Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/00 tsamba 3-4
  • Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
  • Nkhani Yofanana
  • Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Mabuku Athu Ofotokoza Baibulo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Bokosi La Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Kodi Likuoneka Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
km 12/00 tsamba 3-4

Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?

1 Diamondi komanso miyala ina ndi yamtengo wapatali osati kokha chifukwa chakuti ndi yokongola komanso chifukwa chakuti imafuna ndalama zambiri kuti aipeze ndi kuikumba. Chidziŵitso cha Yehova ndi Yesu Kristu n’chamtengo wapatali kwambiri kuposa zimenezi, ndipo ndi zofalitsa zathu zokha padziko lapansi zimene zimafotokoza chuma chauzimu chimenechi mwakuya ndi nzeru yaumulungu.—Aroma 11:33; Afil. 3:8.

2 Tangoganizirani zofalitsa zabwino kwambiri zimene tinalandira ku Msonkhano Wachigawo wakuti “Akuchita Mawu a Mulungu”—buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse, bulosha la Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu, ndi zofalitsa zina zimene analengeza kuti titha kuitanitsa. Zonsezi zili ngati diamondi wamtengo wapatali. Ndi zamtengo wapatali ndipo zitithandiza kum’dziŵa kwambiri Mulungu ndi zolinga zake. Kodi tingasonyeze motani kuti timayamikira zedi mabuku onseŵa?

3 Anthu ena ndi mabanja ena nthaŵi zonse amaika pambali ndalama zopita nazo ku Nyumba ya Ufumu kuti akaike mu limodzi la mabokosi lolembedwa kuti “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14.” Ndipo pamsonkhano wachigawo tinali ndi mabokosi a zopereka kaamba ka cholinga chomwechi. Kodi tinakumbukira kupereka kangachepe kuthandiza ntchito yapadziko lonse posonyeza kuyamika Yehova potipatsa zofalitsa zabwino zimenezi? Titha kupereka zowonjezereka za ntchito yapadziko lonse potenga mabuku kapena magazini ndiponso pokhutulira m’bokosi zopereka zimene talandira mu utumiki wakumunda.

4 Njira ina imene tingasonyezere kuyamikira ndiyo kusankha pogaŵira mabuku kwa anthu amene timakumana nawo mu utumiki wakumunda. Sitingapereke diamondi wokwera mtengo kwa mwana wosadziŵa kufunika kwake. Sitiperekanso mabuku athu amtengo wapataliŵa kwa anthu osayamikira zinthu zauzimu. (Yerekezani ndi Ahebri 12:16.) Kudzipereka kwathu mofunitsitsa ndiponso kupereka mabuku athu mooloŵa manja kuyenera kuchitika mozindikira. Kodi mwininyumba akufunitsitsa kulankhula nafe? Kodi akumvetsera tikamalankhula, kuyankha tikamam’funsa, ndiponso kuŵerenga nawo Baibulo tikamaŵerenga? Ngati akusonyeza chidwi choterocho, timasangalala kum’siyira chofalitsa choyenera. Tikamachititsa maphunziro mogwiritsa ntchito zofalitsa zathu, anthu amaphunzira zimene Baibulo limanena ndipo zimatsegula njira yopalana ubwenzi ndi Yehova. Phindu lenileni lopezeka m’mabuku athu limadalira mmene amagwiritsidwira ntchito.

5 Nthaŵi zonse lingalirani mosamala kuchuluka kwa mabuku amene mukufunikiradi okagaŵira m’munda. N’kofunika kulingalira bwino. Ngakhale n’kofunika kukhala ndi mabuku ambiri, makamaka ngati mukuchita upainiya, palibe chifukwa chosungira mabuku ambiri popeza mukhoza kukatenga ena ku Nyumba ya Ufumu misonkhano isanayambe ndiponso itatha. Khalani ndi mabuku okwanira kuchiyambi kwa mwezi ndipo katengeni ena akatha amene munatenga.

6 Komanso, kumbukirani kuti ngati njira yatsopano yogaŵira mabuku mu utumiki wakumunda sitikuifotokoza bwino, pambuyo pake ena zimawavuta kuwongolera mawu kapena njira zimene azoloŵera kugwiritsa ntchito. Ena apatsa anthu malingaliro akuti mabuku amene tikugaŵira panopa ndi aulere ndipo kwakhala kovuta kuwongolera malingaliro otereŵa. Pamafunika ndalama kuti tigule mapepala, kusindikiza ndi kuwatumiza padziko lonse lapansi ndiponso ntchito yotembenuzira m’zinenero pafupifupi 350. Choncho, ofalitsa ayenera kuuza eninyumba kuti timapereka mabuku popanda kuwauza kuti apereke ndalama mwakuti koma timayamikira kulandira zopereka zawo zaufulu.

7 Nazi zina mwa mfundo zimene zingatithandize kukwaniritsa udindo wathu wothandiza ntchito yapadziko lonse ndi kusonyeza kuyamikira mabuku athu.

8 Kodi ndalama zochirikiza ntchito ya Sosaite yapadziko lonse, kuphatikizapo kusindikiza ndi kugaŵira mabuku ake, zimapezeka bwanji?

Mabokosi olembedwa kuti, “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse.—Mateyu 24:14” amapezeka pafupi ndi potengera magazini ndi mabuku. Ndalama zoponyedwa m’mabokosi ameneŵa zimatumizidwa ku Sosaite mwezi uliwonse. Ndalama zimenezi zimagwira ntchito yolipirira ntchito zonse za Sosaite, kuphatikizaponso kuthandiza kufutukuka kwa ntchito kofunika padziko lonse.

9 Makonzedwe opepukitsidwa a kagaŵiridwe ka mabuku akuthandiza tonsefe kuona kuti ntchito yathu yophunzitsa Baibulo si malonda ayi. Mosiyana kwambiri ndi mabungwe “opemphapempha ndi kuthandiza osauka,” timasangalala kuona kuti anthu achidwi onse angalandire mabuku popanda kuwauza kuti apereke ndalama mwakuti. Kungakhale bwino kukumbutsa anthu kuti zopereka zonse zimene timalandira m’munda ndi za m’mabokosi olembedwa kuti “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse.—Mateyu 24:14,” zimachirikiza ntchito yophunzitsa Baibulo, popeza antchito onse m’gulu limeneli ndi odzifunira ndipo palibe amene amalipidwa kapena kulandira chiwongola dzanja.

10 Kodi Sosaite imatha bwanji kumapereka mabuku kwa anthu onse popanda kuwauza kuti apereke ndalama mwakuti? Ndalama zimene mosapeŵeka zimawonongeka popanga ndiponso potumiza mabuku zimalipiridwa ndi zopereka zaufulu. Atumiki odzipatulira a Yehova ndiwo gwero lalikulu la chichirikizo chimenechi. Mboni za Yehova sizipempha anthu kuwathandiza ntchito yofunika kwambiri imeneyi yolengeza ufumu. Sitinapemphetsepo ndalama kwa anthu. Koma, ndalama zochepa chabe zochokera kwa anthu achidwi chenicheni ndiponso oyamikira amene timakumana nawo m’munda timaziyamikira.

11 Kodi sitikupereka “kaŵiri za mabuku” ngati tiponya ndalama m’bokosi la ntchito ya Sosaite potenga mabuku, ndipo kenako n’kudzaponyamonso zimene talandira m’munda?

Ayi. Ndalama zimene timaponya m’mabokosi a zopereka za ntchito ya Sosaite yapadziko lonse sikuti ndi “za mabuku” okha. Ofalitsa ndiponso anthu osonyeza chidwi chenicheni m’munda amalandira mabuku popanda kuwauza kuti apereke ndalama mwakuti. Ndalama zimene ofalitsa amapereka n’zochirikizira makonzedwe onse a ntchito ya Ufumu. Kufalitsa mabuku ndi mbali yochepa chabe ya ntchito imeneyi. N’chifukwa chake pamene anthu osonyeza chidwi chenicheni apereka ndalama sitiyenera kuwauza kuti zopereka zawo ndi “za mabuku,” chifukwa chakuti monga momwe timawauzira, amene asonyeza chidwi choŵerenga angawalandire popanda kuwauza kuti apereke ndalama mwakuti. Ndalama zilizonse zimene angafune kupereka zidzagwira ntchito yolipirira zomwe zawonongedwa pantchitoyi m’dziko mwawo. Chimodzimodzinso ndi zopereka za ofalitsa.

12 Kodi ofalitsa ndiponso apainiya ayenera kukakamizika kupereka ndalama za ntchito ya Sosaite nthaŵi zonse potenga mabuku m’Nyumba ya Ufumu?

Ayi. Ofalitsa angapange zopereka zawo kuchirikiza ntchito ya Ufumu pamene akufuna malinga ndi mikhalidwe yawo. (2 Akor. 8:10-15; 9:6-14) Ena azitha kupereka ndalama akamatenga mabuku. Zimenezi zidzawathandiza kusaiŵala mwayi ndi udindo wawo wochirikiza ntchitoyi mokhazikika. Ena angamapereke zopereka zawo pamene akuponya ndalama zomwe alandira kwa anthu amene alankhula nawo muutumiki wakumunda. Ambiri angasankhe kumapereka ndalama mwakuti mlungu uliwonse, pomwe ena pamwezi angamaike ndalama zina padera kaamba ka ntchito ya uthenga wabwino, monga amachitira ndi ndalama zothandiza pa Nyumba ya Ufumu. Zilibe kanthu kuti amachita liti zimenezi, koma aliyense ayenera kusankha zimene angapereke payekha kuti achirikize ntchitoyi. Zopereka zimenezo ziyenera kuchitidwa mwadongosolo malinga ndi kupeza kwa munthu. (1 Akor. 16:2) Popereka ndalama zimenezi, tiyenera kukumbukira kuti sitikupereka n’cholinga cholipirira mtengo wa mabuku wokha, koma kuchirikiza ntchito yonse. N’zoona, ngati tatenga mabuku akuti ifeyo tigwiritse ntchito, tidzimve kuti ndi udindo wathu wopereka ndalama.

13 Tiyenera kudziŵa kuti ngakhale timagaŵira mabuku athu kwa anthu osonyeza chidwi popanda kuwauza kuti apereke ndalama mwakuti, pamawonongedwa zambiri popanga ndi kufalitsa mabuku athu. Tikukhulupirira kuti mzimu wa Mulungu uzisonkhezera atumiki Ake ndiponso anthu achidwi m’munda kumapereka mwaufulu kuti tizilipirira mitengo imeneyi ndiponso mitengo ya zina zonse zokhudza ntchitoyi.

14 Pamene mwininyumba wapereka ndalama zochuluka, kodi tiyenera kukakamizika kum’patsa mabuku owonjezereka?

Si choncho ayi. Tikubwerezanso kuti, ndalamazo ndi za ntchito yapadziko lonse, si zolipirira mabuku omwe timagaŵira popanda kuwauza mtengo. M’maulendo ena otsatira tingam’siyire mabuku amene angathandize mwininyumba pavuto linalake popanda kum’tchulira nkhani ya zopereka. Inde, ngati mwininyumbayo wangoganiza yekha kuti apereke ndalama zina, tilandire moyamikira. Tiyenera kukumbukira kuti ndalamazo zidzathandiza mbali zosiyanasiyana za ntchito yathu.

15 Zofalitsa zathu zimakhala zaphindu kwambiri tikazipereka kwa anthu oyamikira Mawu a Mulungu a choonadi. Choncho tonsefe tikhaletu anzeru ndi ozindikira pogwiritsa ntchito zimene tapatsidwa, motero tikumasonyeza kuti timayamikira kwambiri mabuku athu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena