵi ina mu 1994, pamalopo panali antchito 526, kuphatikizapo antchito odzifunira a nthaŵi zonse okwana 350, antchito othandiza okwana 113, komanso ena okwana 63 omwe amayendera tsiku ndi tsiku kudzathandiza pa ntchito imeneyi. Enanso ambiri anathandizira ntchito imeneyi ndi zopereka. Onseŵa amazindikira kuti zimenezi sizikanatheka popanda mzimu wa Yehova.​—Zekariya 4:6.

Omwe anayendera likulu la maphunziroli anatha kuona kuti cholinga cha ntchito yonse imene ikuchitika kumeneku ndicho kupititsa patsogolo chiphunzitso chaumulungu. Chionetsero chomwe chinali poloŵera ku Sukulu ya Gileadi pansanjika yoyamba ya nyumba yasukuluyo chinasonyeza choloŵa chauzimu chaulemerero ndi mbiri ya sukuluyo. Kuyambira kalasi lake loyamba mu 1943 kumalo oyambirira a sukuluyi ku South Lansing, New York, Sukulu ya Gileadi yaphunzitsa anthu oposa 7,000 za utumiki waumishonale. Zionetsero zomwe zinali pansanjika yachiŵiri ya nyumba ya sukuluyi zinasonyeza Sukulu ya Mamembala a Makomiti a Nthambi ndi Sukulu ya Oyang’anira Oyendayenda. Masukulu onse aŵiriŵa amachitikira komweko. Chiyambire mu November 1995, sukulu ya nthambiyi yapereka malangizo apamwamba zedi kwa mamembala 360 a Makomiti a Nthambi ochokera m’mayiko 106.

Pamene alendowo anali kuyendera malowo, anazindikira mwamsanga kuti m’malo ambiri, amatha kuona zina ndi zina kuwonjezera pa zoonetsedwa zithunzi. Amakhoza kuloŵa mkati mwenimweni mwa madipatimenti osiyanasiyana, kuyendera maofesi ndi malo ena antchito, ndikuona bwino lomwe ntchito zomwe zikuchitika. Chochititsa chidwi kwambiri pa kuyenderako chinali Dipatimenti ya Makaseti/​Mavidiyo. Kumeneku akugwiritsa ntchito zipangizo zabwino kwabasi popititsa patsogolo maphunziro a Baibulo! Kupyolera m’zionetsero zopatsa chidziŵitso ndi mavidiyo afupiafupi omwe anali kuonera, alendowo anathandizidwa kumvetsa mmene kujambula mawu kumachitidwira komanso mmene mavidiyo amawakonzera. Anaphunzira kanthu kena ponena za kufufuza mozama kumene kumachitika pokonzekera zothandizira ndi zovala. Anaona mmene malo opangira seŵero amakonzedwera mosawononga ndalama zambiri koma atachita zonse zofunikira mosamalitsa. Anaonerera mmene nyimbo zimagwiritsidwira ntchito popangitsa anthu kudzimva ngati alidi m’chochitika chimene akuchionacho. Chiyambire mu 1990, Sosaite yapanga mavidiyo khumi m’zinenero 41, kusonyeza mitu yosiyanasiyana ya nkhani za m’Baibulo, kuphatikiza pa mavidiyo ena omwe anajambulidwa kaamba ka omwe amagwiritsa ntchito Chinenero Cholankhula ndi Manja cha ku America.

Alendo ambiri omwe anayendera malowo anapita Kokonzera Zithunzi, Dipatimenti Yojambula Zithunzi, Dipatimenti Yamakompyuta, yomwe imaphunzitsa ndi kusamalira za makompyuta, Dipatimenti Yoyang’anira Utumiki, yomwe imayang’anira ntchito za mipingo 11,242 ndi oyang’anira oyendayenda okwana 572, komanso Dipatimenti Yoyankha Makalata, kumene amayankha makalata ngati 14,000 a nkhani zosiyanasiyana chaka chilichonse. Anachita chidwi kwambiri ndi kufufuza kumene kumachitika pa makalata otumizidwa ndi kusonyeza kudera nkhaŵa kwenikweni awo amene mafunso awo akusonyezadi kuti akuyesa kuthetsa mavuto aakulu kwambiri.

Mpambo wosatha wa apaulendowo unakaonanso Dipatimenti Yoyang’anira Ntchito Yotembenuza. Anali odabwa kumva kuti zaka zisanu zapitazi, awonjezera zinenero zina 102 pa chiŵerengero cha zinenero zomwe Sosaite imafalitsira mabuku ofotokoza Baibulo. Padziko lonse lapansi, 80 peresenti ya Mboni za Yehova amaŵerenga zofalitsa za Sosaite m’zinenero zina kupatulapo Chingelezi. Popereka zofunika za anthuŵa, pali antchito odzifunira oposa 1,700 omwe akugwira ntchito yotembenuza m’mayiko 100. Zionetsero zinasonyeza Nsanja ya Olonda m’zinenero za ku America, Europe, Asia, ndi Africa. Alendowo anaonanso Baibulo la New World Translation litasindikizidwa m’zinenero 31 m’zomwe lafalitsidwa. Anamvanso kuti zofalitsa za Watch Tower tsopano zili m’zinenero zokwana 332 ndikutinso bulosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? lafalitsidwa m’zinenero 219 mwa zimenezi.

Ku Dipatimenti ya Zamalamulo, alendoŵa anaŵasonyeza mbali zosiyanasiyana za zochitika zomwe zimafuna kusamalidwa mwalamulo padziko lonse lapansi. Anaonera vidiyo ya mlandu womwe loya wa Mboni ankapereka mfundo zake pankhani yokhudza kuika magazi. Anamvanso zomwe akuchita ndi cholinga chakuti ntchito yolalikira uthenga wabwino isadodometsedwe. (Afilipi 1:7) Chomwe chinachititsa chidwi kwambiri chinali chigamulo chimene bwalo lamilandu la boma linapereka m’March chaka chino. Chigamulocho chinalamulira bungwe loyang’anira mlaga wa Oradell, New Jersey, U.S.A., kuti lisinthe malamulo ake, ndi kuti potero achotse lamulo lakuti ngati Mboni za Yehova zikufuna kuchita utumiki wapoyera kunyumba ndi nyumba m’mlagamo, ziyenera kulandira kaye chilolezo ndipo ziyeneranso kuvala baji.

Sizokhazo zomwe alendoŵa anaona. Mwa zina, m’nyumba yomwe amapangira makoma a nyumba, alendoŵa anaonanso zionetsero za ntchito yomanga ndiponso anayendera zipangizo zosefera madzi oipa, m’nyumba yomwe muli makina amphamvu zamagetsi ndi enanso otenthetsa madzi, zipangizo zothandiza posamalira madzi, ndi nyumba zina zambiri za okonzanso zinthu zikawonongeka. Unalidi mwayi wapadera zedi.

Pologalamu ya Kupatulira Igogomezera Maphunziro Aumulungu

Pologalamu yeniyeni ya kupatulira inachitika Lachitatu, pa May 19, kuyambira 4:00 p.m. Khamu la anthu achimwemwe okwana 6,929 kuphatikizapo ogwira ntchito ku likulu, alendo a Sosaite, komanso anthu okwana 372 anasonkhana pa nthambi ya Canada kumene ankaonera pa wailesi yakanema zonse zimene zinkachitika.

Anthu anasangalala zedi kumva mawu amalonje ogwira mtima a Milton G. Henschel, pulezidenti wa Watch Tower Society. Pambuyo pake, Theodore Jaracz, wa m’Bungwe Lolamulira yemwenso anali tcheyamani wa mwambowo, anaitana William Malenfant. Pokamba “Mfundo Zazikulu za Ntchito Yomanga,” iye anafunsa abale atatu omwe anali ndi gawo lofunika kwambiri kulinganiza, kulemba mapulani, ndi kumanga kwa Likulu la Maphunziro a Watchtower limeneli. Kufunsako kuli mkati, anafotokoza kuti m’zaka zomwe ntchito yomangayo inagundika, antchito othandizira oposa 8,700 ankabwera kudzagwira nawo ntchito imeneyi atadzilipirira okha ulendowo. Umboni wabwino zedi umenewu wa mgwirizano ndi kuoloŵa manja kotheketsedwa ndi chiphunzitso chaumulungu!

Kenako panaperekedwa nkhani yosiyirana yokhala ndi mutu wakuti “Maphunziro Aumulungu a Padziko Lonse Lapansi.” Inakambidwa ndi anthu anayi a m’Bungwe Lolamulira. John E. Barr anagogomezera kuti maziko a maphunziro aumulungu ndi Mawu a Mulungu, Baibulo, lomwe limalimbikitsa Akristu “kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu.” (Akolose 1:10) Daniel Sydlik anafotokoza mmene maphunziro aumulungu akulinganizidwira mwateokalase ndi mutu wa mpingo wachikristu, Yesu Kristu, kufikira kwa aliyense m’gulu la abale lapadziko lonse. (1 Akorinto 12:12-27) Mbali zothera ziŵiri za nkhani yosiyirana imeneyi, zokambidwa ndi Gerrit Lösch ndi Carey Barber, zinasonyeza mmene maphunziro aumulungu amakonzera atumiki kuti afikire anthu kulikonse ndi kuwalangiza kuti nawonso ayende m’njira ya Mulungu.​—Yesaya 2:1-4; 2 Akorinto 3:5.

Kuti adziŵitse omvetsera za sukulu zosiyanasiyana zomwe zili palikulu lamaphunziro limeneli, alangizi ndi ena oyendetsa masukuluwo anawafunsa ndi kukambirana nawo. Anasonyeza cholinga cha sukulu iliyonse pantchito yophunzitsa maphunziro aumulungu padziko lonse lapansi. Analongosola kuti maphunziro a Sukulu ya Gileadi n’ngozikika pa kuphunzira buku limodzilimodzi la m’Baibulo, mbiri yamakono ya anthu a Yehova, ndiponso kukonzekera utumiki wa umishonale. Sukulu yanthambi ndiyo maphunziro ochititsa chidwi kwambiri okhudza mbali zambiri za ntchito yomwe mamembala a Komiti ya Nthambi amagwira. Cholinga cha Sukulu ya Oyang’anira Oyendayenda sikungokwaniritsa zofunika zazikulu za abale oyendayendawo ayi, komanso kuwakonzekeretsa bwino lomwe kuti azitha kupereka thandizo lauzimu lomwe kwenikweni lingakhale lopindulitsa mipingo.

Kumapeto kwa Pologalamu yabwinoyi, Lloyd Barry wa Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yopatulira yokhala ndi mutu wakuti “Kumanga ndi Mlengi wathu Wamkulu.” Ananena kuti Mlengi, Yehova, amasangalala kwambiri ndi zolengedwa zake zonse ndipo akufuna kuti tisangalale naye. (Yesaya 65:18) Popeza kuti “wozimanga zonse ndiye Mulungu,” zitamando zonse ziyenera kupita kwa Yehova Mulungu kaamba ka ntchito zomanga zimenezi. (Ahebri 3:4) Wokamba nkhaniyo atafotokoza maganizo ameneŵa, anapereka pemphero lochokera pansi pa mtima, kupatulira Likulu la Maphunziro a Watchtower kwa Yehova, Mlengi wathu Wamkulu.a

Tili ndi chikhulupiriro kuti madyerero omwe anatenga mlungu wathunthu ameneŵa, sadzaiŵalika kwa onse amene anapezekapo. Bwanji osakonzeka kuti mukaone Likulu la Maphunziro a Watchtower? Tili ndi chikhulupiriro kuti kudzaona ndi kuyendera malowa kudzakhala kolimbikitsa kwa inu pa kuyesetsa kwanu kufuna kuphunzira zochuluka za Mlengi wathu wachikondi ndi kukhala m’miyezo yake yolungama.

[Mawu a M’munsi]

a Mbale Barry anatsiriza moyo wake wa padziko lapansi mokhulupirika pa July 2, 1999. Onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 1999, tsamba 16.

[Zithunzi patsamba 10]

Anthu adzaza m’holo yosonkhanira ndipo omvetsera ena akhala m’chipinda chodyera

[Zithunzi patsamba 10]

Kuyendera malowo kunali kosangalatsa zedi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena