Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 12/15 tsamba 25
  • Analimba Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Analimba Mtima
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Tsanzirani Yesu mwa Kulalikira Molimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2009
  • ‘Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima’
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Mumalalikira Molimba Mtima?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Pitirizani Kulankhula Mawu a Mulungu Molimbika Mtima
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 12/15 tsamba 25

Analimba Mtima

NTHAŴI zina kulimba mtima kuti tilalikire kumakhala kovuta. Ngakhale mtumwi Paulo ananena kuti panthaŵi ina, anachita zimenezo “movutikira kwambiri.” (1 Atesalonika 2:2, NW) Kodi ‘kuvutika’ polalikira kumeneku n’kwaphindu? Sikuti nthaŵi zonse padzakhala zokumana nazo zodabwitsa, koma nthaŵi zambiri anthu a Mulungu amakondwera kuti analimba mtima. Talingalirani zitsanzo zina.

Mtsikana wa zaka zakubadwa zisanu ndi zitatu wotchedwa Tara anamvetsera mosamala pamene mphunzitsi wake anauza kalasi lake kuti panthaŵi ya nkhondo yachiŵiri yapadziko lonse, Ayuda omwe anali m’misasa yachibalo anali kuvala chizindikiro cha Nyenyezi ya Davide chachikasu kuti azidziŵika. Tara anaganizaganiza ngati ayenera kutchulapo mfundo ina. “Ndinapemphera osatseka maso,” iye anatero pokumbukira. Kenako anatukula mkono ndi kunena kuti Mboni za Yehova zinalinso m’misasa yomweyo, ndipo zinkavala chizindikiro chofiirira cha makona atatu. Mphunzitsiyo anachita chidwi ndipo anam’thokoza. Ndemanga ya Tara inatsegula mpata wokambirana zowonjezeka ndi mphunzitsiyo, amene pomalizira pake anasonyezanso kalasi lonselo vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault (Mboni za Yehova Zichirimika Nkhanza za a Nazi).

M’dziko la Guinea, ku West Africa, wofalitsa wosabatizidwa wachinyamata wotchedwa Irène ankafuna kupita patsogolo mu utumiki wake. Mmishonale amene ankaphunzira naye Baibulo anam’limbikitsa kuti ayese kugaŵira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa anzake a kusukulu. Irène anazengereza chifukwa chakuti anzake a m’kalasi lakelo sankafuna kumvetsera. Komabe, atasonkhezeredwa ndi chilimbikitso cha mmishonaleyo, Irène anaganiza kuyamba kufikira wophunzira amene anali kutsutsa kwambiri. Irène anadabwa kuti mtsikanayo anamvetsera ndipo analandira magaziniwo mofunitsitsa. Ophunzira ena anachitanso chimodzimodzi. Irène anagaŵira maganizi ochuluka kwambiri mweziwo kuposa amene anagaŵira m’miyezi yonse isanu yoyambirira .

Ku Trinidad mkulu wina ankazengereza zokafikira mphunzitsi wamkulu pasukulu inayake kuti akam’sonyeze ubwino wa magazini ya Galamukani! m’zamaphunziro. Komabe, analimba mtima. Iye anati: “Ndinapemphera mmene ndinkaloŵa m’mudzi wawo. Ndinalibe mawu nditaona kuti mphunzitsiyo anasangalala kwambiri.” Analandira magazini ya Galamukani! yakuti “Kodi Achinyamata Amakono Ali ndi Tsogolo Lotani?” ndipo analolanso kuigwiritsa ntchito pophunzitsa m’kalasi. Kuyambira pamenepo, walandira magazini 40 okhala ndi nkhani zosiyanasiyana.

Pamene anali wachinyamata, nthaŵi zonse Vaughn anali kuvutika kwambiri kuti alalikire. “Ndinali kuchita mantha, zikhato zangazi zinali kutuluka thukuta, ndipo ndinali kuyankhula mofulumira kwambiri, osayankhulako pang’onopang’ono.” Komano anakhala mtumiki wanthaŵi zonse. Chimodzimodzibe, nthaŵi zina anali kuvutika kuti alimbe mtima ndi kuyankhula. Tsiku lina, atatopa ndi kufunafuna ntchito, anafuna kulalikira kwa winawake m’sitima, “kuti mwina n’kupindulabe patsiku loipalo.” Koma anachita mantha ndi anthu amabizinesi ooneka kukhala apamwamba omwe anali m’sitima ya pansi panthakayo. Pomalizira pake, analimba mtima kuti ayankhule ndi mwamuna wachikulire yemwe anakhala pafupi naye. Chotsatira chake, anakambirana kwanthaŵi yaitali. “Ukufunsa mafunso anzeru chonchi pamsinkhu wakowu,” wabizinesiyo anatero, nafunsa kuti, “Kodi unapita kukoleji ya maphunziro a zaumulungu?” Vaughn anayankha kuti, “Ayi, ndine mmodzi wa Mboni za Yehova.” Mwamunayo anamwetulira nati, “Oho, apo m’pomveka.”

Mboni zonsezi ndi zinanso zosaŵerengeka, n’zosangalala kuti zinalimba mtima kuti zilalikire. Kodi inunso mudzatero?

[Chithunzi patsamba 25]

Tara

[Chithunzi patsamba 25]

Vaughn

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena