Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w11 3/1 tsamba 30-31
  • Muziikira Kumbuyo Kulambira Koona

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muziikira Kumbuyo Kulambira Koona
  • Nsanja ya Olonda—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Amadana Ndi Zinthu Zopanda Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kuwonongedwa kwa Sodomu ndi Gomora
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Yesu Achiritsa Anthu Mozizwitsa
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Mose Anapatsidwa Ntchito Yapadera
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2011
w11 3/1 tsamba 30-31

Zoti Achinyamata Achite

Muziikira Kumbuyo Kulambira Koona

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pamalo opanda phokoso. Pamene mukuwerenga mavesiwo, yerekezerani kuti nkhaniyo ikuchitika inuyo muli pomwepo. Yesani kuona m’maganizo mwanu zimene zikuchitika. Mukhale ngati mukumva zimene anthuwo akulankhula. Yesani kumva mmene anthu a m’nkhaniyi akumvera mumtima mwawo.

Amene akutchulidwa kwambiri m’nkhaniyi: Eliya, Ahabu ndi aneneri a Baala okwana 450

Chidule cha Nkhaniyi: Eliya anasonyeza kuti Yehova ndi wamphamvu kuposa Baala.

1 ONANI NKHANIYI BWINOBWINO.​—WERENGANI 1 MAFUMU 18:17-40.

Pezani pepala ndipo mujambulepo chithunzi chosonyeza pamene panaima Eliya, aneneri a Baala komanso pamene panali maguwa a nsembe.

Kodi “mukumva” phokoso lotani pamene zinthu zachisokonezo zimene azifotokoza mu vesi 26 mpaka 29 zikuchitika?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti mawu a Eliya ankamveka bwanji pamene ankalankhula ndi aneneri a Baala

․․․․․

2 FUFUZANI MOZAMA.

N’chifukwa chiyani Eliya anafunika kulimba mtima kuti alankhule ndi Ahabu ndiponso kuti achite zinthu zimene zinachititsa manyazi aneneri a Baala? (Zokuthandizani: Werengani 1 Mafumu 18:4, 13, 14.)?

․․․․․

Gwiritsani ntchito zinthu zofufuzira zimene muli nazo kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya kulambira Baala. Mwachitsanzo, kodi ina mwa miyambo imene ankachita polambira Baala inali yotani? Kodi kulambira Baala kunakhudza bwanji Aisiraeli

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Eliya anakumba ngalande kuzungulira guwa la nsembe la Yehova komanso kuthira madzi paguwali?

․․․․․

3 GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA ZOKHUDZA . . .

Mmene munthu angasonyezere kulimba mtima poikira kumbuyo kulambira koona.

․․․․․

Madalitso amene munthu angapeze chifukwa chochita zinthu molimba mtima.

․․․․․

MMENE MUNGAGWIRITSIRE NTCHITO MFUNDOZI.

Tchulani njira imodzi kapena zingapo zimene mungasonyezere kulimba mtima pa nkhani ya kuikira kumbuyo kulambira koona.

․․․․․

4 M’NKHANIYI, KODI NDI MFUNDO ITI IMENE YAKUKHUDZANI MTIMA KWAMBIRI, NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․

Ngati mulibe Baibulo, uzani a Mboni za Yehova, kapena kawerengeni Baibulo pa Adiresi ya pa Intaneti iyi: www.jw.org.

[Bokosi patsamba 31]

Zokhudza Msonkhano Wachigawo

Kuyambira chaka chino, madeti ndiponso malo amisonkhano yachigawo sadziikidwanso mu Nsanja ya Olonda. Madeti ndi malo amisonkhanowa azipezeka pa adiresi ya pa Intaneti iyi, www.jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena