Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w13 10/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2013
  • Nkhani Yofanana
  • Chiukiriro—Cha Yani, ndipo Kuti?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Akufa Adzauka?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chokhudza Anthu Amene Anamwalira?
    Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2013
w13 10/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?

Imfa ili ngati tulo ndipo munthu akamwalira sadziwa kanthu komanso sangachite chilichonse. Komabe Mulungu, amene analenga moyo, akhoza kupangitsa kuti anthu amene anamwalira auke n’kukhalanso ndi moyo. Pofuna kutsimikizira kuti akhoza kuchita zimenezi, Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zoukitsa anthu ndipo anaukitsa anthu angapo.—Werengani Mlaliki 9:5; Yohane 11:11, 43, 44.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti imfa ili ngati tulo?

Mulungu analonjeza kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo m’dziko latsopano mmene mudzakhale chilungamo. Koma pakali pano anthu amenewa ayenera kuyembekezerabe mpaka pa nthawi imene Mulungu wakonza kudzawaukitsa. Mulungu Wamphamvuyonse amalakalaka kugwiritsa ntchito mphamvu zake pochititsa kuti anthu amene anamwalira akhalenso ndi moyo.—Werengani Yobu 14:14, 15.

Kodi zidzakhala bwanji anthu akadzaukitsidwa?

Anthu akadzauka adzatha kuzindikira achibale awo komanso anzawo. Ngakhale zitakhala kuti thupi la munthu linawola, Mulungu akhoza kumuukitsa munthu ndi thupi lina latsopano.—Werengani 1 Akorinto 15:35, 38.

Anthu ena ochepa amaukitsidwa kuti akakhale kumwamba. (Chivumbulutso 20:6) Koma ambiri amene adzaukitsidwe adzakhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi pompano. Pa nthawiyi adzakhalanso ndi mwayi wokhala ndi moyo kwa muyaya.—Werengani Salimo 37:29; Machitidwe 24:15.

Kuti mumve zambiri, werengani mutu 6 ndi 7 wa buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Mukhozanso kulipanga dawunilodi pa www.jw.org

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena