Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/99 tsamba 3-4
  • Pitirizanibe Kubala Zipatso ndi Kupirira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizanibe Kubala Zipatso ndi Kupirira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Pitirizanibe Kukhala M’gulu la Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Yehova Amakonda Anthu Amene ‘Amabereka Zipatso’ Mopirira
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • ‘Achimwemwe Ali Awo Amene Apirira’
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Mubale Chipatso Chambiri”
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 12/99 tsamba 3-4

Pitirizanibe Kubala Zipatso ndi Kupirira

1 Polembera mpingo wa ku Kolose, zaka zosaposa 30 imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu Kristu kutachitika, mtumwi Paulo ananena kuti choonadi cha uthenga wabwino chinali kubala zipatso ndi kuwonjezeka m’dziko lonse. (Akol. 1:5, 6) Lerolino m’lingaliro lenileni, Mboni za Yehova zafika ‘malekezero ake a dziko lapansi’ ndi uthenga wabwino wa Ufumu pamlingo waukulu. (Mac. 1:8; Yoh. 14:12) M’chaka cha utumiki cha 1998, panali kuwonjezereka kwa 3.6 peresenti pa avareji ya ofalitsa Ufumu apadziko lonse, ndipo tinafika chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 5,888,650 m’mayiko 233!

2 M’mayiko amene kulalikira Ufumu wa Mulungu kuli koletsedwa ndipo malipoti sakhala onse, anapereka lipoti la kuwonjezereka kwakukulu ndithu la 6.0 peresenti! Mosasamala kanthu za mavuto ochuluka amene ali m’mayiko ameneŵa, ofalitsa akupitirizabe ‘kubala zipatso ndi kupirira.’ (Luka 8:15) M’malo ena ziletso zachepa, komabe m’mayiko ena mikhalidwe yovuta sikusintha.

3 M’mayiko amene muli ufulu waukulu wochita ntchito yolalikira Ufumu, timakumana ndi mavuto ena osiyanasiyana. Timapeza anthu osasamala ndi opanda chidwi, makamaka m’mayiko olemera. Atumiki a Yehova ayenera kuonetsetsa kuti sakutengera mikhalidwe yotereyi. Sitikufuna kuti zinthu zakuthupi, zosangalatsa, maseŵera, ndi zododometsa zina zisokoneze ntchito yathu ya teokalase. Apo ayi tingakhale opanda chidwi ndi kulephera kuzindikira kufunika kopitirizabe kubala zipatso ndi kupirira.—Luka 21:34-36.

4 ndi Kofunika Kupirira ndi Kulimbikira: Kupirira n’kofunika pamene uthenga wabwino ukuletsedwa kapena ngati tili ndi ufulu wochepa posamalira maudindo athu achikristu. M’mayiko ena, abale athu akhala akugwira ntchito m’mikhalidwe yovuta kwa zaka zambiri. Kupirira kwawo mavuto oterewo kwabweretsa zabwino, ndipo iwo tsopano akupeza madalitso ochuluka. (Aroma 5:3-5; Agal. 6:9) Mavuto alionse amene tingakumane nawo, tikufuna kupirirabe. Umboni wa Ufumu uyenera kuperekedwa, ndipo tonsefe tiyenera kupitiriza kusonyeza umphumphu wathu. Mwakupirira kwathu, tidzapulumutsa moyo wathu.—Marko 13:10; Luka 21:19.

5 Tingasonyeze kuti sitiona zinthu zauzimu mwachibwanabwana mwa kulimbikira kwambiri mu utumiki wa Yehova, osalema mu ntchito yolalikira. M’mayiko ena kumene zoyendera n’zovuta kwambiri, kumene chuma chakuthupi chili chosoŵa, ndi kumene kuli mavuto azachuma, sakuleka kulalikira uthenga wabwino. M’mayiko ochepa mwa mayiko otereŵa, ofalitsa a mumpingo nthaŵi zambiri amafika avareji ya maola 13 mu utumiki wakumunda mwezi uliwonse. Chiŵerengero chawo cha apainiya chikuwonjezerekanso. Zimenezi zimapangitsa ife amene tili ndi chuma chakuthupi chochuluka kudzifunsa. Kodi tingawonjezere pa zimene timachita nthaŵi zonse mu ntchito yofunika kwambiri yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira?

6 Kodi Tingachite Zambiri?: Kukhala nthaŵi yambiri mu utumiki wakumunda kumafuna kusintha pang’ono ndandanda zathu. Ngati Lamlungu timakhala ola limodzi mu utumiki wakumunda, kodi tingawonjezere nthaŵi imeneyo mwakukhala ola lina kupanga maulendo obwereza kapena kuchititsa phunziro la Baibulo? Kapena ngati timachititsa phunziro la Baibulo, kodi tingaphatikizepo ola limodzi kapena kuposerapo mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba kapena kupanga maulendo obwereza angapo tisanapite ku phunziroko? Loŵeruka tikatha maola aŵiri mu ulaliki wa magazini, tingakapereke magazini panjira ya magazini imene tinayambitsa kapena kupanga maulendo obwereza angapo. Anthu amene amakhala m’matauni angaone kukhala koyenera kuthera nthaŵi ina mu umboni wa mumsewu. M’njira zimenezi ndiponso zina, tikhoza kuwonjezera zimene timachita mu utumiki wakumunda. Zotsatirapo zabwino zidzawonjezekanso.

7 Mosakayikira, kukhala nthaŵi yaitali mu utumiki wakumunda, kupanga maulendo obwereza, chotsatira chake chidzakhala kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri. M’kupita kwa nthaŵi izi zikapangitsa anthu ambiri kukhala m’choonadi ndi kutithandiza kukwaniritsa ntchito yolalikira Ufumu.—Mat. 28:19, 20.

8 Pemphero N’lofunika: Kuti tipitirizebe kubala zipatso ndi kupirira, tiyenera kupempha dalitso la Yehova ndi kumvera chitsogozo cha mzimu wake. Tiyenera kupempherera utumiki wathu kwa Yehova. Pamene tikupemphera kwa Yehova ponena za ntchito yathu ya m’munda, timakumbutsidwa kuti ndife antchito anzake. (1 Akor. 3:9) Ndi thandizo la Yehova, tingapirire mu utumiki wathu ngakhale pamene sitikuona zotsatira nthaŵi yomweyo. M’madera ena, kuwonjezereka kwakhalapo olengeza Ufumu atapirira mokhulupirika kwa zaka zambiri. Pamene tikuyang’ana m’tsogolo, nthaŵi zonse n’kofunika kupempha chitsogozo ndi chithandizo cha Mulungu kotero kuti tisaleke koma tikwaniritse utumiki wathu mokwanira. (2 Tim. 4:5) Padakali zipatso zambiri zomwe zikupezeka m’ntchito yolalikira Ufumu ndi yopanga ophunzira.

9 Yesu anagogomezera kufunika koti tizipemphera nthaŵi zonse. (Luka 18:1) Paulo analangiza kuti: “Pempherani kosaleka.” (1 Ates. 5:17) Pali zifukwa zofunika zimene tiyenera kukhalira olimbikira kupemphera tsopano lino. Pali ntchito yambiri posamalira nkhosa zimene zikuwonjezeka chaka ndi chaka. Tikufuna kuthandiza ena kubala zipatso ndi kupirira. Tiyenera kusamalira zosoŵa zosiyanasiyana za wofalitsa aliyense payekha ndi za gulu lonse. Poona kufunika kwa zopereka zochirikizira ntchito ndi zopitirizira kusindikiza mabuku onena za Baibulo, tifuna kupempha Yehova kuti apitirizebe kusonkhezera anthu oopa Mulungu kukhala ooloŵa manja pankhani imeneyi.— 2 Akor. 9:8-11.

10 Pamene mbali zina za munda wa dziko lonse zikutseguka kwambiri kuposa kale lonse pankhani za teokalase, uphungu wa m’Malemba wa pa Akolose 4:2 ulidi watanthauzo kwambiri: “Chitani khama m’kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko.” Tiyenera kupempherera abale athu kulikonse kuti apitirizebe kubala zipatso, kuthandiza anthu ena onga nkhosa opezeka m’magawo amene kale anali ovuta kwambiri kuchitirako umboni.

11 Sonyezani Kuyamikira: Tili oyamikira zedi zogaŵira zauzimu zochuluka zimene timasangalala nazo kwambiri! Tikuthokoza Yehova kaamba ka zimenezi, ndipo tikupemphereranso kuti apitirize kudalitsa ntchito ya kapolo wokhulupirika ndi Bungwe lake Lolamulira. Ntchito yawo yodzichepetsa ndi yolimbika imene amatigwirira ndi onga nkhosa padziko lonse ikuyamikiridwa kwambiri.

12 Pofesa mbewu za Ufumu, mabuku ambiri agaŵiridwa. (Mat. 13:3-8, 18-23) Komabe, m’munda mukufunika mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo. Lipoti la dziko lonse likusonyeza kuti mbali yaikulu yolima ndi kuthirira mwa kupanga maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo apanyumba yachitika. Pamene tikupitiriza kuchita mbali yathu pa zinthu zofunika zimenezi za utumiki wathu, tikuthokoza Yehova chifukwa cha madalitso ake osalekeza amene amakulitsa zinthu. Ndithudi, tikupempherera dalitso limenelo.—1 Akor. 3:6, 7.

13 Zosoŵa Zina: Chifukwa choti ali m’dziko ngakhale sali mbali yake, Akristu adzapitirizabe kukumana ndi ziyeso komanso zitsutso, ndipo izi zidzawonjezereka m’masiku otsiriza ano. Ena pakali pano akupirira chizunzo kapena zovuta zina. Ena akuchita ntchito zawo zachikristu m’mayiko amene muli nkhondo. Abale athu akumana ndi masoka onga ngati zivomezi, mphepo za mkuntho, ndi namondwe. Pamene zimenezi zichitika, tiyenera kupempherera abale athu a m’malo otereŵa. (Yerekezani ndi Machitidwe 12:5; 2 Akorinto 1:11.) Nthaŵi zina kumakhala koyenera kufikira kapena kulembera akuluakulu a boma ponena za kuletsedwa kwa ntchito yathu, kuzunzidwa kwa abale athu, kapena nkhani zina zokhudza zinthu za Ufumu. M’mikhalidwe ngati imeneyi, timachita zomwe ife patokha tingathe, ndipo timapempherera anthu ameneŵa kuti akhale aubwenzi ndi atumiki anzathu.—1 Tim. 2:1, 2.

14 M’dziko loipa la Satana mabanja ali ndi mavuto ambiri. (2 Akor. 4:4) Mabanja angakumane ndi mavuto aakulu. Iwo ayenera kulimbikitsidwa kupempha chitsogozo cha Mulungu, ndipo ifenso tingawapempherere. (1 Akor. 7:5; 1 Pet. 3:7) Mitu ya mabanja iyenera kudziŵa kuti Yehova adzamvetsera mapemphero awo a mtima wonse opempha chitsogozo chosamalira bwino mabanja awo. (Ower. 13:8; Afil. 4:6, 7) Achinyamata ndi achikulire omwe akukumana ndi mikhalidwe yovuta. Izi zingachitike kusukulu, pantchito yolembedwa, paulendo, kapena pazochitika zina. Pemphero limatithandiza kukana mzimu wadziko loipali ndi kupitirizabe kubala zipatso pamene tikupitiriza kuchita zokondweretsa Mulungu.—Mat. 6:13; Aef. 6:13-18; 1 Yoh. 3:22.

15 Yehova ndi wakumva pemphero wamkulu. (Sal. 65:2) Nthaŵi zonse tiyenera kuika nkhawa zathu pa iye. (Sal. 55:22) Tili ndi mwayi wosonyeza nkhawa yathu mwa kupempherera zinthu zonse za Ufumu ndi umoyo wa abale athu kwina kulikonse. Pamene tiona ntchito ya otsogolera mumpingo ndi ya amene amatsogolera ntchito yofutukula ya padziko lonse, posamalira anthu odwala mwauzimu, kapena posamalira mavuto aang’ono kapena aakulu a anthu ena, tonsefe tiyenera kumuuza Yehova nkhani zoterozo m’pemphero. (1 Ates. 5:25; Yak. 5:14-16) Inde, tiyenera kutaya nkhawa zathu kwa Yehova ndi chidaliro chonse kuti mosasamala kanthu za zimene tingapemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, iye adzatimva. (1 Pet. 5:7; 1 Yoh. 5:14) Tikhaletu a changu mu utumiki wa Ufumu ndi kuyang’anabe kwa Yehova kuti atithandize kupitirizabe kubala zipatso ndi kupirira.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena