Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp17 No. 1 tsamba 5-6
  • Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kukhale Kosangalatsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kukhale Kosangalatsa?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndi Ndani Amene Anagawa Machaputala ndi Mavesi a M’Baibulo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Mungaphunzirenso Izi
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikuthandizani Kwambiri?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
wp17 No. 1 tsamba 5-6
Mayi akuwerenga Baibulo ndipo akugwiritsa ntchito zinthu zina zomuthandiza kuphunzira

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI KUTI KUWERENGA BAIBULO KUZIKUSANGALATSANI

Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kukhale Kosangalatsa?

Kodi mumaona kuti kuwerenga Baibulo n’kotopetsa, kapena kosangalatsa? Zimene mumachita powerenga n’zimene zingachititse kuti muzisangalala kapena ayi. Tiyeni tione zimene mungachite kuti muzisangalala powerenga Baibulo.

Muziwerenga Baibulo lolondola komanso losavuta. Ngati mutamawerenga Baibulo limene lili ndi mawu ambiri ovuta kapena akalekale omwe simukuwadziwa, kuwerengako sikungakusangalatseni. Choncho mungachite bwino kupeza Baibulo losavuta kumva limene lingakufikeni pamtima. Komabe muyenera kutsimikizira kuti Baibulolo linamasuliridwa molondola.a

Mungawerenge pogwiritsa ntchito chipangizo chamakono. Masiku ano mukhoza kuwerenganso Baibulo pa intaneti kapena kulichita dawunilodi kuti muziwerengera pakompyuta, tabuleti kapena pafoni. Mabaibulo ena amakhala ndi zinthu zokuthandizani kuona mwamsanga mavesi osiyanasiyana okhudza nkhani imene mukuwerenga komanso kuona mmene Mabaibulo ena anamasulirira mavesi amene mukuwerenga. M’zilankhulo zina, Baibulo limapezekanso longomvetsera. Anthu ambiri amakonda kumvetsera Baibulo akakwera basi, akamachapa kapena kuchita zinthu zina. Kodi mungayeseko zina mwa zinthu zimene tatchulazi?

Muzigwiritsa ntchito zinthu zothandiza pophunzira Baibulo. Pali zinthu zina zimene zingakuthandizeni kwambiri powerenga Baibulo. Mwachitsanzo, pali mapu a madera otchulidwa m’Baibulo omwe angakuthandizeni kudziwa pamene pali malo enaake ndiponso kumvetsa nkhani imene mukuwerenga. Nkhani za m’magazini a Nsanja ya Olonda kapena za pachigawo chakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa” pawebusaiti ya jw.org, zingakuthandizeni kumvetsa nkhani zambiri za m’Baibulo.

Muzisinthasintha njira zowerengera. Ngati mumaona kuti kuwerenga Baibulo kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso n’kovuta, mukhoza kuyamba ndi nkhani imene imakusangalatsani kwambiri. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza anthu otchuka a m’Baibulo, mungayambe ndi kuwerenga za anthuwo. Mukhoza kuwerenga malemba amene ali m’bokosi lakuti “Anthu a M’Baibulo Amene Mungawerenge Nkhani Zawo.” Apo ayi, mwina mungafune kuwerenga malemba onse okhudza nkhani inayake kapena kuwerenga potsatira nthawi imene zinthu zinachitika. Mungachite bwino kuyesa imodzi mwa njira zimene tatchulazi.

a Anthu ambiri amaona kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ndi lolondola, lodalirika komanso losavuta kuwerenga. Baibuloli linapangidwa ndi a Mboni za Yehova ndipo likupezeka m’zilankhulo zoposa 130. Mukhoza kuchita dawunilodi Baibulo limeneli pawebusaiti ya jw.org kapena pa pulogalamu ya JW Library. Komanso ngati mungakonde, a Mboni za Yehova akhoza kukupatsani Baibuloli.

ANTHU A M’BAIBULO AMENE MUNGAWERENGE NKHANI ZAWO

Akazi ena okhulupirika

Abigayeli

1 Samueli chaputala 25

Esitere

Esitere chaputala 2-5, 7-9

Hana

1 Samueli chaputala 1-2

Mariya

(Mayi a Yesu) Mateyu chaputala 1-2; Luka chaputala 1-2; mungaonenso Yohane 2:1-12; Machitidwe 1:12-14; 2:1-4

Rahabi

Yoswa chaputala 2, 6; mungaonenso Aheberi 11:30, 31; Yakobo 2:24-26

Rabeka

Genesis chaputala 24-27

Sara

Genesis chaputala 17-18, 20-21, 23; mungaonenso Aheberi 11:11; 1 Petulo 3:1-6

Amuna ena okhulupirika

Abulahamu

Genesis chaputala 11-24; mungaonenso 25:1-11

Davide

1 Samueli chaputala 16-30; 2 Samueli chaputala 1-24; 1 Mafumu chaputala 1-2

Yesu

Mabuku a Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane

Mose

Ekisodo chaputala 2-20, 24, 32-34; Numeri chaputala 11-17, 20, 21, 27, 31; Deuteronomo chaputala 34

Nowa

Genesis chaputala 5-9

Paulo

Machitidwe chaputala 7-9, 13-28

Petulo

Mateyu chaputala 4, 10, 14, 16-17, 26; Machitidwe chaputala 1-5, 8-12

ZINTHU ZOTHANDIZA POPHUNZIRA BAIBULO ZIMENE A MBONI ZA YEHOVA ANAPANGA

  • JW.ORG—Webusaitiyi ili ndi zinthu zambiri zothandiza pophunzira Baibulo, monga nkhani zakuti “Kuyankha Mafunso a M’baibulo.” Ilinso ndi malangizo okuthandizani kupanga dawunilodi pulogalamu ya JW Library

  • ‘Onani Dziko Lokoma’—Kabukuka kali ndi mapu komanso zithunzi za malo otchulidwa m’Baibulo

  • Insight on the Scripturesb—Ndi mabuku awiri ofotokoza za anthu, malo ndiponso mawu ena a m’Baibulo

  • “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial”*—Bukuli limatchula nthawi komanso malo amene buku lililonse la m’Baibulo linalembedwera. Limafotokozanso chifukwa chimene buku lililonse linalembedwera ndiponso zimene zili m’bukulo

  • Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu—Kabukuka kali ndi mapu, zithunzi komanso zinthu zina zothandiza

  • Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?—Kabukuka kali ndi masamba 32 ndipo kamafotokoza mwachidule uthenga wa m’Baibulo

b Mabukuwa akupezeka m’Chingelezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena