Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1998
Kulangiza kumatanthauza “kuphunzitsa kapena kukhomereza m’maganizo chidziŵitso kapena luso lina.” Timaphunzitsidwa nthaŵi zonse chidziŵitso cha Mulungu kupyolera m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Ndiponso, potengamo mbali m’sukuluyi, timakulitsa maluso athu olankhula ndi kuphunzitsa. Programu ya sukulu ya 1998 idzatipatsa mipata yambiri yopitira patsogolo mwauzimu.
Popenda ndandanda ya sukulu ya chaka chamaŵa, mudzaona kuti nthaŵi ndi nthaŵi, Nkhani Na. 3 idzachokera m’buku la Chidziŵitso. Ndiponso, pamabuku ophunzira mu 1998, tawonjezerapo buku la Chimwemwe cha Banja, ndi kabuku ka Mitu ya Nkhani ya Baibulo Yokambitsirana, ndiye mabukuwo aziphunziridwa pang’onopang’ono pa Nkhani Na. 3 ndi Na. 4. Ngati Nkhani Na. 4 yachokera m’buku la Chimwemwe cha Banja, mbale woisamalira aikambire mpingo. Chikumbutso nchakuti pasakhale aliyense paprogramu ya sukulu yemwe adzadya nthaŵi.
Mbali Yatsopano: Kuti tipindule kwambiri, palinso “Ndandanda Yowonjezera ya Kuŵerenga Baibulo” m’mabulaketi pambuyo pa nambala ya nyimbo ya mlungu uliwonse. Ngakhale kuti programu ya sukulu ya mlungu ndi mlungu sinazikidwa pa ndandandayo, tsimikizanibe kuitsatira. Zimenezo zidzakuthandizani kuzoloŵera kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ngati simunayambe kale kutero.
Kuti mudziŵe zambiri ponena za nkhani, uphungu, ndi kupenda kolemba, chonde ŵerengani mosamalitsa malangizo omwe ali mu “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1998,” ngakhalenso patsamba 3 la Utumiki Wathu Waufumu wa October 1996.
Ngati simunadzilembetsebe m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki, tikukulimbikitsani kudzilembetsa tsopano. Sukulu yapadera imeneyi idakachita mbali yofunika pakuphunzitsa atumiki a Yehova odzichepetsa ndi odzipereka kuti akhale atumiki ake okhoza bwino.—1 Tim. 4:13-16.