Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/99 tsamba 2-7
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira December 6
  • Mlungu Woyambira December 13
  • Mlungu Woyambira December 20
  • Mlungu Woyambira December 27
  • Mlungu Woyambira January 3
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 12/99 tsamba 2-7

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

CHIDZIŴITSO: Kuyambira kope lino la Utumiki Wathu wa Ufumu, Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki izikhalanso ndi Msonkhano wa Utumiki wa mlungu woyamba wa mwezi wotsatira. Kusintha kumeneku kwachitika kuti tipeŵe kuchedwa kumene kungakhalepo polandira Utumiki Wathu wa Ufumu chifukwa cha makonzedwe atsopano otumizira.

Mlungu Woyambira December 6

Nyimbo Na. 207

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 15: “Tsanzirani Kupanda Tsankho kwa Yehova.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozani tanthauzo la kupanda tsankho, mmene Yehova amakusonyezera, ndi mmene tingasonyezere zimenezi mu utumiki wathu.

Mph. 20: “Kodi Sitinazimvepo Zimenezi?” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Funsani omvetsera kupereka ndemanga za mmene kubwerezabwereza kwawathandizira kumvetsa ndi kudziŵa choonadi bwino.—Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 1995, masamba 21-2, ndi ya August 15, 1993, masamba 13-14, ndime 10-12.

Nyimbo Na. 218 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 13

Nyimbo Na. 168

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Perekani malingaliro a mmene tingayankhire mwanzeru moni wa panthaŵi yatchuti. Ngati mpingo uli ndi mabuku a Munthu Wamkulu kapena Mphunzitsi Wamkulu m’sitoko, sonyezani mmene angagwiritsidwire ntchito bwino mu utumiki nthaŵi yatchuti cha Khirisimasi.

Mph. 15: “Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2000.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Pendani kusintha kuli m’munsiku pa ndandanda ya chaka chatsopano. Nkhani No. 3 izichokera m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba. Nkhani No. 4 izichokera mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo ndipo miyezi itatu yakumapeto kwa chaka nkhaniyi izidzachokera mu Kukambitsirana za m’Malemba. Pamene pali chizindikiro cha (#) ndiye kuti n’koyenera kuti mbale akambe nkhaniyo. Limbikitsani onse kumayendera limodzi ndi ndandanda yawo yoŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu komanso kuchita khama kukamba nkhani zimene apatsidwa m’sukulu.

Mph. 20: “Kodi Mukanena Chiyani kwa Wosakhulupirira Mulungu?” Mafunso ndi mayankho. Pendani zifukwa zosiyanasiyana zimene zapangitsa ena kutaya chikhulupiriro mwa Mulungu. Perekani njira zina zimene tingayankhire anthu ameneŵa, kuwathandiza kuona kufunika kokhulupirira kuti Mulungu aliko. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziŵiri cha ulaliki wachidule. Kuti mupeze zowonjezereka, onani buku la Kukambitsirana, masamba 306-13.

Nyimbo Na. 220 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 20

Nyimbo Na. 219

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Khalani ndi ofalitsa asimbe mwachidule zokumana nazo zenizeni zimene anakumana nazo posachedwapa mu utumiki wakumunda.

Mph. 15: Kuyankha Oyembekezera Kuimitsa kukambitsirana. Kukambirana ndi omvetsera komanso zitsanzo za ulaliki. Ŵerengani “Ndemanga” patsamba 15-16 mu buku la Kukambitsirana. Sankhani “oimitsa kukambitsirana” aŵiri kapena atatu patsamba 16-20, kapena gwiritsani ntchito zina zimene mumakumana nazo kwambiri m’gawo lanu. Pendani malingaliro ena a mmene tingayankhire, ndipo fotokozani chifukwa chake zingakhale zogwira ntchito kumaloko. Mwachidule onetsani zitsanzo zingapo za izo. Funsani omvetsera kusimba mayankho amene anagwiritsa ntchito amene anali ndi zotsatira zabwino.

Mph. 20: Kodi Ndiyenera Kuloŵa Ntchito Yokhudzana ndi Zachipembedzo? Nkhani yokambidwa ndi mkulu, kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 1999 masamba 28-30. Anthu ena aloŵa ntchito zoterozo ndipo m’kupita kwa nthaŵi azindikira kuti zimene anali kuchita sizogwirizana ndi malamulo a Baibulo. Pendani funso limene tiyenera kulilingalira posankha ntchito yolembedwa imene imakhudzana ndi zachipembedzo. Limbikitsani onse kusankha ntchito imene adzakhalabe paunansi wabwino ndi Yehova.—2 Akor. 6:3, 4, 14-18.

Nyimbo Na. 109 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira December 27

Nyimbo Na. 166

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Ngati mpingo wanu usinthe nthaŵi za misonkhano m’chaka chatsopano, perekani chilimbikitso mokoma mtima mukumapempha onse kumapezekabe mosaphonya pamisonkhano nthaŵi zatsopanozo. Dziŵitsani ophunzira Baibulo ndi ena okondwerera za kusintha kulikonse. Kumbutsani onse kupereka malipoti autumiki wakumunda a December.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: Kugaŵira Mabuku Akale m’January. Nkhani ndi zitsanzo. Sonyezani mabuku akale aŵiri kapena atatu amasamba 192, osindikizidwa 1986 isanafike, amene mpingo uli nawo m’sitoko, ndipo limbikitsani ofalitsa kutenga ena mwa mabuku ameneŵa mu utumiki wakumunda. (Ngati mulibe lililonse, kambiranani zina zimene mungagaŵire m’January.) Fotokozani chifukwa chake mabuku akale ameneŵa akadali abwino popangitsa anthu kuchita chidwi ndi Baibulo. M’buku lililonse gogomezerani mfundo ndi mafanizo ofunika kukamba amene angagwiritsidwe ntchito moyenera poyamba kukambirana. Sonyezani chitsanzo cha ulaliki chimodzi kapena ziŵiri. Pamene mwapeza okondwerera, mungagwiritse ntchito bulosha la Mulungu Amafunanji poyambitsa phunziro.

Nyimbo Na. 224 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira January 3

CHIDZIŴITSO: Mipingo siyenera kuchita Msonkhano wawo wa Utumiki wa mlungu woyambira January 3 tsiku lake lisanafike pokhapokha ngati woyang’anira dera akuchezera mpingowo.

Nyimbo Na. 10

Mph. 8: Zilengezo za pampingo.

Mph. 17: Dziŵani Mmene Mungayankhire. (Akol. 4:6) Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Buku la Kukambitsirana ndi chida chabwino kwambiri poyambitsa kukambirana choonadi cha Baibulo ndi ena. Pamene mwininyumba atsutsa chimodzi mwa zikhulupiriro zathu, tingagwiritse ntchito mbali yakuti “Ngati Wina Anena Kuti—” yopezeka kumapeto kwa chigawo chimene chikukamba za chikhulupiriro chimenecho. Kambiranani ndemanga za Baibulo zimene zili patsamba 58-62, ndipo onani chifukwa chake mayankho operekedwawo angakhale ogwira mtima kwambiri.

Mph. 20: “Pitirizanibe Kubala Zipatso ndi Kupirira.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera m’mphatika. Gwirizanitsani nkhaniyi ndi zochitika za kumaloko, limbikitsani onse kuona mikhalidwe yawo mmene Yehova amaionera.

Nyimbo Na. 56 ndi pemphero lomaliza.

Yapitirizidwa patsamba 7

Misonkhano (kuchokera patsamba 2)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena