Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lv mutu 13 tsamba 144-159
  • Zikondwerero Zimene Mulungu Amadana Nazo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zikondwerero Zimene Mulungu Amadana Nazo
  • Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KHIRISIMASI UNALI MWAMBO WOLAMBIRA DZUWA
  • KODI BAIBULO LIMATI CHIYANI PA NKHANI YOKUMBUKIRA TSIKU LOBADWA?
  • ISITALA
  • PHWANDO LAUKWATI WANU LIKHALE LOLEMEKEZA MULUNGU
  • KODI MWAMBO WOWOMBANITSA MATAMBULA NDI WACHIPEMBEDZO?
  • “INU OKONDA YEHOVA, DANANI NACHO CHOIPA”
  • MUZILEMEKEZA MULUNGU M’MAWU NDI ZOCHITA ZANU
  • Kodi Mulungu Amasangalala Ndi Zikondwerero Zonse?
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Khalani ndi Cholinga Choti Muzilambira Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Yesetsani Kuti Muzilambira Mulungu M’njira Yovomerezeka
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Vuto la Kusiyanasiyana kwa Zipembedzo
    Mboni za Yehova ndi Maphunziro
Onani Zambiri
Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
lv mutu 13 tsamba 144-159
Mwana akumasula mphatso imene makolo ake amupatsa

MUTU 13

Zikondwerero Zimene Mulungu Amadana Nazo

“Nthawi zonse muzitsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.”—AEFESO 5:10.

1. Kodi Yehova amakokera kwa iye anthu otani, nanga n’chifukwa chiyani anthuwa ayenera kukhala maso?

YESU anati: “Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23) Yehova akapeza anthu amene amafuna kumulambira ndi mzimu ndi choonadi, ngati mmene anakupezerani inuyo, amawakokera kwa iye ndi kwa Mwana wake. (Yohane 6:44) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri. Komabe, popeza Satana ndi katswiri wa chinyengo, anthu amene amakonda choonadi cha m’Baibulo ‘nthawi zonse ayenera kutsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.’—Aefeso 5:10; Chivumbulutso 12:9.

2. Fotokozani mmene Yehova amaonera anthu amene amaphatikiza kulambira koona ndi konyenga.

2 Taganizirani zimene zinachitika pafupi ndi phiri la Sinai, pamene Aisiraeli anapempha Aroni kuti awapangire mulungu. Aroni anavomera ndipo anapanga fano la mwana wa ng’ombe n’kuwauza kuti likuimira Yehova. Iye anati: “Mawa kuli chikondwerero cha Yehova.” Zimene anachitazi kunali kuphatikiza kulambira koona ndi konyenga. Ndiye kodi Yehova anasangalala nazo? Ayi, chifukwa iye anapha anthu pafupifupi 3,000 amene analambira fano limeneli. (Ekisodo 32:1-6, 10, 28) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Ngati tikufuna kuti Mulungu apitirize kutikonda, tiyenera kupewa kukhudza “chinthu chilichonse chodetsedwa” ndipo tiziyesetsa kuteteza choonadi kuti chisakhale chodetsedwa.—Yesaya 52:11; Ezekieli 44:23; Agalatiya 5:9.

3, 4. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mofatsa mfundo za m’Baibulo tisanachite nawo miyambo kapena zikondwerero zilizonse zotchuka?

3 Atumwi ankaletsa Akhristu oyambirira kutengera ziphunzitso za ampatuko. Koma n’zomvetsa chisoni kuti iwo atafa, ena amene ankati ndi Akhristu ngakhale kuti sankakonda choonadi, anayamba kutengera miyambo, zikondwerero ndiponso maholide achikunja, ndipo ankati zimenezi zinali zovomerezeka kwa Akhristu. (2 Atesalonika 2:7, 10) Tikambirana zina mwa zikondwerero zimenezi ndipo tiona mmene zikusonyezera mzimu wa dziko, osati wa Mulungu. Kunena mwachidule, zikondwerero za dzikoli zimafanana pa mfundo zotsatirazi: Zimalimbikitsa anthu kutsatira zilakolako za thupi, zimalimbikitsa zikhulupiriro za chipembedzo chonyenga ndi kukhulupirira mizimu. Zinthu zimenezi ndi zizindikiro za “Babulo Wamkulu.”a (Chivumbulutso 18:2-4, 23) Muyenera kukumbukiranso kuti zikondwerero ndi miyambo yambiri yotchuka masiku ano zinachokera ku miyambo ya chipembedzo chonyenga imene Yehova ankanyansidwa nayo. N’zoonekeratu kuti iye amanyansidwabe ndi zikondwerero zangati zimenezi zomwe zimachitika masiku ano. Ifenso tiyenera kunyansidwa ndi zikondwerero zoterezi.—2 Yohane 6, 7.

4 Monga Akhristu oona, timadziwa kuti pali zikondwerero zina zimene Yehova amadana nazo. Koma m’pofunika kutsimikiza mtima kuti tisamachite nawo ngakhale pang’ono zikondwerero zimenezi. Tikambirana chifukwa chake Yehova amadana ndi zikondwerero ngati zimenezi. Ndipo kudziwa zimenezi kungatilimbikitse kutsimikiza mtima kupewa chilichonse chimene chingatilepheretse kuti Mulungu apitirize kutikonda.

KHIRISIMASI UNALI MWAMBO WOLAMBIRA DZUWA

5. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu sanabadwe pa 25 December?

5 Baibulo silinena kuti anthu ankakondwerera tsiku limene Yesu anabadwa. Ndipotu tsiku lenileni limene Yesu anabadwa silikudziwika. Komabe, pali umboni wakuti Yesu sanabadwe pa 25 December. Kumene Yesu anabadwira, nthawi imeneyi kumakhala mvula ndiponso kumazizira kwambiri.b Tikudziwa zimenezi chifukwa Luka analemba kuti Yesu anabadwa ‘abusa akugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo.’ (Luka 2:8-11) Luka sakanalemba mfundo imeneyi zikanakhala kuti abusa ankachita zimenezi chaka chonse. M’mwezi wa December, ku Betelehemu kumakhala kukugwa mvula ndi chipale chofewa, choncho ziweto ziyenera kuti zinkakhala m’makola ndipo sizikanatheka kuti abusa ‘azigonera kubusa.’ Chinanso n’chakuti, Yosefe ndi Mariya anapita ku Betelehemu chifukwa Kaisara Augusito analamula kuti kukhale kalembera. (Luka 2:1-7) N’zokayikitsa kwambiri kuti Kaisarayu akanalamula anthu amene ankadana ndi ulamuliro wa Roma kupita kumizinda yakwawo m’nyengo ya mvula komanso yozizira kwambiri imeneyi.

6, 7. (a) Kodi zochitika zambiri za pa Khirisimasi zinachokera kuti? (b) Kodi mphatso za pa Khirisimasi zimasiyana bwanji ndi mphatso zimene Akhristu amapatsana?

6 Chikondwerero cha Khirisimasi sichinachokere m’Malemba koma chinachokera ku zikondwerero zachikunja za anthu akale, monga chikondwerero cha ku Roma chotchedwa Saturnalia, chimene chinali chokhudza kulambira mulungu wa zaulimi wotchedwa Saturn. Komanso buku lina lachikatolika linanena kuti, anthu olambira mulungu wotchedwa Mithra, pa 25 December ankachita chikondwerero “chokumbukira kubadwa kwa dzuwa lomwe ankati n’losagonjetseka. Khirisimasi inayamba nthawi imene kulambira dzuwa kunali pachimake ku Roma.” Apa n’kuti patatha zaka pafupifupi 300 kuchokera pamene Khristu anafa.—New Catholic Encyclopedia.

Akhristu oona amapereka mphatso chifukwa cha chikondi

7 Panyengo ya zikondwerero zachikunja zimenezi, anthu ankakhala ndi maphwando ndiponso ankapatsana mphatso. Zimenezi n’zimenenso zimachitika pa Khirisimasi masiku ano. Ndiponso mofanana ndi masiku ano, mphatso zambiri za pa Khirisimasi nthawi imeneyo, sizinkaperekedwa mogwirizana ndi mfundo ya pa 2 Akorinto 9:7. Lemba limeneli limati: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” Akhristu oona amapatsana mphatso chifukwa cha chikondi ndipo sachita kusankha tsiku linalake loti azichitira zimenezi. Komanso sayembekezera kuti munthu amene am’patsa mphatsoyo nayenso awapatse mphatso. (Luka 14:12-14; werengani Machitidwe 20:35.) Komanso, chifukwa chakuti sachita nawo Khirisimasi sakhala ndi nkhawa zimene anthu ambiri amakhala nazo pokonzekera Khirisimasi ndiponso sawononga ndalama.—Mateyu 11:28-30; Yohane 8:32.

8. Kodi okhulupirira nyenyezi anam’patsa Yesu mphatso pokondwerera kubadwa kwake? Fotokozani.

8 Kodi okhulupirira nyenyezi anam’patsa Yesu mphatso pokondwerera kubadwa kwake? Ayi. Mphatso zimene anapereka zinali zongosonyeza ulemu kwa munthu wofunika kwambiri ameneyu. Ndipo umenewu unali mwambo wotchuka pa nthawiyo. (1 Mafumu 10:1, 2, 10, 13; Mateyu 2:2, 11) Ndipotu, sanapereke mphatsozi pa tsiku limene Yesu anabadwa. Nthawi imene okhulupirira nyenyezi anafika ndi mphatsozi, Yesu sanali wakhanda koma anali atatha miyezi yambiri ndipo ankakhala m’nyumba, osati modyera ng’ombe.

KODI NDIZICHITA NAWO ZIKONDWEREROZI?

Mzimayi wachikhristu akukana kuika maluwa mu ofesi yake pachikondwerero chinachake chotchuka

Mfundo Yofunika Kuiganizira: “‘Tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova. ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’” “‘ndipo ndidzakulandirani.’”—2 Akorinto 6:17.

Musanachite nawo mwambo kapena chikondwerero chinachake, dzifunseni mafunso awa:

  • Kodi chikondwerero kapena mwambo umenewu unachokera ku ziphunzitso kapena miyambo ya chipembedzo chonyenga ndi kukhulupirira mizimu?—Yesaya 52:11; 1 Akorinto 4:6; 2 Akorinto 6:14-18; Chivumbulutso 18:4.

  • Kodi cholinga chake ndi kupereka ulemu kapena kutamanda munthu winawake, bungwe kapena zizindikiro zinazake zoimira dziko?—Yeremiya 17:5-7; Machitidwe 10:25, 26; 1 Yohane 5:21.

  • Kodi zochitika za pazikondwererozi zimasonyeza kuti fuko kapena mtundu wina ndi woposa unzake?—Machitidwe 10:34, 35; 17:26.

  • Kodi chikondwerero kapena mwambo umenewu umasonyeza “mzimu wa dziko,” umene umachita zinthu zosiyana ndi mzimu woyera wa Mulungu?—1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2.

  • Kodi ndingakhumudwitse anthu ena ngati nditachita nawo chikondwerero kapena mwambo umenewu?—Aroma 14:21.

  • Ngati ndasankha kusachita nawo chikondwerero kapena mwambo umenewu, kodi ndingafotokoze bwanji mwaulemu chifukwa chimene sindikuchitira nawo zimenezo?—Aroma 12:1, 2; Akolose 4:6.

Malemba otsatirawa angakuthandizeni kuyankha mafunso okhudza zikondwerero zosiyanasiyana:

  • “[Aisiraeli osakhulupirika] anayamba kusakanikirana ndi mitundu ina, ndi kuyamba kuphunzira zochita zawo.”—Salimo 106:35.

  • “Munthu wokhulupirika pa chinthu chaching’ono alinso wokhulupirika pa chinthu chachikulu, ndipo munthu wosalungama pa chinthu chaching’ono alinso wosalungama pa chinthu chachikulu.”—Luka 16:10.

  • “Simuli mbali ya dzikoli.”—Yohane 15:19.

  • “Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.”—1 Akorinto 10:21.

  • “Nthawi imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”—1 Petulo 4:3.

KODI BAIBULO LIMATI CHIYANI PA NKHANI YOKUMBUKIRA TSIKU LOBADWA?

9. Kodi n’chiyani chinachitika pa zikondwerero zokumbukira tsiku lobadwa zimene zinatchulidwa m’Baibulo?

9 Ngakhale kuti nthawi zonse anthu amasangalala mwana akabadwa, Baibulo silinena kuti pali mtumiki wa Mulungu aliyense amene anakondwererapo tsiku lake lobadwa. (Salimo 127:3) Kodi zinangochitika mwangozi kuti olemba Baibulo asalembe zimenezi? Ayi. Tikutero chifukwa Baibulo limatchula zikondwerero ziwiri zokumbukira tsiku lobadwa. Chikondwerero cha Farao wa ku Iguputo ndi cha Herode Antipa. (Werengani Genesis 40:20-22; Maliko 6:21-29.) Komabe, Baibulo limasonyeza kuti zikondwerero zonsezi zinali zoipa. Makamaka cha Herode Antipa amene anadula mutu wa Yohane M’batizi pa chikondwererochi.

10, 11. Kodi Akhristu oyambirira ankaiona bwanji nkhani yokondwerera tsiku lobadwa, ndipo n’chifukwa chiyani?

10 Buku lina linati Akhristu oyambirira, “ankakhulupirira kuti mwambo wokondwerera tsiku lobadwa ndi wachikunja.” (The World Book Encyclopedia) Mwachitsanzo, anthu akale a ku Girisi ankakhulupirira kuti munthu aliyense akamabadwa, pamafika mzimu winawake umene umateteza munthuyo pa moyo wake wonse. Buku lina linatinso anthu a ku Girisi, ankakhulupirira kuti mzimu umenewu “umakhala pa ubale winawake ndi mulungu amene anabadwa pa tsiku limene munthuyo wabadwa.” Kuyambira kale, kukondwerera tsiku lobadwa kumagwirizana kwambiri ndi kukhulupirira nyenyezi.—The Lore of Birthdays.

KODI KUKONDWERERA TSIKU LOBADWA N’KOGWIRIZANA BWANJI NDI KULAMBIRA SATANA?

N’zochititsa chidwi kudziwa kuti tsiku lofunika kwambiri kwa anthu a chipembedzo cholambira Satana ndi tsiku lobadwa. Chifukwa chiyani amaona choncho? Chifukwa amakhulupirira kuti munthu aliyense angakhale mulungu ngati akufuna. Choncho, poti iwo amadziona ngati mulungu, akamakondwerera tsiku lawo lobadwa amaona ngati akukondwerera kubadwa kwa mulungu. N’zoona kuti anthu ambiri amene amakondwerera tsiku lawo lobadwa samadziona kukhala ofunika kwambiri kufika pamenepa. Komabe, buku lofotokoza mbiri ya chikondwerero cha tsiku lobadwa linati: “Maholide ena amasangalatsa, koma chikondwerero cha tsiku lobadwa chimapangitsa munthu kudziona kukhala wofunika kwambiri kuposa anthu ena onse.”—The Lore of Birthdays.

11 Atumiki a Mulungu akale sankakondwerera masiku obadwa chifukwa ankadziwa kuti zimenezi zinachokera kwa okhulupirira mizimu ndi anthu ena achikunja. Komanso, iwo ayenera kuti sankachita nawo zikondwerero zimenezi chifukwa chakuti ankayendera mfundo za Mulungu. N’chifukwa chiyani tikutero? Anthu amenewa anali odzichepetsa ndipo ankaona kuti kubadwa kwawo sichinali chinthu chofunika kwambiri choti n’kukondwerera.c (Mika 6:8; Luka 9:48) M’malomwake, iwo ankalemekeza Yehova ndipo ankamuthokoza chifukwa chowapatsa mphatso yamtengo wapatali ya moyo.d—Salimo 8:3, 4; 36:9; Chivumbulutso 4:11.

12. Kodi tsiku lomwalira limaposa bwanji tsiku lobadwa?

12 Anthu onse okhulupirika kwa Mulungu akamwalira adzaukitsidwa chifukwa Mulungu amawakumbukira. (Yobu 14:14, 15) Lemba la Mlaliki 7:1 limati: “Mbiri yabwino imaposa mafuta onunkhira, ndipo tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa.” “Mbiri yabwino” imeneyi ndi imene timapanga chifukwa chotumikira Mulungu mokhulupirika. Chochititsa chidwi n’chakuti mwambo umene Akhristu analamuliridwa kuti azichita ndi wokumbukira imfa ya Yesu, amene “dzina” lake lapamwamba kwambiri, n’lofunika kuti tidzapulumuke. Koma Akhristu sanalamulidwe kuti azikumbukira kubadwa kwake.—Aheberi 1:3, 4; Luka 22:17-20.

ISITALA

13, 14. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu oona sachita nawo mwambo wa Isitala?

13 Isitala ndi mwambo umene matchalitchi Achikristu amachita pokumbukira kuuka kwa Khristu. Koma kodi Khristu analamula anthu kuti azikumbukira kuuka kwake? Ayi. Mabuku a mbiri yakale amanena kuti Akhristu oyambirira sankachita nawo Isitala. Komanso ankakhulupirira kuti mwambowu ndi wachikunja. Buku lina limanena kuti: “M’Chipangano Chatsopano mulibe lemba lililonse losonyeza kuti anthu ankakondwerera Isitala. . . . Panalibe nthawi inayake yapadera imene Akhristu oyambirira ankaiona kuti inali yopatulika.”—Encyclopœdia Britannica.

14 Monga taonera, mwambo wa Isitala unachokera ku chikunja. Ndiye kodi mukuganiza kuti Yehova angavomereze kuti anthu azichita mwambo wachikunja umenewu ponamizira kuti akukumbukira kuuka kwa Mwana wake? Ayi, sangavomereze. (2 Akorinto 6:17, 18) Ndipotu m’Malemba mulibe lamulo lonena kuti anthu azikumbukira kuuka kwa Yesu. Anthu amene amachita Isitala n’kumati akukumbukira kuuka kwa Yesu amakhumudwitsa kwambiri Mulungu.

PHWANDO LAUKWATI WANU LIKHALE LOLEMEKEZA MULUNGU

15, 16. (a) N’chifukwa chiyani Akhristu amene akufuna kulowa m’banja ayenera kufufuza ngati miyambo yaukwati ya kwawo ili yogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo? (b) Kodi Akhristu ayenera kuganizira chiyani pa nkhani ya miyambo yaukwati monga kuwaza mpunga kapena zinthu zina?

15 Mawu a Mulungu amati posachedwapa “mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso [m’Babulo Wamkulu].” (Chivumbulutso 18:23) Chifukwa chiyani amatero? Chifukwa cha zochita zake zamizimu zimene zingaipitse banja kuyambira pa tsiku laphwando la ukwati.—Maliko 10:6-9.

16 Padziko lonse, anthu amatsatira miyambo yosiyanasiyana yaukwati. Komatu miyambo ina imene imaoneka ngati yabwinobwino, iyenera kuti inachokera ku miyambo ya ku Babulo. Miyambo imeneyi cholinga chake amati n’kubweretsa ‘mwayi’ kwa akwati ndi anthu obwera paphwando la ukwati. (Yesaya 65:11) Mwambo umodzi woterewu ndi wowaza mpunga kapena zinthu zina. Mwambo umenewu uyenera kuti unachokera pa chikhulupiriro chakuti chakudya chimasangalatsa mizimu ndipo chimapangitsanso kuti isavulaze akwati. Komanso, kwa nthawi yaitali anthu akhala akukhulupirira kuti mpunga uli ndi mphamvu zothandiza anthu kubereka, kukhala osangalala komanso kukhala ndi moyo wautali. N’chifukwa chaketu aliyense amene akufuna kuti Mulungu apitirize kumukonda, ayenera kupewa miyambo yodetsa ngati imeneyi.—Werengani 2 Akorinto 6:14-18.

17. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene mwamuna ndi mkazi amene akufuna kuchita ukwati komanso anthu oitanidwa ayenera kutsatira?

17 Atumiki a Yehova amapewanso miyambo ina imene ingapangitse kuti nkhani ndi phwando la ukwati wawo zikhale ngati zachikunja kapenanso miyambo imene ingakhumudwitse ena. Mwachitsanzo, Akhristu akapemphedwa kulankhula paukwati, amapewa kulankhula mawu onyoza, olaula komanso nthabwala zimene zingachititse manyazi akwati ndiponso anthu ena. (Miyambo 26:18, 19; Luka 6:31; 10:27) Amapewanso kuchita maphwando aukwati odzionetsera kwambiri amene sasonyeza kudzichepetsa koma amangosonyeza “kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.” (1 Yohane 2:16) Ngati mukufuna kuchita ukwati musaiwale kuti Yehova amafuna kuti tsiku laukwati wanu lidzakhale lapadera kwambiri, loti mukamalikumbukira muzidzasangalala osati kunong’oneza bondo.e

KODI MWAMBO WOWOMBANITSA MATAMBULA NDI WACHIPEMBEDZO?

18, 19. Kodi buku lina limanena kuti mwambo wowombanitsa matambula unayamba bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani mwambo umenewu uli wosaloledwa kwa Akhristu?

18 Mwambo wotchuka umene umachitika pa maukwati kapena pa zikondwerero zina ndi wowombanitsa mabotolo kapena matambula. Buku lina limene linalembedwa m’chaka cha 1995 linati: “Zikuoneka kuti mwambo wowombanitsa matambula . . . ndi mwambo umodzi wachikunja umene watsala pa miyambo yakale imene inkatsatiridwa popereka nsembe kwa milungu. Nsembe zimenezi zinali magazi kapena vinyo . . . ankapereka nsembezi pofuna kudalitsidwa. Popempha madalitsowo iwo ankapemphera mwachidule kuti ‘mukhale ndi moyo wautali’ kapena ‘mukhale ndi thanzi labwino.’”—International Handbook on Alcohol and Culture.

19 N’zoona kuti anthu ambiri sadziwa kuti kuwombanitsa mabotolo kapena matambula ndi mwambo wa chipembedzo chonyenga kapena mwambo wosonyeza kukhulupirira mizimu. Mwambo wokweza m’mwamba matambula a vinyo umatanthauza kupempha madalitso “kumwamba” kapena kuti kwa mizimu. Koma zimenezi si zogwirizana ndi zimene Malemba amanena.—Yohane 14:6; 16:23.f

“INU OKONDA YEHOVA, DANANI NACHO CHOIPA”

20. Kodi Akhristu ayenera kupewa zikondwerero zofala ziti ngakhale zitakhala zosakhudzana ndi chipembedzo chonyenga, ndipo n’chifukwa chiyani ayenera kutero?

20 Masiku ano, makhalidwe abwino alowa pansi kwambiri. Babulo Wamkulu ndi amene akuchititsa zimenezi. Ndipo chifukwa cha zimenezi, mayiko ena akhazikitsa maphwando osiyanasiyana kumene anthu amavina monyanyira ndipo nthawi zina maphwandowa amakhala olimbikitsa khalidwe logonana pakati pa amuna kapena akazi okhaokha. Kodi n’zoyenera kuti munthu ‘wokonda Yehova’ azipezeka kapena kuonerera maphwando amenewa? Kodi kuchita zimenezi kungasonyeze kuti iye amadanadi ndi zoipa? (Salimo 1:1, 2; 97:10) Ndi bwino kutengera maganizo a wamasalimo amene anapemphera kuti: “Chititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”—Salimo 119:37.

21. Kodi ndi zikondwerero zotani zimene Mkhristu ayenera kusankha yekha kuchita kapena kusachita nawo?

21 Pa nthawi ya zikondwerero zadziko, Mkhristu ayenera kusamala kuti asachite chilichonse chimene chingasonyeze kuti akuchita nawo. Paulo analemba kuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31; onani bokosi lakuti, “Kusankha Zinthu Mwanzeru.”) Komabe, ngati mwambo kapena chikondwerero chinachake si chogwirizana ndi miyambo ya chipembedzo chonyenga, si chokhudza ndale kapena si chosonyeza kukonda kwambiri dziko lako, ndipo si chotsutsana ndi mfundo za m’Baibulo, Mkhristu aliyense angasankhe yekha kuchita kapena kusachita nawo. Iye ayeneranso kuganizira mmene ena amaonera mwambo kapena chikondwerero chimenechi posafuna kuwakhumudwitsa.

MUZILEMEKEZA MULUNGU M’MAWU NDI ZOCHITA ZANU

22, 23. Kodi tingatani kuti tizifotokozera anthu malamulo olungama a Yehova mogwira mtima?

22 Anthu ambiri amaona kuti masiku a zikondwerero zotchuka amawapatsa mpata wocheza ndi mabanja komanso anzawo. Choncho ngati wina chifukwa chosatimvetsa, atanena kuti zimene timakhulupirira pa nkhani imeneyi sizisonyeza chikondi komanso n’zonyanyira, tingamufotokozere mwaulemu kuti Mboni za Yehova zimadziwa kuti kucheza ndi banja komanso mabwenzi n’kofunika. (Miyambo 11:25; Mlaliki 3:12, 13; 2 Akorinto 9:7) Chaka chonse timacheza ndi anthu amene timawakonda. Koma chifukwa chakuti timakonda Mulungu ndiponso malamulo ake olungama, sitimafuna kuti miyambo imene Mulungu amadana nayo iwononge kucheza kwathuko.—Onani bokosi lakuti, “Kulambira Koona Kumasangalatsa Kwambiri.”

23 Mboni zina zathandizapo anthu amene amafunadi kudziwa zenizeni pa nkhaniyi, pogwiritsa ntchito mfundo za m’Mutu 16 wa buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?g Komabe, kumbukirani kuti cholinga chathu si kugonjetsa anthu ndi mfundo zathu ayi, koma timafuna kuti anthuwo ayambe kulambira koona. Choncho, muyenera kukhala aulemu, oleza mtima ndiponso “nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere.”—Akolose 4:6.

24, 25. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kulimbitsa chikhulupiriro chawo ndi kukonda kwambiri Yehova?

24 Monga atumiki a Yehova timaphunzitsidwa bwino kwambiri. Timadziwa chifukwa chimene timakhulupirira ndi kuchita zinthu zina komanso chifukwa chimene sitichitira zinthu zina. (Aheberi 5:14) Choncho, makolo muziphunzitsa ana anu kuti azigwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Mukamachita zimenezi ndiye kuti mukulimbitsa chikhulupiriro chawo, mukuwathandiza kuti anthu akawafunsa za chikhulupiriro chawo aziyankha kuchokera m’Malemba, komanso mukuwathandiza kumvetsa kuti Yehova amawakonda.—Yesaya 48:17, 18; 1 Petulo 3:15.

25 Anthu onse amene amalambira Mulungu “ndi mzimu ndi choonadi” amapewa zikondwerero zosagwirizana ndi Malemba. (Yohane 4:23) Komanso amayesetsa kukhala okhulupirika m’zochita zawo zonse. Masiku ano, anthu amaona kuti kukhala okhulupirika n’kosathandiza. Koma monga mmene tionere m’mutu wotsatira, zonse zimene Mulungu amafuna kuti tizichita zimakhala zothandiza nthawi zonse.

a Onani bokosi lakuti, “Kodi Ndizichita Nawo Zikondwererozi?” Kuti mudziwe nkhani zina zofotokoza zikondwerero ndi maholide osakondweretsa Mulungu, onani m’buku la Watch Tower Publications Index, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

b Baibulo komanso mabuku a mbiri yakale amasonyeza kuti Yesu ayenera kuti anabadwa mu 2 B.C.E., m’mwezi wa Etanimu pa kalendala yachiyuda. Pa kalendala yathu mwezi umenewo ndi mwezi wa September kapena October. Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, patsamba 56 ndi 57, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

c Onani bokosi lakuti, “Kodi Kukondwerera Tsiku Lobadwa N’kogwirizana Bwanji ndi Kulambira Satana?”

d Pangano la Chilamulo linanena kuti mkazi akabereka mwana azipereka nsembe ya machimo kwa Mulungu. (Levitiko 12:1-8) Lamulo limeneli linkawakumbutsa Aisiraeli kuti makolo amapatsira ana awo uchimo, komanso kuti aziona kubadwa kwa mwana moyenerera, ndipo liyenera kuti linawathandiza kupewa kutengera miyambo yachikunja yokhudza masiku obadwa.—Salimo 51:5.

e Onani nkhani zitatu zofotokoza za ukwati ndi maphwando mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2006, patsamba 18 mpaka 31.

f Onani Nsanja ya Olonda ya February 15, 2007, patsamba 30 ndi 31.

g Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

KULAMBIRA KOONA KUMASANGALATSA KWAMBIRI

Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe” ndipo amafuna kuti atumiki ake azisangalala. (1 Timoteyo 1:11) Malemba otsatirawa akusonyeza mfundo imeneyi:

  • “Munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.”—Miyambo 15:15.

  • “Ndazindikira kuti palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso azichita zabwino pamene ali ndi moyo, komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.”—Mlaliki 3:12, 13.

  • “Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto, ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.”—Miyambo 11:25.

  • “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”—Mateyu 11:28, 30.

  • “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:32.

  • “Aliyense [apereke] mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”—2 Akorinto 9:7.

  • “Makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa ndiwo chikondi, chimwemwe, mtendere, . . . kukoma mtima, ubwino.”—Agalatiya 5:22.

  • “Zipatso za kuwala ndizo chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama ndi choona.”—Aefeso 5:9.

KUSANKHA ZINTHU MWANZERU

Nthawi zina tingafunike kusonyeza kuti timakondadi Yehova ndiponso kuti timamvetsa mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, mwamuna kapena mkazi wanu wosakhulupirira angakupempheni kuti mukadye chakudya limodzi ndi achibale ake patsiku la holide inayake. Malinga ndi chikumbumtima chawo, Akhristu ena angalole kupita koma ena angakane. Ngati Mkhristu walola kupita, zochita zake ziyenera kusonyezeratu kuti sakukondwerera nawo holideyo ndiponso kuti wangopita kukacheza ndi kukadya limodzi ndi achibale ake basi.

Mkhristu amene wasankha kuchita zimenezi, angachite bwino kukambirana mwaulemu ndi mwamuna kapena mkazi wake asanapite kwa achibale akewo. Iwo angakambirane kuti adziwe ngati achibalewo angakhumudwe Mkhristuyo atakana kuchita nawo zinthu zokhudza holideyo zimene achibalewo angachite. Mwina zimenezi zingachititse mwamuna kapena mkazi wosakhulupirirayo kusintha tsiku lokacheza kwa achibalewo.—1 Petulo 3:15.

Pambuyo pofotokoza maganizo ake, kodi mkazi wachikhristu angatani ngati mwamuna wake akumukakamizabe kuti apite naye kochezako? Pali mfundo zingapo zimene angaziganizire. Mwachitsanzo, iye angaone kuti mwamunayo, monga mutu wa banja, ali ndi udindo wopezera chakudya banjalo. (Akolose 3:18) Ndipo patsiku la holideli akukwaniritsa udindo wakewu pomutengera iyeyo kukadya kwa abale ake. Ndipo mwina mkaziyo angathe kukhala ndi mwayi wolalikira achibalewo pa nthawiyo. Chakudyacho si chodetsedwa chifukwa chakuti chikudyedwa patsiku la holide. (1 Akorinto 8:8) Mkhristuyo, angaone kuti akudya chakudyacho monga amachitira masiku onse ndipo sayenera kuchita nawo zinthu monga kupereka mafuno abwino okhudzana ndi holideyo, kuimba nawo nyimbo, kuwombanitsa mabotolo kapena matambula ndiponso kuchita nawo zinthu zina zokhudzana ndi holideyo.

Muyeneranso kuganizira mmene kupita ku phwando limeneli kungakhudzire anthu ena. Mkazi wachikhristu afunika kuganizira ngati anthu ena angakhumudwe atadziwa zoti patsikuli iye wapita kwa achibale ake osakhulupirira.—1 Akorinto 8:9; 10:23, 24.

Komanso, ayenera kuganizira ngati achibale ake osakhulupirirawo angakamukakamize kuchita zinthu zosiyana ndi zimene amakhulupirira. M’posavuta kuti munthu agonje chifukwa cha mtima wofuna kusakhumudwitsa anthu ena. Choncho, ndi bwino kuganizira nkhaniyi mofatsa musanapite kwa achibalewo. Mkhristu ayenera kuganizira mfundo zonsezi komanso ayenera kuganizira ngati kupita kumeneko kungawononge chikumbumtima chake.—Machitidwe 24:16.

Kodi Ndiyenera Kulandira Bonasi pa Khirisimasi?

Panyengo ya Khirisimasi, bwana angapereke mphatso kapena bonasi kwa antchito ake. Kodi Mkhristu ayenera kukana mphatso zimenezi? Ayi, angathe kulandira. N’kutheka kuti bwanayo sakuganiza kuti aliyense wolandira bonasiyo ndiye kuti akukondwerera Khirisimasi. Mwina bwanayo akungofuna kugawira antchito akewo ndalama zowonjezereka zimene kampaniyo yapeza. Kapenanso bwanayo angapereke bonasiyo poyamikira ntchito imene anthuwo agwira chaka chonsecho ndiponso kuwalimbikitsa pantchito yawo. Bwanayo angapereke mphatsozo kwa antchito ake onse, kaya ndi Asilamu, Ayuda kapenanso achipembedzo china chilichonse, mosatengera kuti amakondwerera Khirisimasi kapena ayi. Choncho, sikuti wa Mboni za Yehova ayenera kukana mphatsoyo chifukwa chakuti yaperekedwa pa nthawi ya Khirisimasi kapena m’dzina la chikondwerero chinachake.

Ngakhale mphatso itaperekedwa pa holide ya chipembedzo, sizikutanthauza kuti aliyense amene walandira mphatsoyo akugwirizana ndi zimene chipembedzocho chimakhulupirira. Mwina mnzanu wakuntchito kapena wachibale wanu angakuuzeni kuti, “Ndikudziwa kuti simumakondwerera nawo chikondwererochi, komabe ndikufuna kuti ndikupatseni mphatsoyi.” Ngati mukuona kuti chikumbumtima chanu sichikuvutitsani, mungalandire ndi kuthokoza popanda kutchula china chilichonse chokhudzana ndi chikondwererocho. (Machitidwe 23:1) Koma mungathe kudzamufotokozera mosamala munthuyo zimene mumakhulupirira nthawi ina imene mukuona kuti munthuyo sangakhumudwe.

Komabe, bwanji ngati wopereka mphatsoyo akupereka ndi cholinga chofuna kumuyesa Mkhristuyo kuti aone ngati ali wolimba pa chikhulupiriro chake kapena ngati angachite zosiyana ndi zimene amakhulupirira chifukwa cha dyera? Apa, Mkhristu angachite bwino kwambiri kukana mphatsoyo. Tisaiwale kuti timafuna kumatumikira Yehova Mulungu ndi mtima wathu wonse.—Mateyu 4:8-10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena