Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 12/1 tsamba 16
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo?
    Kodi Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo Tingawapeze Kuti?
  • Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
    Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?
  • Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 12/1 tsamba 16

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi ana angaphunzire bwanji kukonda Mulungu?

Bambo akuphunzitsa mwana wake pogwiritsa ntchito zinthu zimene Mulungu analenga

Mungagwiritse ntchito zinthu zomwe Mulungu analenga pothandiza ana anu kudziwa komanso kukonda Mulungu

Ana anu angaphunzire kukonda Mulungu pokhapokha ngati ali ndi umboni woti iye alipo ndiponso amawakonda. Komanso ayenera kudziwa mfundo zosiyanasiyana zokhudza Mulungu. (1 Yohane 4:8) Mwachitsanzo, ayenera kudziwa mayankho a mafunso otsatirawa: Kodi Mulungu analengeranji anthu? N’chifukwa chiyani amalola kuti anthufe tizivutika? Kodi Mulungu adzawachitira chiyani anthu m’tsogolomu?—Werengani Afilipi 1:9.

Pofuna kuthandiza ana anu kuti azikonda Mulungu, muyenera kusonyeza kuti inunso mumakonda Mulungu. Ana anu akaona kuti mumakonda Mulungu, nawonso angayambe kumukonda.—Werengani Deuteronomo 6:5-7; Miyambo 22:6.

Kodi mungatani kuti muziphunzitsa ana anu mogwira mtima?

Mawu a Mulungu ndi amphamvu. (Aheberi 4:12) Choncho thandizani ana anu kudziwa mfundo zosavuta kumvetsa za m’Baibulo. Pophunzitsa, Yesu ankagwiritsa ntchito mafunso, ankamvetsera anthu akamalankhula komanso ankafotokoza Malemba. Izi zinachititsa kuti aziphunzitsa mogwira mtima. Inunso mukamachita zimenezi pophunzitsa ana anu, mungathe kuwafika pa mtima.—Werengani Luka 24:15-19, 27, 32.

Komanso, m’Baibulo muli nkhani zosonyeza mmene Mulungu ankachitira zinthu ndi anthu. Nkhani zimenezi zingathandize ana anu kuti amudziwe bwino Mulungu komanso kuti azimukonda. Mabuku ofotokoza nkhani zoterezi akupezeka pa webusaiti ya www.jw.org/ny.—Werengani 2 Timoteyo 3:16.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 14 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pa webusaiti yathu ya www.jw.org/ny. Mungathenso kutilembera pogwiritsa ntchito maadiresi omwe ali patsamba 2 kuti tikutumizireni bukuli kwaulere

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena