Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w12 10/1 tsamba 4-5
  • N’Chifukwa Chiyani Anthu Akupitirizabe Kuchita Ziphuphu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’Chifukwa Chiyani Anthu Akupitirizabe Kuchita Ziphuphu?
  • Nsanja ya Olonda—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Ziphuphu Zidzatha
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Lonjezo la Dziko Lopanda Kusaona Mtima
    Nsanja ya Olonda—1995
  • N’chifukwa Chiyani Kuli Ziphuphu Zochuluka Chotere?
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2012
w12 10/1 tsamba 4-5

N’Chifukwa Chiyani Anthu Akupitirizabe Kuchita Ziphuphu?

“Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”—MLALIKI 8:9.

MAWU amenewa akufotokoza bwino zimene zakhala zikuchitika mu ulamuliro wa anthu. Ulamuliro wa anthu wabweretsa mavuto osaneneka. Kwa zaka zambiri anthu a zolinga zabwino ofuna kukonza zinthu alephera kukwaniritsa zolinga zawozo chifukwa cha ziphuphu ndi dyera. N’chifukwa chiyani zili chonchi? Kodi ziphuphu zidzatha? Ziphuphu zimachitika chifukwa cha zinthu zikuluzikulu zitatu izi:

1. Mphamvu ya uchimo.

Baibulo limanena momveka bwino kuti tonsefe “ndi ochimwa.” (Aroma 3:9) Uchimo “umene uli mwa” anthufe uli ngati matenda osachiritsika komanso otengera kwa makolo. Kwa zaka zambirimbiri uchimo wakhala ‘ukulamulira’ anthu ngati mfumu ndipo “chilamulo” chake chikugwirabe ntchito mwa ife. Uchimo umapangitsa anthu ambiri kuti azingoganizira zofuna zawo basi. Umapangitsanso kuti anthuwa azifunitsitsa kupeza chuma kapena udindo ngakhale zitakhala kuti zimenezo zingachititse kuti anthu ena avutike.—Aroma 5:21; 7:17, 20, 23, 25.

2. Dziko loipali.

Anthu ambiri m’dzikoli ali ndi makhalidwe oipa monga dyera komanso kudzikonda. Zimenezi zimachititsa kuti anthu ena azitengera makhalidwe oipawa. Chifukwa chodzikonda, anthu amafunitsitsa kukhala ndi udindo. Iwotu amalakalaka kukhala ndi ndalama komanso chuma ngakhale kuti ndi olemera kale. N’zomvetsa chisoni kuti iwo amachita zinthu zachinyengo n’cholinga choti apeze zimene akufunazo. M’malo mopewa kutsatira zoipa zimene ena akuchita, anthu oterewa ‘amangotsatira khamu pochita zoipa.’—Ekisodo 23:2.

3. Mphamvu ya Satana Mdyerekezi.

Satana, yemwe ndi wopanduka, “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Iye ndi katswiri pogwiritsa ntchito anthu kuti akwanitse zolinga zake. Mochenjera amagwiritsa ntchito mtima wa munthu amene akulakalaka chuma komanso zinthu zapamwamba kuti munthuyo azichita zinthu mwachinyengo.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Satana amangotigwiritsa ntchito anthufe ngati zidole zake, moti palibe zimene tingachite kuti tipewe zofuna zakezo? Nkhani yotsatira ikuyankha funso limeneli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena