Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2000
1 Kwa anthu a Yehova, Sukulu ya Utumiki Wateokalase yakhala dalitso kwambiri. Kwa zaka zoposa 50 zapitazi, yathandiza mamiliyoni a anthu kukulitsa maluso awo monga okamba nkhani poyera ndi aphunzitsi a choonadi cha Baibulo. (Sal. 145:10-12; Mat. 28:19, 20) Kodi mungaone mmene sukulu yakuthandizirani? Ingapitirize kutero m’chaka cha 2000 ngati mutengamo mbali mokwanira ndi kugwiritsira ntchito uphungu woperekedwawo.
2 Malangizo a nkhani ndi zofalitsa zimene zidzagwiritsidwa ntchito zalembedwa patsamba loyamba la ndandanda ya sukulu ya 2000. Nthaŵi ya nkhani iliyonse, komwe yatengedwa, mmene iyenera kuperekedwera, ndi nkhani zina zaperekedwa. Chonde khalani ndi nthaŵi yoŵerenga malangizoŵa bwinobwino ndi kuwagwiritsira ntchito.
3 Kuŵerenga Baibulo Mlungu ndi Mlungu: Pa ndandanda ya sukulu pali mbali ziŵiri zosiyana za kuŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu. Imodzi ndi muyeso wa nkhani yoŵerenga Baibulo imene utali wake umakhala pafupifupi masamba asanu a Baibulo. Mfundo za Baibulo zimachokera pa kuŵerenga kumeneku. Kuŵerenga kwinako ndi kowonjezera kumene kumakhala kotalikirapo kuŵirikiza kaŵiri koyambako. Mwakutsatira zimenezi, mukhoza kumaliza kuŵerenga Baibulo lonse m’zaka zitatu. N’kodziŵikiratu kuti ena angafune kuŵerenga kuposa mmene zaikidwira m’mbali yowonjezeredwayi, ndipo ena sangakwanitse kuyendera nayo limodzi. M’malo modziyerekezera ndi ena, kondwerani ndi zimene mungakwaniritse. (Agal. 6:4) Chofunika kwambiri n’kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse.—Sal. 1:1-3.
4 Kuti mulembetse m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase, lankhulani ndi woyang’anira sukulu. Musaone nkhani imene mwapatsidwa mwachibwanabwana, ndipo musalephere wambawamba kuikamba. Itengeni sukuluyi monga makonzedwe ochokera kwa Yehova. Konzekerani bwino, khalani ozoloŵerana ndi nkhani imene mwapatsidwa, ndipo lankhulani kuchokera pansi pa mtima, motero mukumapindula kwambiri ndi sukulu yapaderayi.