Sukulu ya Utumiki Wateokalase ya 2001
1 Pali zifukwa zambiri za m’Malemba zosonyeza chifukwa chake tonsefe tiyenera kutengamo mbali mokwanira m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase.—Miy. 15:23; Mat. 28:19, 20; Mac. 15:32; 1 Tim. 4:12, 13; 2 Tim. 2:2; 1 Pet. 3:15.
2 Pulogalamu yoŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu yakhala mbali ya sukulu kwanthaŵi yaitali. Imakhala yokwanira kuŵerenga tsamba limodzi la Baibulo tsiku lililonse. Kuyambira chaka chino, mlungu uliwonse wa kubwereramo kolemba pazikhalanso kuŵerenga Baibulo. Ndandanda ya kuŵerenga Baibulo kowonjezera, imene yakhala ikuonekera pandandanda ya sukulu zaka zitatu zapitazi yatha. Koma ngati mukufuna kuŵerenga Baibulo kwambiri kuwonjezera pandandandayo, mukhoza kupanga ndandanda yanuyanu yoŵerenga.
3 Nkhani Na. 2 imaphunzitsa abale “kuŵerenga [poyera, NW]” Mawu a Mulungu. (1 Tim. 4:13) Ngati mwapatsidwa nkhani yoŵerenga, ikonzekereni mwa kuŵerenga mokweza mobwerezabwereza. Mukhoza kugwiritsa ntchito makaseti a Baibulo a Sosaite kuti muwongolere katchulidwe kanu ka mawu, kamvekedwe ka mawu, ndi mbali zina zofunika pa kuŵerenga kwabwino.
4 Nkhani Na. 3 ndi Na. 4 zizichokera mu buku la Kukambitsirana, limene linakonzedwa kuti lizigwiritsidwa ntchito muutumiki wakumunda. Ngati mfundo zake zili zochuluka zosati n’kukambidwa m’nthaŵi yoperekedwayo, sankhani mfundo zokhazo zimene zingagwire ntchito kwambiri m’gawo la mpingo wanu. Mungagwiritse ntchito njira iliyonse yaulaliki imene ili yoyenera m’gawo lanu.
5 Yesetsani kwambiri kukamba nkhani zonse zimene mwapatsidwa mu sukuluyi. Khalani ndi nthaŵi yokwanira kuti mukonzekere bwino, ndipo lankhulani kuchokera pansi pa mtima. Mudzakhala olimbikitsa kwambiri mu mpingo, ndipo inunso mudzapindula mwa kutengamo mbali ndi mtima wonse m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase mu chaka cha 2001.