Dziperekeni Pothandiza Anthu Atsopano
1 Ndi mwayitu kwabasi kukhala ndi anthu amene anazoloŵera kufalitsa uthenga wabwino. Amathandiza kwambiri mpingo akamagwiritsa ntchito luso lawo komanso zimene akudziŵa kuthandiza anthu atsopano ambiri, amene akubwera ku gulu la Yehova lerolino. Iwo amamvera langizo louziridwa lakuti: “Monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo.”—1 Pet. 4:10.
2 Tifunika kuyamikira ofalitsa osabatizidwa limodzi ndi awo amene angobatizidwa kumene chifukwa chogwira ntchito molimbika mu utumiki wakumunda. Komabe, luso lawo pa ntchito yolalikira lingakhale la mbali imodzi kapena ziŵiri basi, monga kugaŵira magazini ndi kulalikira mwamwayi. Kuti kupita patsogolo kwa atsopano ameneŵa kuonekere, iwo afunika kuchita nawo mbali zonse za utumiki monga momwe angathere ndi kukulitsa luso lawo monga olengeza uthenga wabwino. Atsopano adzathandizidwa kukhala atumiki a Ufumu a luso mwa kuyenda ndi awo amene ali ozoloŵera kwambiri.—Mlal. 4:9, 10.
3 Dziperekeni: Kodi mungadzipereke kuti muthandize ena mu utumiki? Atsopano sakungofunika kuphunzira mmene angagaŵire magazini basi koma mmenenso angagwiritsire ntchito Baibulo mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Musananyamuke ulendo wa ku utumiki, onani ngati aliyense ali ndi Baibulo lake. Ngati alibe, athandizeni mmene angapezere Baibulo. Afunika kuphunzira mmene angayambire ndi kupitiriza kukambirana ndi eninyumba. Wina amene sanazoloŵere kulalikira angakhale ndi mantha kupanga maulendo obwereza ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo. Koma awo amene akufuna, angaphunzire mmene angagwirire ntchito zatsopano zimenezi ngati alandira thandizo ndi chilimbikitso choyenera.
4 Momwe Mungathandizire: Njira imodzi yomwe mungathandizire anthu amene sanazoloŵere kwenikweni ndiyo kusonkhana nawo pamodzi ndi kukambirana zitsanzo za ulaliki za mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Mwa kugwiritsa ntchito buku la Kukambitsirana, sankhani mawu oyamba oyenera ndipo yesererani kuyankha anthu otsutsa ndi okana kukambirana. Poyesererapo, mungagwiritse ntchito malemba ndi mmene mungagaŵire buku logaŵira nthaŵi imeneyo. Mungakambirane mmene mungamalizire kukambirana paulendo woyamba n’cholinga choti muyale maziko a ulendo wobwereza, kapena mungasonyeze mmene mungayambire phunziro la Baibulo. Kukonzekera kotero kudzathandiza wofalitsa watsopano kukhala ndi chidaliro choti angathe kulankhula ndi anthu za Mawu a Mulungu.
5 Khalani ndi makonzedwe otsimikizika opita mu utumiki wakumunda. Wofalitsa watsopanoyo angasankhe kungoyenda nanu kaye nyumba zingapo kuti aonere. Ndiyeno angayese kuchita zomwe anakonza panthaŵi yoyeserera. Pamene mukuyendera limodzi, kambiranani mmene mungasinthire maulaliki anu kukhala abwino ndi mmene mungachitire ndi anthu opanda chidwi ndi otsutsa. Khalani wolimbikitsa ndi wothandiza. Kumbutsani watsopanoyo kuti imeneyo ndi ntchito ya Yehova ndi kuti adzadalitsa khama lanu lonse.—Afil. 4:13.
6 Yendaninso ndi Ana: Ana amasangalala kwambiri mu utumiki akakonzekera bwino ulaliki. Tingalimbikitse ana aang’ono kwambiri kukonzekera ulaliki wosavuta wa magazini. Ngati angathe, angapatsidwe mwayi wakuti amuŵerengere mwininyumba lemba la m’Baibulo. Thandizani aliyense kulimbikira malingana ndi msinkhu komanso luso lake. Makolo ndi ena mu mpingo angathandize ndi kulimbikitsa ana aang’ono kwambiri komanso amene akukula kuti akhale aluso ‘polunjika nawo bwino mawu a choonadi.’—2 Tim. 2:15; onani om-CN tsamba 99, ndime 2.
7 Amene amachititsa maphunziro a Baibulo adzafunika kuthandiza ophunzira kuti ayenere mwamsanga kukhala ofalitsa osabatizidwa. Akulu, atumiki otumikira, apainiya ndi makolo ayenera kukhala okonzeka kuthandiza awo amene akungoyamba kumene ntchito yolalikira. Kodi mungadzipereke kuthandiza atsopano? Yambani ndinu kuchita zimenezo, popeza kuti ‘tikalumikizana pamodzi, thupi lonse lidzakula.’—Aef. 4:16, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.