Thandizani Ena Kudziŵa Kufunika kwa Baibulo
1 Yesu anapereka zimene ophunzira ake anafunikira. Luka 24:45 amati: “Anawatsegulira mitima yawo, kuti adziŵitse Malembo.” Anadziŵa kuti ngati anafuna kukhala ndi chivomerezo cha Atate wake, kunali kofunika kuti iwo aphunzire ndi kumvetsa Mawu a Mulungu, Baibulo. (Sal. 1:1, 2) Ntchito yathu ya kulalikira ili ndi chifuno chimodzimodzicho. Chonulirapo chathu ndicho kuyambitsa maphunziro a Baibulo, kumene ‘tingaphunzitse anthu kusunga zinthu zonse zimene Yesu analamulira.’ (Mat. 28:20) Polingalira zimenezi m’maganizo, zotsatirapozi ndi njira zina zimene zingakhale zothandiza pamene mupanga maulendo obwereza.
2 Ngati poyamba munakambitsirana za buku lakuti “Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?” mungapitirize makambitsirano anu motere:
◼ “Ndingakonde kukusonyezani chinachake chimene chimasonyeza kufunika kwenikweni kwa uphungu wa Baibulo. Anthu ambiri amakuona kukhala kovuta kugwirizana ndi ena. Kodi tingachitenji kuti tikulitse mayanjano abwino ndi anansi athu? [Pambuyo pa yankho, tsegulani pamasamba 167-8, ndime 15, ndi kuŵerenga Mateyu 7:12. Wonjezeranipo malingaliro otchulidwa m’ndime 16.] Ichi nchitsanzo china cha nzeru yopezeka mu uphungu wa Baibulo. Ndikadzafikanso, ndidzakusonyezani uphungu umene Baibulo limapereka kuthandiza okwatirana kupeza chimwemwe chokulirapo mu unansi wawo.” Pangani makonzedwe a kudzabweranso kudzakambitsirana masamba 170-2, amene amasonyeza zimene Baibulo limanena kaamba ka moyo wabanja wachimwemwe.
3 Ngati munalankhulapo kwa winawake amene anachita chidwi ndi Baibulo, mwinamwake mafikidwe awa angakhale ogwira ntchito kuyambitsa phunziro:
◼ “Mwachionekere onse amene mumalankhula nawo adzakuuzani kuti angakonde kukhala m’dziko lamtendere ndi lachisungiko. Ngati izo ndizo zimene aliyense amafuna, kodi nchifukwa ninji tili ndi dziko lodzaza chipwirikiti ndi chiwawa? [Yembekezerani yankho.] New World Translation imakusonyezani pamene mungapeze yankho la funsolo m’Baibulo.” Tsegulani patsamba 1659, ndi kusonyeza “Bible Topics for Discussion” No. 43a, “Who is responsible for world distress.” Ŵerengani 2 Akorinto 4:4. Fotokozani mmene Mulungu adzawonongera Mdyerekezi ndi kudzetsa dziko lamtendere ndi chimwemwe zamuyaya. Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4. Ndiyeno munganene kuti: “Pamene ndidzafikanso, ndidzakusonyezani malemba amene amafotokoza chifukwa chake mungayembekezere dziko lopanda mavuto.”
4 Ngati munagwiritsira ntchito njira yolunjika kuyambitsa phunziro ndipo munthuyo anali wokondweretsedwa, munganene izi pamene mubwerera:
◼ “Pamene tinakambitsirana ulendo uja, tinakambitsirana zina za chifukwa chake kuphuzira Baibulo kuli kopindulitsa. Kuyesayesa kuchita zochuluka za zimenezi kungatithandize kudziŵa zimene Mulungu watisungira. [Ŵerengani Yohane 17:3.] Tinapanga programu yophunzira Baibulo imene yathandiza ambiri kuphunzira zochuluka ponena za zimene Mulungu walonjeza ndi mmene tingamkondweretsere.” Sonyezani buku la Knowledge, sonyezani mitu yake, ndipo sonyezani mmene timachititsira phunziro la Baibulo.
5 Ngati mungathandize anthu oona mtima kudziŵa kufunika kopambana kwa Mawu a Mulungu, mudzawathandiza m’njira yabwino koposa. Nzeru imene angaphunzire mwa kuphunzira m’masamba ake ingakhale “mtengo wa moyo,” umene udzawabweretsera chimwemwe chochuluka.—Miy. 3:18.