Mbiri Yateokratiki
Angola: M’mwezi wa December, chiwonkhetso cha magazini ogaŵiridwa chinawonjezeka kuposa pa 10,000, chiŵerengero chapamwamba kuposa chapapitapo. Ofalitsa 21,965 akuchititsa maphunziro a Baibulo 60,691.
Equatorial Guinea: Ofalitsa 219 anasangalala ndi programu yawo ya tsiku la msonkhano wapadera m’December. Panali chiŵerengero chapamwamba cha ofikapo 521 ndipo 7 anabatizidwa.
Guatemala: Ofalitsa 13,243 m’December anakondwera kuona anthu okwanira 32,911 akufika pa Misonkhano yawo Yachigawo ya “Chiphunzitso Chaumulungu.” Panali 597 amene anabatizidwa pamisonkhano imeneyo.
Latvia: Ntchito ikupitabe patsogolo ku Latvia. M’December wapitayo chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 577 chinachitira lipoti. Maphunziro a Baibulo apanyumba okwanira 1,816 anachititsidwa, ndipo ofalitsa ampingo anagaŵira magazini 20.5 pa avareji.