Kubwereramo Kolemba M’sukulu ya Utumiki Wateokalase
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa September 6 kufikira December 20, 1999. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso n’ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. Yehova walola anthu kulamulira modziimira paokha kuti asonyeze kuti njira Yake yolamulira n’njabwino ndipo yolungama nthaŵi zonse. (Deut. 32:4; Yobu 34:10-12; Yer. 10:23) [w97-CN 2/15 tsa. 5 ndime 3]
2. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu amatsutsa kudandaula kulikonse. [w97-CN 12/1 tsa. 30 ndime 3-4]
3. Makolo amalemekeza ana awo okwatira kapena okwatiwa, mwa kusaswa malamulo a Mulungu pankhani ya umutu ndi kuchita zinthu molongosoka. (Gen. 2:24; 1 Akor. 11:3; 14:33, 40) [fy-CN tsa. 164 ndime 6]
4. Marko 6:31-34 amasonyeza kuti Yesu anali kuchitira chifundo makamu a anthu chabe chifukwa chakuti anali odwala ndi osauka. [w97-CN 12/15 tsa. 29 ndime 1]
5. Ngati Mkristu wa nkhosa zina walephera kukhala nawo pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu, ayenera kuchita phwandolo patapita mwezi, mogwirizana ndi mfundo ya pa Numeri 9:10, 11. (Yoh. 10:16) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 2/1 tsa. 31 ndime 9.]
6. Ngakhale kuti agogo achikristu samatengeratu udindo wa bambo ndi mayi wakuphunzitsa ana awo choonadi cha Baibulo, agogowo ntchito yawo ingakhale yothandizira kuti mwana akule bwino mwauzimu. (Deut. 6:7; 2 Tim. 1:5; 3:14, 15) [fy-CN tsa. 168 ndime 15]
7. Miyambo 6:30 imasonyeza kuti kuba kungakhale kopanda mlandu komanso koyenera m’mikhalidwe ina. [g97-CN 11/8 tsa. 21 ndime 2]
8. Mu 1530, William Tyndale ndiye anali woyamba kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova, potembenuzira Malemba Achihebri m’Chingelezi. [w97-CN 9/15 tsa. 28 ndime 3]
9. Lero, mzinda wophiphiritsira wothaŵirako ndiwo njira ya Mulungu yotitetezera ku imfa chifukwa choswa lamulo lake pankhani ya kupatulika kwa magazi. (Numeri 35:11) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 11/15 tsa. 17 ndime 8.]
10. Mbale sayenera kum’lipiritsa chiwongola dzanja. (Lev. 25:35-37) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 2/15 tsa. 30.]
Yankhani mafunso otsatiraŵa:
11. Kodi mikate iŵiri yokhala ndi chotupitsa imene mkulu wansembe anali kupereka pa Phwando la Pentekoste inali kuimiranji? (Lev. 23:15-17) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w98-CN 3/1 tsa. 13 ndime 21.]
12. Kodi Chaka Choliza Lipenga chachikristu chinayamba liti, ndipo chinapatsa anthu ufulu wotani panthaŵi imeneyo? (Lev. 25:10) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 5/15 tsa. 24 ndime 14.]
13. N’chifukwa chiyani panaperekedwa chilango cha imfa kwa aliyense “wakutemberera” makolo ake? (Lev. 20:9) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 2/15 tsa. 29-30.]
14. Kodi Mose anasonyeza mwa njira iti yabwino kwambiri kuti analibe mzimu wa nsanje? (Num. 11:29) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 9/15 tsa. 18 ndime 11.]
15. Kodi nkhani ya Kora, Datani, ndi Abiramu imasonyeza bwanji kuti si nthaŵi zonse kuti munthu akaona chinthu m’pamene amakhulupirira? [w97-CN 3/15 tsa. 4 ndime 2]
16. Kodi Mateyu 15:3-6 ndi 1 Timoteo 5:4 akusonyeza mfundo ziŵiri ziti za kulemekeza makolo okalamba? [fy-CN mas. 173-5 ndime 2-5]
17. Kodi ndi phunziro lofunika lotani limene likugogomezedwa pa Numeri 26:64, 65? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani g95-CN 8/8 mas. 10-11 ndime 5-8.]
18. Kodi chitsanzo cha Pinehasi chimatithandiza bwanji kuzindikira zimene kudzipatulira kwa Yehova kumatanthauza? (Num. 25:11) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN tsa. 16 ndime 12-13.]
19. Kodi munthu wokhala m’mudzi wophiphiritsira wopulumukiramo, ‘angalumphe bwanji malire’ a mudziwo? (Num. 35:26) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w95-CN 11/15 tsa. 20 ndime 20.]
20. Kodi Codex Sinaiticus inakhala bwanji dalitso pakutembenuza Baibulo? [w97-CN 10/15 tsa. 11 ndime 2]
Pezani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Yehova walola kuipaku kupitirizabe kuti potsirizira adzasonyeze kuti iye yekha ndiye ․․․․․․․ ndi kutinso anthu ake onse angakhale ndi mtendere ndi chimwemwe chosatha ngati ․․․․․․․ malamulo ake. (Sal. 1:1-3; Miy. 3:5, 6; Mlal. 8:9) [w97-CN 2/15 tsa. 5 ndime 4]
22. Pamene wina m’banja achitira mnzake nkhanza, ․․․․․․․ amene ayenera kukakamiza wosalakwayo kupatukana ndi mnzakeyo kapena kukhalabe naye. [fy-CN tsa. 161 ndime 20]
23. Mogwirizana ndi Salmo 144:15b, chimwemwe chenicheni ndi mkhalidwe wa mumtima, munthu amakhala nacho ngati ali ndi ․․․․․․․ chenicheni ndi ․․․․․․․ wabwino ndi Yehova. [w97-CN 3/15 tsa. 23 ndime 7]
24. Baibulo limene linatembenuzidwira m’Chigiriki chofala, lomwe linamalizidwa cha mu 150 B.C.E., linatchedwa kuti ․․․․․․․ lotembenuzidwira m’Chilatini ndi Jerome linatchedwa kuti ․․․․․․․, lomwe linamalizidwa cha mu 400 C.E. [w97-CN 8/15 tsa. 9 ndime 1; tsa. 10 ndime 4]
25. Baibulo limamasulira mawu akuti ․․․․․․․ pa Numeri 35:20, 21. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani g74 5/8 tsa. 27.]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Kamodzi pachaka, pa (Phwando Lamisasa; Tsiku Lachitetezo; Paskha), mtundu wonse wa Aisrayeli, pamodzi ndi alendo omwe anali kulambira Yehova, anali kufunikira (kuleka kugwira ntchito iliyonse; kupereka chakhumi; kupereka nsembe ya zipatso zoundukula) ndiponso kusala kudya. (Lev. 16:29-31) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 7/1 tsa. 10 ndime 12.]
27. Chimodzi cha zolinga za Komiti Yotembenuza Baibulo la New World, chinali chakuti atembenuze (mofanana ndithu liwu ndi liwu; chinenero choyambacho m’mawu ena; mogwirizana ndi mmene amadziŵira chiphunzitso chakutichakuti) kuti athandize woŵerenga kumvetsetsa kalankhulidwe ka zinenero zoyambazo ndi mmenenso anthu ake anali kuganizira. [w97-CN 10/15 tsa. 11 ndime 5]
28. Malinga ndi Ahebri 13:19, kupempherera okhulupirira anzathu mosalekeza kumakhudza (pa zimene Mulungu walolera kuchitika; nthaŵi pamene Mulungu angachitepo kanthu; mmene Mulungu angayendetsere zinthu). [w97-CN 4/15 tsa. 6 ndime 1]
29. “Mphonje [yobiriŵira] m’mphepete mwa zovala” za Aisrayeli inali yofunika monga (chokometsera chopatulika; chizindikiro cha kudzichepetsa; chikumbutso chooneka chowakumbutsa kulekana ndi dziko monga anthu a Yehova). (Num. 15:38, 39, NW) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w83 10/15 tsa. 20 ndime 16.]
30. Mwachionekere ‘kuzunza moyo’ kumatanthauza ( kusala kudya; kudzimenya; kupeŵa zosangalatsa zamtundu uliwonse). (Lev. 16:29, NW) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w84 2/15 tsa. 29.]
Gwirizanitsani malemba otsatiraŵa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa:
Num. 16:41, 49; Mat. 19:9; Luka 2:36-38; Akol. 2:8; 3:14.
31. Kudzimana konyanya sikuchititsa munthu kukhala woyera mwapadera kapena kupeza nzeru yeniyeni. [g97-CN 10/8 tsa. 13 ndime 4]
32. Chigololo ndicho chifukwa chokha chimene Malemba amalola munthu kusudzula mnzake n’kukwatiranso ngati afuna. [fy-CN mas. 158-9 ndime 15]
33. Kukhala wokangalika pantchito zateokalase, ngakhale m’zaka zaukalamba, kungam’thandize munthu kupirira atafedwa mwamuna wake kapena mkazi wake. [fy-CN 170-1 tsa. 21]
34. Kung’ung’udzira Yehova chifukwa cha njira yake yochitira chilungamo mwa kugwiritsa ntchito atumiki ake omwe waika kungaloŵetse munthu m’vuto. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 6/15 tsa. 21 ndime 13.]
35. Chikondi chopanda dyera chimamangirira mwamuna ndi mkazi, ndipo chimawapangitsa kufuna kuchitirana zabwino kwambiri ndi kuchitiranso ana awo zabwino. [fy-CN tsa. 187 ndime 11]
S-97-CN Zam, Mal & Moz #299 12/99