Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w07 8/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Davide ndi Sauli
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Chifukwa chake Davide Akuthawa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Zimene Zili Mʼbuku la 1 Samueli
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • “Kumvera Kuposa Nsembe”
    Nsanja ya Olonda—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2007
w07 8/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Davide atapha Goliati, Mfumu Sauli anamufunsa kuti, “Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani?” N’chifukwa chiyani Sauli anafunsa funso limeneli pamene m’mbuyomo anaitanitsa Davide kuti azikamutumikira?​—1 Samueli 16:22; 17:58.

Yankho lachidule lingakhale lakuti mwina Sauli anaiwala kuti Davide anali ndani chifukwa chakuti poyambapo anangoonana kwa nthawi yochepa. Komabe zimenezi n’zokayikitsa, chifukwa nkhani imene ili pa 1 Samueli 16:18-23 imasonyeza kuti Mfumu Sauli anachita kuitanitsa Davide mwapadera ndipo anamukonda kwambiri moti anamuika kukhala wonyamula zida zake. Sauli ayenera kuti ankamudziwa bwino Davide.

Akatswiri ena a Baibulo amati 1 Samueli 17:12-31 ndi 1 Samueli 17:55–18:5 anawonjezeredwa pambuyo pake chifukwa mavesi amenewa sapezeka m’Mabaibulo ena a Septuagint ya Chigiriki, lomwe ndi Baibulo la Malemba Achiheberi lomasuliridwa m’zaka za ma 100 B.C.E. Komabe si nzeru kuganiza choncho mwa kungoona zimene zili mu Septuagint zokha, chifukwa mavesi amenewa amapezeka m’malemba apamanja ena odalirika a Malemba Achiheberi.a

Popeza kuti Sauli anayamba wafunsa Abineri kenako Davide mwini wakeyo, ndiye n’zachionekere kuti iye sanali kungofuna kudziwa dzina la bambo ake a Davide. Sauli anafuna kudziwa kuti ndi munthu wotani amene anabereka mnyamata wotereyu, chifukwa tsopano anaona Davide, yemwe anali atangogonjetsa Goliati, kuti anali ndi chikhulupiriro zedi ndiponso anali wolimba mtima kwambiri, zomwe anali asanazionepo mwa Davide. Mwina Sauli anali kuganiza zoti nawonso bambo ake a Davide, omwe anali a Jese, kapena anthu ena a m’banja lawo, awaike m’gulu lake la asilikali, chifukwa iwonso angakhale olimba mtima ngati Davide.

Ngakhale kuti lemba la 1 Samueli 17:58 limangotchula yankho lachidule la Davide lakuti, “ndili mwana wa kapolo wanu Jese wa ku Betelehemu,” mavesi otsatira amasonyeza kuti n’kutheka kuti anakambirana kwa nthawi yaitali ndithu. Pamfundoyi, taonani zimene C. F. Keil ndi F. Delitzsch ananena: “Mawu a pa [1 Samueli 18:1] akuti, ‘pakutsiriza iye kulankhula ndi Sauli,’ akuonetseratu kuti Sauli analankhula naye zinanso zokhudza banja la kwawo, chifukwatu mawu amenewa akusonyeza kuti anakambirana kwa nthawi yotalikirapo.”

Ndi mfundo zonsezi, tinganene kuti Sauli pofunsa funso lakuti, “Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani?” sanali kufuna kudziwa kuti Davide anali ndani, chifukwa zimenezi ankazidziwa kale, koma anafuna kudziwa bwino mbiri yake.

[Mawu a M’munsi]

a Umboni wakuti mavesi amene mulibe mu Septuagint ndi olondola, mungaupeze m’buku la Insight on the Scriptures, Voluyumu 2, tsamba 855, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 31]

N’chifukwa chiyani Sauli anafunsa Davide kuti anali mwana wa ndani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena