Tikuphunzitsidwa ndi Yehova
1 Motsogozedwa ndi Mulungu, tsopano pologalamu yophunzitsa yapadziko lonse ikuchitika m’mayiko 233. M’dzikoli palibe china chimene chingafanane nayo. Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova, akutiphunzitsa mmene tingapindulire pakali pano pamene akutiphunzitsanso za moyo wosatha.—Yes. 30:20; 48:17.
2 Sukulu za Maphunziro Aumulungu: Onani sukulu zimene tsopano lino zikuchitika kaamba ka phindu la anthu a Yehova. Sukulu ya Utumiki Wateokalase, yochitika mlungu uliwonse m’mipingo 87,000, imaphunzitsa mamiliyoni a ofalitsa Ufumu kukhala atumiki a uthenga wabwino ogwira mtima. Kodi munalembetsa m’sukuluyi? Kodi ndinu mmodzi wa anthu zikwizikwi amene anapita ku Sukulu ya Utumiki Waupainiya ya milungu iŵiri? Mwina kuchepetsedwa kwa maola a apainiya okhazikika kupangitsa anthu ambiri kuchita upainiya ndi kukhala oyenera kupita kusukulu imeneyi. Sukulu Yophunzitsa Utumiki ya miyezi iŵiri, imene tsopano ikuchitika m’zinenero zikuluzikulu padziko lonse, ikukonzekeretsa akulu ndi atumiki otumikira amene ali osakwatira kukhala ndi maudindo ateokalase owonjezereka. Nthaŵi ndi nthaŵi, akulu ndi atumiki otumikira amalandira malangizo apadera m’Sukulu ya Utumiki wa Ufumu.
3 Malikulu a Maphunziro a Watchtower ku Patterson, New York, akugwiritsidwa ntchito kuchitirapo sukulu zitatu zapadera, zimene zimapereka maphunziro apamwamba ateokalase. Maphunziro a miyezi isanu a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower amakonzekeretsa atumiki m’ntchito ya umishonale m’mayiko akunja. Mamembala a m’Makomiti a Nthambi padziko lonse amapita kusukulu ya miyezi iŵiri ya kayendetsedwe ka nthambi. Mu May 1999 sukulu yatsopano ya miyezi iŵiri ya oyang’anira oyendayenda inayamba ndi ophunzira 48 ochokera ku United States ndi Canada. Pomalizira pake, atumiki a Yehova onse amapeza mapindu kuchokera m’maphunziro amene Yehova akupereka kudzera m’sukulu zosiyanasiyana zimenezi.
4 Kuphunzitsidwa ndi Cholinga Chotani? Wa m’Bungwe Lolamulira wina anati: “Pologalamu yathu yamakono yophunzitsa yakonzedwa kuti ithandize anthu a Yehova kulikonse kufika pa kukula msinkhu kofotokozedwa pa Miyambo 1:1-4.” Yehova apitirizetu kupereka kwa aliyense wa ife “lilime la ophunzira.”—Yes. 50:4.