KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
Kodi akufa adzakhalanso ndi moyo?
N’zomveka kuti Mulungu adzaukitsa anthu chifukwa ndi amene anatilenga
Yehova Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse. (Salimo 36:9) Popeza ndi amene analenga zonse, n’zosakayikitsa kuti adzaukitsa anthu omwe anamwalira. (Werengani Machitidwe 24:15) Koma n’chifukwa chiyani adzachite zimenezi?
Pamene Mulungu ankalenga anthu sankafuna kuti azifa. (Genesis 1:31; 2:15-17) Iye sanasinthe maganizo akewa ndipo amafunabe kuti anthu adzakhale ndi moyo padzikoli mpaka kalekale. Choncho zimamupweteka kwambiri akamaona anthu akuvutika kenako n’kufa.—Werengani Yobu 14:1, 14, 15.
Kodi anthu oukitsidwa adzakhala kuti?
Kodi Mulungu analenga anthu kuti azikhala kuti? Anawalenga kuti azikhala padziko lapansi. Koma angelo ndi amene anawalenga kuti azikhala kumwamba. (Genesis 1:28; Yobu 38:4, 7) Komanso kumbukirani kuti Yesu ali padziko lapansi anaukitsa anthu ndipo anthuwo anakhala padziko lapansi lomweli. Ndi zimenenso zidzachitike mtsogolomu. Anthu ambiri omwe adzaukitsidwe azidzakhala padziko lapansili.—Werengani Yohane 5:28, 29; 11:44.
Koma pali anthu ena ochepa omwe Mulungu wasankha kuti adzaukitsidwire kumwamba. Anthuwa adzaukitsidwa ndi matupi ngati a angelo. (Luka 12:32; 1 Akorinto 15:49, 50) Anthu amenewa adzakhala mafumu limodzi ndi Khristu kumwamba ndipo azidzalamulira dziko lapansili.—Werengani Chivumbulutso 5:9, 10.