Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp18 No. 1 tsamba 12-13
  • 3 Lingakuthandizeni Kupirira Mavuto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 3 Lingakuthandizeni Kupirira Mavuto
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MATENDA OKHALITSA
  • IMFA YA MNZATHU KAPENA WACHIBALE
  • Kuchokera ku Tondovi Kumka ku Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi Kupemphera Kungakuthandizeni Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2021
  • Kupemphera N’kothandiza Kwambiri
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mmene Ena Anapezera Mayankho
    Nsanja ya Olonda—2003
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
wp18 No. 1 tsamba 12-13
Mzimayi ali kumanda ndipo akulira; mzimayi ali panjinga ya olumana ndipo akumvetsera uthenga wa m’Baibulo

3 Lingakuthandizeni Kupirira Mavuto

Pali mavuto ena amene sitingawapewe kapena kuwathetsa. Mwachitsanzo, ngati mwaferedwa kapena ngati mukudwala matenda okhalitsa palibe chimene mungachite, mungangofunika kupirira. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji pa mavuto ngati amenewa?

MATENDA OKHALITSA

Mtsikana wina dzina lake Rose anati: “Ndinabadwa ndi vuto linalake limene limachititsa kuti ndizimva kupweteka kwambiri. Vutoli limachititsa kuti thanzi langa lizifooka.” Vuto lalikulu limene Rose ankakumana nalo linali lakuti nthawi zambiri akamawerenga Baibulo komanso mabuku othandiza kuphunzira Baibulo ankalephera kuika maganizo ake pa zimene akuwerengazo. Koma mawu a Yesu a palemba la Mateyu 19:26 ndi amene anamuthandiza. Lembali limati: “Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” Rose anazindikira kuti pali njira zambiri zophunzirira. Popeza nthawi zambiri ankamva kupweteka akamawerenga, anaganiza zoti azingomvetsera Baibulo kapena mabuku othandiza kuphunzira Baibulo amene anajambulidwa.a Rose anati: “Njira imeneyi ndi imene inandithandiza kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu.”

Nthawi zina Rose amakhumudwa chifukwa choona kuti sakutha kuchita zimene ankachita poyamba. Koma lemba limene limamulimbikitsa ndi la 2 Akorinto 8:12 lomwe limati: “Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe, osati zimene sangathe.” Mawu amenewa amamukumbutsa Rose mfundo yakuti Mulungu amasangalala ndi zimene iye amachita chifukwa ndi zimene angakwanitse.

IMFA YA MNZATHU KAPENA WACHIBALE

Delphine amene tamutchula kale uja anati: “Mwana wanga wamkazi wazaka 18 atamwalira, ndinali ndi chisoni kwambiri moti ndinkangoona ngati nanenso ndifa. Ndinkaona kuti palibe chomwe chinkayenda.” Koma mawu a palemba la Salimo 94:19 ndi omwe anamuthandiza. Lembali limati: “Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.” Delphine anati: “Ndinapempha Yehova kuti andithandize kupeza zochita zimene zingandithandize kuti ndizisangalala.”

Delphine anayamba kumatanganidwa ndi ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Kenako zinthu zinayamba kusintha. Iye ankaona kuti ali ngati chekeni chomwe chathyoka koma munthu angathe kuchigwiritsabe ntchito. Ankaona kuti ngakhale kuti ali ndi mavuto ambiri, angathe kuthandiza ena. Delphine anati: “Ndikamagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pothandiza anthu amene ndinkaphunzira nawo Baibulo, inenso ndinkalimbikitsidwa. Ndinazindikira kuti imeneyi inali njira imene Mulungu ankandithandizira kuti ndizikhala wosangalala.” Delphine analemba mayina a anthu otchulidwa m’Baibulo amene anakhalapo ndi chisoni chifukwa choferedwa. Iye anati: “Anthu onsewa ankakonda kupemphera.” Iye anazindikiranso kuti “sungapeze mayankho amene ukufuna ngati sumawerenga Baibulo.”

Kuphunzira Baibulo kwamuthandiza Delphine kuti asamaganizire kwambiri za m’mbuyo koma zakutsogolo. Mfundo imene imamuthandiza kwambiri ndi ya pa Machitidwe 24:15 yakuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” Iye amakhulupirira kwambiri kuti Yehova adzaukitsa mwana wake. Delphine anati: “M’maganizo mwanga ndimamuona mwana wanga ataukitsidwa. Ndimakhulupirira kuti Yehova anakonza kale tsiku loti adzamuukitse. Ndimatha kumuona ndili naye limodzi m’munda wathu wamaluwa ndikusangalala kwambiri ngati mmene zinalili patsiku lomwe anabadwa.”

a Zinthu zongomvetserazi zimapezeka pa webusaiti yathu ya jw.org.

Baibulo lingakuthandizeni kwambiri ngakhale pa nthawi ya mavuto

Kodi Mulungu Angatithandize Bwanji?

Baibulo limayankha momveka bwino funso limeneli. Limati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi, ndipo anthu amene amamuopa adzawachitira zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” (Salimo 145:18, 19) Mawu amenewa ndi olimbikitsa kwambiri. Koma kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphero a anthu amene amafunitsitsa kuti awathandize?

POTIPATSA MPHAMVU:

Mavuto angachititse kuti tikhumudwe komanso tifooke potumikira Mulungu. (Miyambo 24:10) Koma Yehova “amapereka mphamvu kwa munthu wotopa, ndipo wofooka amam’patsa nyonga zochuluka.” (Yesaya 40:29) Mtumwi Paulo, yemwe pa nthawi ina anakumana ndi mavuto, anati: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Mzimu woyera wa Mulungu unkathandiza Paulo kuti akhale ndi mphamvu. Inunso mungapemphe Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera.​—Luka 11:13.

POTIPATSA NZERU:

Kodi mungatani ngati mukufuna kumvetsa malangizo enaake a m’Baibulo komanso mmene mungawatsatirire? Yakobo analemba kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” (Yakobo 1:5) Muyeneranso kuchita zogwirizana ndi zimene mwapemphazo powerenga Baibulo komanso kuyesetsa kutsatira zimene limanena. (Yakobo 1:23-25) Mukamachita zimenezi mudzaona kuti malangizo a m’Baibulo ndi othandiza kwambiri.

POTIPATSA MTENDERE:

Ngati mukuda nkhawa kwambiri ndi zinazake Yehova angakuthandizeni kuti mukhale ndi mtendere wamumtima. Mawu ake amati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Ngati mukuda nkhawa ndi zinazake, mungapemphe Yehova kuti akupatseni mtendere wamumtima.

Koma kodi mungatani ngati mavuto anu sakutha? Musaganize kuti Mulungu wakusiyani. Ngakhale kuti nthawi zina Mulungu sangachititse kuti mavuto anu athe, iye angakupatseni mphamvu kuti muzitha kupirira. (1 Akorinto 10:13) Komanso Baibulo limanena kuti posachedwapa mavuto onse adzatheratu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena