Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w17 June tsamba 32
  • Kodi Mukudziwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Yesu Anayeretsa Kachisi
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Yesu Anayeretsanso Kachisi
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Ayeretsa Kachisi
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
w17 June tsamba 32
Yesu akuthamangitsa anthu amene ankachita malonda m’kachisi

Kodi Mukudziwa?

Kodi amalonda amene ankagulitsa nyama kukachisi mu Yerusalemu analidi ngati “achifwamba”?

BUKU la Mateyu limanena kuti: “Yesu analowa m’kachisi ndi kuthamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda. Iye anawauza kuti: ‘Malemba amati, “Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,” koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.’”​—Mat. 21:12, 13.

Mabuku a mbiri yakale ya Ayuda amasonyeza kuti amalondawa ankapeza phindu mwachinyengo pokweza kwambiri mitengo. Mwachitsanzo, buku lina limanena kuti pa nthawi ina amalondawo ankagulitsa nkhunda ziwiri zoti anthu apereke nsembe pa mtengo wa dinari imodzi yagolide. Ndalamayi ndi imene munthu wamba ankapeza akagwira ntchito kwa masiku 25. Nkhunda kapena njiwa ndi zimene anthu osauka ankaloledwa kupereka nsembe. Koma amalondawo ankagulitsanso mbalame zimenezi pa mtengo wodula kwambiri. (Lev. 1:14; 5:7; 12:6-8) Rabi wina dzina lake Simeon ben Gamaliel ataona zimene zinkachitikazi, anadandaula kwambiri. Choncho anachepetsa chiwerengero cha nsembe zimene anthu ankayenera kupereka ndipo izi zinathandiza kuti mtengo wa njiwa ziwiri utsike ndi 99 peresenti.

Malinga ndi zimene tafotokozazi, Yesu ananena zoona pamene anatchula amalonda akukachisi kuti “achifwamba.” Zili choncho chifukwa anthuwo anali achinyengo komanso adyera kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena