Ukwati Wolemekezeka kwa Mulungu ndi kwa Anthu
“Panali ukwati m’Kana . . . ndipo Yesu . . . ndi akuphunzira ake anaitanidwa ku ukwatiwo.”—YOHANE 2:1, 2.
1. Kodi nkhani yonena za Yesu ali ku Kana imatiuza za chiyani?
YESU, amayi ake, ndiponso ena mwa ophunzira ake ankadziwa kuti ukwati wolemekezeka wa anthu a Mulungu umakhala wosangalatsa. Ndipo Kristu anachititsa ukwati wina kukhala wapadera ndi wosangalatsa kwambiri mwa kuchita chozizwitsa chake choyambirira kulembedwa m’Baibulo. (Yohane 2:1-11) N’kutheka kuti mwasangalalapo kupita ku ukwati wa Akristu ofuna kutumikira Yehova monga banja losangalala. Kapena mwina mukuyembekezera kuchita ukwati woterowo kapena mufuna kuthandiza mnzanu kuti ukwati wake udzakhale wosangalatsa. Kodi n’chiyani chingathandize kuti zinthu zidzayende bwino?
2. Kodi Baibulo lili ndi nkhani zotani zokhudza ukwati?
2 Akristu aona kuti malangizo a m’Mawu ouziridwa a Mulungu n’ngothandiza kwambiri mwamuna ndi mkazi akamakonzekera ukwati. (2 Timoteo 3:16, 17) N’zoona kuti Baibulo lilibe mfundo zatsatanetsatane za mmene ukwati wachikristu uyenera kuchitikira. M’pomveka kuti silitero chifukwa miyambo ndi malamulo a boma amasiyanasiyana malinga ndi malo komanso nthawi. Mwachitsanzo, kalekale, ku Israyeli kunalibe mwambo wapadera wa ukwati. Tsiku la ukwati, mkwati ankatenga mkwatibwi n’kupita naye kunyumba kwake kapena kunyumba kwa atate ake. (Genesis 24:67; Yesaya 61:10; Mateyu 1:24) Ukwati unkachitika anthu akaonerera mwambowu. Sipankakhala mwambo wina wapadera monga momwe zimakhalira pa ukwati wa masiku ano.
3. Kodi Yesu anathandizapo pa mwambo wotani ku Kana?
3 Aisrayeli ankaona kuti munthu akachita zimenezi ndiye kuti wakwatira. Nthawi zina akatero ankachitanso phwando. Lemba la Yohane 2:1 limati: ‘Panali ukwati m’Kana.’ Koma mawu a chinenero choyambirira omwe anamasuliridwa kuti ukwati palembali, angakhale bwino kuwamasulira kuti “phwando la ukwati” kapena kuti “madyerero a ukwati.”a (Mateyu 22:2-10; Luka 14:8) Nkhaniyi imanena momveka bwino kuti Yesu analipo ndipo anathandizapo pa phwando la ukwati wachiyuda. Pamenepa, mfundo yaikulu n’njakuti, zomwe zinkachitika pa ukwati nthawi imeneyo n’zosiyana ndi zinthu zimene zimachitika masiku ano.
4. Kodi Akristu ena amasankha kuchita ukwati wotani, ndipo n’chifukwa chiyani?
4 Masiku ano, m’mayiko ambiri muli malamulo amene Akristu ofuna kulowa m’banja amafunika kutsatira. Akatero, angathe kumangitsa ukwati wawo m’njira iliyonse yovomerezeka ndi boma. Angachite zimenezi mwina pa mwambo waung’ono ndiponso wosavuta kuutsatira wochititsidwa ndi woweruza milandu, meya, kapena mtumiki wachipembedzo wovomerezedwa ndi Boma. Ena amasankha kukwatira mwa njira imeneyi, mwina ataitana achibale kapena anzawo achikristu angapo kuti adzachitire umboni kapena kungofuna kuti adzasangalalire limodzi pa mwambo wofunika umenewu. (Yeremiya 33:11; Yohane 3:29) Komanso, Akristu ena angasankhe kuti asakhale ndi phwando lalikulu la ukwati lomwe lingafune zinthu ndiponso ndalama zambiri pokonzekera. M’malo mwake, angakonze zoitana anzawo apamtima ochepa kuti akhale nawo pa chakudya. Chilichonse chomwe tingasankhe kuchita pankhaniyi, tiyenera kuzindikira kuti Akristu ena okhwima maganizo angakhale ndi maganizo osiyana ndi athu.—Aroma 14:3, 4.
5. N’chifukwa chiyani Akristu ambiri akamakwatirana amafuna kukhala ndi nkhani ya ukwati, ndipo kodi nkhaniyi imakhala yotani?
5 Akristu ambiri amasankha kuti pa ukwati wawo padzakambidwe nkhani ya m’Baibulo.b Amazindikira kuti Yehova ndiye anayambitsa ukwati ndipo m’Mawu ake anaikamo malangizo anzeru othandiza kuti banja liyende bwino komanso kuti likhale lachimwemwe. (Genesis 2:22-24; Marko 10:6-9; Aefeso 5:22-33) Ndiponso ambiri amafuna kuti anzawo komanso achibale awo achikristu asangalalire nawo limodzi pa mwambowo. Komano, kodi tiyenera kuona motani kusiyana komwe kulipo pa malamulo a boma, dongosolo, ngakhalenso miyambo ya ukwati yofala m’madera osiyanasiyana? Nkhani ino ifotokoza zimene zimachitika m’madera osiyanasiyana. Zina zingasiyane kwambiri ndi zimene inu mumadziwa kapena zomwe zimachitika m’dera lanu. Komabe, mupeza mfundo kapena zochitika zina zomwe ndi zofunika kwa atumiki onse a Mulungu.
Ukwati Wotsatira Malamulo Umakhala Wolemekezeka
6, 7. N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza zimene malamulo a boma amafuna pankhani ya ukwati, ndipo tingachite motani zimenezo?
6 Ngakhale kuti Yehova ndiye anayambitsa ukwati, maboma a anthu ali ndi malamulo amene amafuna kuti anthu omwe akukwatirana awatsatire. M’poyenera kutsatira zimenezo. Yesu anati: “Perekani zake za Kaisara kwa Kaisara, ndi zake za Mulungu kwa Mulungu.” (Marko 12:17) Mtumwi Paulo nayenso analangiza kuti: “Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.”—Aroma 13:1; Tito 3:1.
7 M’mayiko ambiri, Kaisara kapena kuti boma, ali ndi malamulo pankhani ya munthu woyenerera kukwatira kapena kukwatiwa. Motero, Akristu awiri amene ali omasuka mwa Malemba akasankha kuti akwatirane, amayesetsa kutsatira malamulo a dziko lawo. Mwina pangafunike kutenga mtchatho, kumangitsa ukwati pamaso pa munthu woimira boma pa za ukwati, ndipo mwinanso kukalembetsa m’kaundula, dongosolo lonse la ukwati likatha. Kaisara Augusto atalamula kuti pachitike ‘kalembera,’ Mariya ndi Yosefe anamvera lamulolo, n’kupita ku Betelehemu “kukalembedwa.”—Luka 2:1-5.
8. Kodi ukwati uli ndi mphamvu zotani, ndipo Mboni za Yehova zimachita chiyani posonyeza kuti zimamvetsa mfundo imeneyi?
8 Akristu akakwatirana motsatira malamulo ndiponso movomerezeka, Mulungu amaona kuti mgwirizano wa anthu awiriwo wayamba kugwira ntchito. N’chifukwa chake Mboni za Yehova sizibwereza mwambo wa ukwati mwa kuchita miyambo yambirimbiri ya lamulo, ndiponso sizibwereza malumbiro a ukwati, monga pachikondwerero choti mwamuna ndi mkazi akwanitsa zaka 25 kapena 50 ali m’banja. (Mateyu 5:37) (Matchalitchi ena amanyalanyaza ukwati wolembetsa ku boma, n’kumati si ukwati weniweni pokhapokha wansembe kapena mbusa akachita mwambo wake kapena akalengeza kuti anthuwo akwatirana.) M’mayiko ambiri, boma limapatsa mtumiki wa Mboni za Yehova mphamvu zomangitsira ukwati. Ngati n’zotheka kutero, iye angafune kumangitsa ukwati panthawi ya nkhani ya ukwatiwo pa Nyumba ya Ufumu. Awa ndi malo a kulambira koona m’dera lililonse, ndipo ndi oyenera kukambiramo nkhani ya mwambo woterewu, umene unayambitsidwa ndi Yehova Mulungu.
