Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Baibulo silinena kalikonse za kumenyanitsa matambula, nangano n’chifukwa chiyani Mboni za Yehova sizichita nawo zimenezi?
Kumenyanitsa matambula amene muli vinyo (kapena chakumwa china choledzeretsa) ndi chizolowezi chakale ndiponso chofala, ngakhale kuti kachitidwe kake kamasiyanasiyana malinga ndi dera lake. Nthawi zina anthu amangokweza m’mwamba matambula awo, osawamenyanitsa. Munthu amene wanena kuti anthu amenyanitse matambula, nthawi zambiri amafunira munthu wina moyo wachimwemwe, thanzi labwino, moyo wautali, ndi zina zotero. Anthu ena amene akuchita nawo zimenezi mwina amanena mawu ovomerezana ndi munthuyo kapena amakweza m’mwamba matambula awo n’kumwako vinyo pang’ono. Anthu ambiri amaona kuti umenewu ndi mwambo wopanda vuto lililonse kapena n’kusonyeza ulemu, koma pali zifukwa zabwino zimene Mboni za Yehova sizimenyanitsira nawo matambula.
Akhristu sachita nawo zimenezi, osati chifukwa choti safunira anzawo moyo wachimwemwe kapena thanzi labwino. Kalata imene bungwe lolamulira la Akhristu oyambirira linalembera mipingo, inatha ndi mawu amene angatanthauze “thanzi labwino,” “tikufunirani zabwino zonse,” kapena “tsalani bwino.” (Machitidwe 15:29) Ndipo olambira oona ena anauza mafumu kuti: “Mbuye wanga . . . akhale ndi moyo nthawi zamuyaya,” kapena “Mfumu ikhale ndi moyo kosatha.”—1 Mafumu 1:31; Nehemiya 2:3.
Koma kodi mwambo womenyanitsa matambula unayamba bwanji? Nsanja ya Olonda yachingelezi ya January 1, 1968, inagwira mawu buku la The Encyclopædia Britannica (la 1910), Voliyumu 13, tsamba 121. Bukuli limati: “Mwambo womwa vinyo pofunira anthu amoyo ‘thanzi labwino’ mwina unachokera ku mwambo wakale wachipembedzo womwa vinyo pofuna kukondweretsa milungu ndi anthu akufa. Agiriki ndi Aroma akamadya chakudya ankathira vinyo pansi monga nsembe kwa milungu yawo, ndipo akamadya pa mwambo wapadera ankamwa vinyo pofuna kukondweretsa milunguyo ndi anthu akufa.” Bukulo linapitiriza kuti: “Mwambo womwa vinyo monga nsembe umenewu, unkagwirizana kwambiri ndi kumwa vinyo pofunira anthu amoyo thanzi labwino.”
Kodi zili chonchobe masiku ano? Buku lakuti International Handbook on Alcohol and Culture la mu 1995, limati: “[Kumenyanitsa matambula] mwina ndi mbali yomwe yatsala ya mwambo wachipembedzo wakale wopereka nsembe kwa milungu pothira pansi magazi kapena vinyo. Pamwambo umenewu ankapereka nsembezi posinthanitsa ndi pempho, kapena pemphero limene ankalinena mwachidule m’mawu awa: ‘Ukhale ndi moyo wautali!’ kapena ‘Ukhale ndi thanzi labwino!’”
N’zoona kuti wolambira woona saona kuti chizolowezi chinachake kapena zinthu zinazake n’zoipa kokha chifukwa choti zinayambira ku zipembedzo zonyenga zakale kapena zimafanana ndi zochitika za m’zipembedzozi. Taganizirani za makangaza. Buku lina lodziwika bwino lofotokoza za m’Baibulo limati: “Zikuoneka kuti makangaza ankagwiritsidwanso ntchito monga chizindikiro chopatulika m’zipembedzo zachikunja.” Komabe, Mulungu ananena kuti makangaza opangidwa ndi nsalu aikidwe mu mpendero wa malaya a mkulu wa ansembe, ndipo nsanamira zamkuwa za kachisi wa Solomo zinakongoletsedwa ndi makangaza. (Eksodo 28:33; 2 Mafumu 25:17) Komanso, mphete ya ukwati panthawi ina inkagwiritsidwa ntchito m’zipembedzo zonyenga. Koma anthu ambiri masiku ano sadziwa zimenezo, ndipo mphete amangoiona ngati umboni woti munthu ali pa banja.
Nanga bwanji kugwiritsira ntchito vinyo pazochitika zachipembedzo? Mwachitsanzo, panthawi ina amuna a ku Sekemu, amene ankalambira Baala analowa “m’nyumba ya mulungu wawo, nadya, namwa, natemberera Abimeleki,” mwana wa Gideoni. (Oweruza 9:22-28) Kodi mukuganiza kuti munthu wokhulupirika kwa Yehova akanamwa nawo vinyo ameneyo, mwina n’kupempha kuti mulungu wonyenga awathandize kuthana ndi Abimeleki? Pofotokoza nthawi imene anthu ambiri mu Isiraeli anapandukira Yehova, Amosi anati anthuwo ankagona pansi “ku maguwa a nsembe alionse, ndi m’nyumba ya Mulungu wawo akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.” (Amosi 2:8) Kodi olambira oona akanachita nawo zimenezo, kaya vinyoyo anathiridwa pansi monga nsembe kwa milunguyo kapena anangomwedwa pa zochitika zimenezo? (Yeremiya 7:18) Kapena kodi wolambira woona angakweze m’mwamba tambula yake ya vinyo n’kupempha kuti mulungu winawake achitire munthu zinazake kapena am’patse tsogolo labwino?
N’zochititsa chidwi kuti nthawi zina, anthu olambira Yehova ankakweza manja awo m’mwamba n’kupempha kuti zinthu ziwayendere bwino. Ankakweza manja awo kwa Mulungu woona. Timawerenga kuti: “Solomo anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova . . . natambasulira manja ake kumwamba, nati, Yehova Mulungu wa Israyeli, palibe Mulungu wolingana ndi inu . . . ndipo mverani inu m’Mwamba mokhala inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.” (1 Mafumu 8:22, 23, 30) Mofanana ndi zimenezi, “Ezara analemekeza Yehova . . . navomereza anthu onse, ndi kuti, Amen, Amen; nakweza manja awo, nawerama, nalambira Yehova.” (Nehemiya 8:6; 1 Timoteyo 2:8) N’zoonekeratu kuti anthu okhulupirika amenewo sanali kukweza manja awo m’mwamba kuti adalitsidwe ndi mulungu winawake wopatsa mwayi.—Yesaya 65:11.
Anthu ambiri amene amamenyanitsa matambula masiku ano mwina saganiza kuti akupempha kuti mulungu winawake awayankhe kapena awadalitse, koma sangafotokozenso chifukwa chimene amakwezera m’mwamba matambula awo a vinyo. Komabe, zilibe kanthu kuti anthuwa saganizira mozama nkhani imeneyi. Akhristu oona sangawatsanzire.
N’zodziwika bwino kuti pankhani zinanso, Mboni za Yehova sizichita nawo zinthu zimene anthu ambiri amachita. Mwachitsanzo anthu ambiri amachita zinthu zolemekeza zizindikiro za dziko, kapena mbendera, ndipo saona kuti kuchita zimenezi n’kulambira. Akhristu oona saletsa anthu ena kuchita zimenezi, koma iwowo sachita nawo. Mboni zambiri zikadziwa nthawi imene zinthu zimenezi zichitike, zimachita zinthu mwanzeru n’cholinga choti zisakhumudwitse anthu ena. Mulimonse mmene zingakhalire, sizifuna kuchita nawo zinthu zosonyeza kukonda dziko lawo mopitirira muyeso, chifukwa n’zosemphana ndi zimene Baibulo limanena. (Eksodo 20:4, 5; 1 Yohane 5:21) Masiku ano, anthu ambiri mwina saona kuti kumenyanitsa matambula n’kokhudzana ndi kupembedza. Komabe, pali zifukwa zomveka zimene Akhristu amapewera kumenyanitsa matambula. Kunachokera ku zipembedzo zonyenga ndipo ngakhale masiku ano kumaonedwa ngati kupempha winawake amene ali kumwamba kuti atidalitse, kapena kupempha winawake wa mphamvu zoposa zathu kuti atithandize.—Eksodo 23:2.