9. (a) Ngati ukwati wamangitsidwira ku boma, kodi mwamuna ndi mkazi wachikristu angasankhe kuchita chiyani? (b) Kodi akulu angakhudzidwe motani ndi ntchito yokonzekera ukwati?
9 M’mayiko ena muli malamulo akuti mwamuna ndi mkazi azikamangitsa ukwati wawo ku maofesi a boma, monga ku maofesi a akuluakulu oyang’anira mzinda, kapena malamulo oti ukwati wawo azikaumangitsa pamaso pa munthu woimira boma. Nthawi zambiri Akristu amasankha kuti pambuyo pa mwambo wa lamulo umenewu akhale ndi nkhani ya ukwati pa Nyumba ya Ufumu tsiku lomwelo kapena tsiku lotsatira. (Safuna kuti kuchokera patsiku la mwambowo, padutse masiku ambiri asanakhale ndi nkhani ya m’Baibuloyo, chifukwa chakuti kwa Mulungu, anthu, ndiponso ku mpingo wachikristu, iwo amakhala atakwatirana mwa lamulo.) Ngati mwamuna ndi mkazi amene adzamangitsire ukwati wawo ku boma akufuna kudzakhala ndi nkhani pa Nyumba ya Ufumu, ayenera kupempheratu chilolezo kwa akulu a m’Komiti ya Utumiki ya Mpingo. Kuwonjezera pa kutsimikizira kuti mwamuna ndi mkaziyo ali ndi mbiri yabwino, akulu amenewa amaonetsetsanso kuti nthawi ya ukwatiwo sikusokoneza misonkhano ya nthawi zonse ndiponso zinthu zina zimene zakonzedwa kudzachitikira pa nyumbayo. (1 Akorinto 14:33, 40) Amaonanso bwino pempho la akwatiwo la mmene adzakonzere Nyumba ya Ufumuyo, ndipo amaonanso ngati kungakhale kofunikira kulengeza za ukwatiwo.
10. Ngati pangafunikire kukamangitsa ukwati ku boma, kodi nkhani ya ukwati ingakhudzidwe motani ndi zimenezi?
10 Mkulu wokamba nkhaniyo amayesetsa kuikamba mwaubwenzi, mwaulemu ndiponso moti iwalimbikitse anthu mwauzimu. Ngati mwamuna ndi mkaziyo ayamba ndi kumangitsa ukwati wawo pamaso pa nthumwi ya boma, mkulu wokamba nkhaniyo ayenera kufotokoza momveka bwino kuti anthuwo anakwatirana mogwirizana ndi malamulo a Kaisara. Ngati pamwambo wa ku bomawo panalibe malumbiro a ukwati, mwamuna ndi mkaziyo angafune kuchita zimenezo m’kati mwa nkhaniyo.c Ngati analumbira kale pa mwambowo, koma mwamuna ndi mkazi ongokwatirana kumenewo akufuna kulumbira pamaso pa Yehova ndiponso mpingo, ayenera kugwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti analumbira kale, zomwe zingasonyeze kuti anthuwo ‘anamangidwa [kale] pamodzi.’—Mateyu 19:6; 22:21.
11. Kodi anthu amakwatirana motani m’madera ena, ndipo zimenezo zimakhudza motani nkhani ya ukwati?
11 M’madera ena mulibe malamulo ofuna kuti mwamuna ndi mkazi akwatirane mwa mwambo winawake, ngakhalenso ofuna kumangitsira ukwati pamaso pa nthumwi ya boma. Ukwati umachitika iwo akapereka ku boma chikalata chosainidwa cholembetsera ukwati. Akatero, amalowetsa m’kaundula mtchatho wa ukwatiwo. Zikatero, anthu awiriwo amaonedwa kuti ndi mwamuna ndi mkazi wake, ndipo tsiku lomwe laikidwa pa mtchatho wawo ndilo limakhala tsiku la ukwati wawo. Monga momwe taonera kale, anthu amene akwatirana mwa njira imeneyi angafune kuti pambuyo polembetsa ukwati akhale ndi nkhani ya m’Baibulo pa Nyumba ya Ufumu. Mbale wokhwima mwauzimu amene wasankhidwa kukamba nkhaniyi amadziwitsa anthu onse obwera ku mwambowo kuti anthu awiriwo akwatirana kale chifukwa chakuti adula kale mtchatho. Malumbiro alionse ayenera kuchitika mogwirizana ndi zimene zafotokozedwa m’ndime 10 ndiponso m’mawu a m’munsi a ndimeyi. Anthu ofika pa Nyumba ya Ufumu adzasangalalira limodzi ndi akwatiwo ndiponso kupindula ndi malangizo a m’Mawu a Mulungu.—Nyimbo ya Solomo 3:11.
Ukwati Wotsatira Mwambo Komanso Womangitsa ku Boma
12. Kodi ukwati wotsatira mwambo ndi ukwati wotani, ndipo m’pofunika kuchita chiyani pambuyo pa ukwati woterowo?
12 M’mayiko ena, mwamuna ndi mkazi amatha kuchita ukwati wotsatira mwambo (kapena kuti chikhalidwe). Izi sizikutanthauza kungokhalira pamodzi kwa mwamuna ndi mkazi, kapena ukwati wina umene umangotengedwa ngati ukwati kumalo ena koma womwe si wovomerezeka mwa malamulo.d Koma ukwati wotsatira mwambo womwe tikunena pano ndi ukwati umene anthu alowa mogwirizana ndi miyambo yovomerezeka ndi mtundu kapena anthu ambiri m’dera lawolo. Mwa zina, mwina pangakhale kupereka ndi kulandira malowolo onse, ndipo akatero mwamuna ndi mkaziyo amakhala okwatirana mwalamulo komanso mogwirizana ndi Malemba. Boma limaona ukwati wa mwambo woterowo kuti ndi wovomerezeka, walamulo ndiponso woti sungathe wambawamba. Zimatheka kukalembetsa ku boma ukwati womwe wachitika motsatira mwambo, ndipo anthuwo akatero, mwamuna ndi mkaziyo amatha kupatsidwa mtchatho. Kulembetsa ukwatiwo kungateteze mwamuna ndi mkaziyo mwalamulo kapena kungathe kuteteza mkazi ngati mwamuna wamwalira ndiponso kungadzateteze ana m’tsogolo. Mpingo ungalimbikitse aliyense amene wakwatira motsatira mwambo kuti akalembetse mwamsanga ukwati wakewo. N’zochititsanso chidwi kuona kuti m’nthawi ya Chilamulo cha Mose, anthu ankalembetsa ukwati ndiponso kubadwa kwa mwana.—Mateyu 1:1-16.
13. Pambuyo pa ukwati wotsatira mwambo, kodi m’pofunika kuchitanji ndi nkhani ya ukwati?
13 Anthu amene akwatirana mwalamulo pa ukwati wotsatira mwambo, amayamba kukhala mwamuna ndi mkazi wake akamangitsa ukwatiwo. Monga momwe taonera kale, Akristu amene akumangitsa ukwati wawo mwalamulo angafune kukhala ndi nkhani ya ukwati, komanso kupanga malumbiro a ukwati, pa Nyumba ya Ufumu. Ngati zatero, wokamba nkhaniyo ayenera kunena kuti anthuwo anakwatirana kale mogwirizana ndi malamulo a Kaisara. Nkhani imeneyi iyenera kukambidwa kamodzi basi. Ukwati wotsatira mwambo (chikhalidwe) komanso wovomerezeka ndi malamulo umenewu ndi umodzi, n’chifukwa chakenso pamakhala nkhani imodzi ya m’Malemba. Kuyesetsa kuti mwambo womangitsa ukwati ndi nkhani yake zisatalikirane kwambiri, mwina zichitike tsiku limodzi, kumathandiza kuti anthu m’deralo azilemekeza ukwati wachikristu.
14. Kodi Mkristu angachite chiyani ngati n’zotheka kuchita ukwati wotsatira mwambo ndiponso womangitsa ku boma?
14 M’mayiko ena kumene ukwati wotsatira mwambo umakhala wovomerezeka mwalamulo, mulinso dongosolo loti ukwati uzimangitsidwa ku boma. Ukwati womangitsa ku boma nthawi zonse umachitikira pamaso pa nthumwi ya boma, ndipo mwina pangachitike zinthu zonse ziwiri, kupanga malumbiro a ukwati ndiponso kusaina mu kaundula. Akristu ena amakonda ukwati womangitsira ku boma kusiyana ndi ukwati wotsatira mwambo. Palibe malamulo amene amafuna kuti munthu achite ukwati wa mitundu yonse iwiri; mtundu uliwonse wa ukwatiwu ndi wovomerezeka mwalamulo. Mfundo zimene tanena m’ndime 9 ndi 10 zokhudza nkhani ya ukwati ndiponso malumbiro, zimagwiranso ntchito pa ukwati wamtunduwu. Chachikulu n’chakuti mwamuna ndi mkaziyo akwatirana m’njira yolemekezeka kwa Mulungu ndiponso kwa anthu.—Luka 20:25; 1 Petro 2:13, 14.
Pitirizani Kukhala ndi Ukwati Wolemekezeka
15, 16. Kodi ulemu uyenera kusonyezedwa motani mu ukwati?
15 M’banja la mfumu ya ku Perisiya mutabuka mavuto, mlangizi wamkulu wa mfumuyo, dzina lake Memukana, anapereka malangizo abwino kwambiri akuti, ‘akazi onse azichitira amuna awo ulemu.’ (Estere 1:20) M’mabanja achikristu, malangizo amenewa sayenera kuchokera kwa mfumu iliyonse yaumunthu monga lamulo ayi. Akazi ayenera kulemekeza amuna awo. N’chimodzimodzinso ndi amuna achikristu, nawonso amalemekeza ndi kuyamikira akazi awo. (Miyambo 31:11, 30; 1 Petro 3:7) M’mabanja mwathu sitiyenera kuyembekezera kuti padutse zaka zambirimbiri tisanayambe kulemekezana. Tiyenera kuyamba kulemekezana tikangokwatirana, patsiku la ukwati lomwelo.
16 Sikuti ndi mwamuna ndi mkazi wake yekhayo amene ayenera kusonyeza ulemu patsiku la ukwati. Ngati mkulu wachikristu adzakambe nkhani ya ukwati, nayonso nkhaniyo iyenera kukambidwa mwaulemu. Pokamba nkhani, azilankhula ndi mwamuna ndiponso mkaziyo. Popeza nkhaniyi imathandizira kupereka ulemu kwa anthu omwe akukwatiranawo, wokambayo sayenera kuikamo nthabwala kapena nthano. Sayenera kufotokozamo kwambiri maganizo ake omwe angachititse manyazi anthu omwe akukwatiranawo kapena anthu omvera. M’malo mwake, ayenera kuyesetsa kulankhula mwaubwenzi ndiponso molimbikitsa, ndipo asonyeze amene anayambitsa ukwati ndiponso malangizo Ake abwino kwambiri. Inde, nkhani yolemekezeka yomwe mkulu angakambe pa ukwati ingathandizire kuti ukwatiwo ukhale wolemekeza Yehova Mulungu.
17. N’chifukwa chiyani Akristu amatsatira malamulo pa ukwati wawo?
17 Mwachidziwikire, m’nkhaniyi mwaphunziramo mfundo zambiri za malamulo a ukwati. N’kutheka kuti mfundo zina sizingagwire ntchito mwachindunji m’dera lanu. Komabe, tonsefe tikufunika kuzindikira kufunika koti dongosolo la ukwati wa Mboni za Yehova lizisonyeza kuti timalemekeza malamulo a m’dziko mwathu, kapena kuti zofuna za Kaisara. (Luka 20:25) Paulo anatilimbikitsa kuti: “Perekani kwa anthu onse mangawa awo; msonkho kwa eni ake a msonkho; kulipira kwa eni ake a kulipidwa; . . . ulemu kwa eni ake a ulemu.” (Aroma 13:7) Inde, n’kofunika kuti Akristu, kungochokera patsiku la ukwati, azilemekeza zimene Mulungu akufuna kuti tizichita.
18. Kodi m’pofunika kuganizira mbali iti ya ukwati imene anthu angasankhe kukhala nayo, ndipo nkhani zokhudza mbali imeneyi tingazipeze kuti?
18 Pambuyo pa ukwati wachikristu pamakhala phwando, kapena kuti madyerero ake. Musaiwale kuti Yesu anapitapo ku phwando loterolo. Ngati pakonzedwa phwando loterolo, kodi uphungu wa m’Baibulo ungatithandize motani kuonetsetsa kuti phwandolo nalonso likhale lolemekeza Mulungu ndiponso losonyeza chitsanzo chabwino cha anthu okwatirana kumenewo ndi pa mpingo wachikristu? Nkhani yotsatirayi ifotokoza zimenezi.e
[Mawu a M’munsi]
a Mawu a Chigiriki omwewo angagwiritsidwenso ntchito kutchula phwando lina lililonse losakhudzana ndi ukwati.—Estere 9:22, Septuagint.
b Mboni za Yehova zimakhala ndi nkhani ya mphindi 30 yakuti “Ukwati Wolemekezeka M’maso mwa Mulungu.” Nkhaniyi imakhala ndi malangizo abwino kwambiri a m’Malemba opezeka m’buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja ndiponso mabuku ena a Mboni za Yehova, ndipo imakhala yothandiza kwambiri anthu omwe akukwatiranawo ndiponso anthu ena onse opezeka pa mwambowo.
c Malumbiro olemekeza Mulungu amene timagwiritsa ntchito, ngati kwanuko kulibe malamulo amene angapangitse kuti malumbirowa asinthidwe, ndi awa. Mkwati amanena kuti: “Ine [dzina la mkwati] ndikukutenga iwe [dzina la mkwatibwi] kukhala mkazi wanga wamtchatho, amene ndidzam’konda ndi kum’samalira, kunthawi yonse imene awirife tidzakhala ndi moyo padziko lapansi, momvera lamulo la Mulungu kwa amuna achikristu, loperekedwa m’Malemba Oyera, molingana ndi makonzedwe a Mulungu a ukwati.” Mkwatibwi amanena kuti: “Ine [dzina la mkwatibwi] ndikukutengani inu a [dzina la mkwati] kukhala mwamuna wanga wamtchatho, amene ndidzam’konda ndi kum’samalira ndi kum’lemekeza kwambiri, kunthawi yonse imene awirife tidzakhala ndi moyo padziko lapansi, momvera lamulo la Mulungu kwa akazi achikristu, loperekedwa m’Malemba Oyera, molingana ndi makonzedwe a Mulungu a ukwati.”
d Nsanja ya Olonda ya November 1, 1962, pamasamba 502 ndi 503, ili ndi mfundo zokhudza ukwati umene umangotengedwa ngati ukwati kumalo ena koma womwe si wovomerezeka mwa malamulo.
e Onaninso nkhani yakuti “Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri,” patsamba 28.
Kodi Mukukumbukira?
• Pankhani ya ukwati, n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mbali yokhudza malamulo a boma ndiponso mbali yauzimu?
• Akristu akamangitsa ukwati wawo ku boma, kodi angasankhe kuchita chiyani mwambo umenewu ukangotha?
• N’chifukwa chiyani nkhani ya ukwati imakambidwira pa Nyumba ya Ufumu?
[Chithunzi patsamba 18]
Kale, paukwati wa Aisrayeli, mkwati ankatenga mkwatibwi n’kupita naye kunyumba kwake kapena kunyumba kwa atate ake
[Chithunzi patsamba 21]
Pambuyo pa ukwati wotsatira mwambo, Akristu angasankhe kukhala ndi nkhani pa Nyumba ya Ufumu