Pitirizanibe Kulankhula Choonadi
1 Atumwi anati: “Sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Lerolino ifenso tiyenera kupitirizabe kulankhula choonadi. Ngakhale kuti kugaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kuli njira yopezera awo amene adzamvetsera, tiyenera kubwererako ngati tikufuna kuphunzitsa okondwerera choonadi chowonjezereka.
2 Pamene mwabwerera kumene munasiya “Galamukani!” wa May wapadera ndi nkhani yake yakuti “Pamene Sikudzakhalanso Nkhondo,” mungayambitse phunziro la Baibulo mwa kufunsa kuti:
◼ “Paulendo woyamba, tinalankhula za nkhondo za mitundu ndi mbali ya chipembedzo mu izo. Kodi mwazindikira kuti zochitika zimenezi zikusonyeza bwino lomwe kuti tikukhala mu amene Baibulo limatcha masiku otsiriza? [Sonyezani buku la Knowledge. Ŵerengani ndime yoyamba ya mutu 11, ndipo sonyezani nsonga zimene zilipo m’bokosi patsamba 102.] Bukuli limafotokoza nkhani imeneyi pamodzi ndi zinanso 18 zondandalikidwa pano pa zamkatimu. [Sonyezani tsamba 3.] Ngati zili bwino, ndingakonde kukusonyezani mmene bukuli lingakuthandizireni kumvetsetsa nkhani zofunika zimenezi za Baibulo.” Ngati akulolani, yambani phunziro patsamba 6.
3 Ngati munali mutalonjeza kuti mudzabwererako kukafotokoza mmene kulili kotheka kukhala ndi moyo wosungika tsopano, munganene zonga izi:
◼ “Pamene tinakumana nthaŵi yoyamba, ndinaŵerenga ndi inu mbali ina m’Baibulo imene imatipatsa chifukwa choyembekezera zabwino mtsogolo mwa anthu. Lero ndikufuna kukusonyezani chinachake chimene chimasonyeza amene angatipatse malingaliro achisungiko tsopano lino.” Ŵerengani Salmo 4:8. Tsegulani buku la Knowledge patsamba 168 ndipo ŵerengani ndime 19. Ndiyeno funsani kuti: “Kodi mungakonde kukhala ndi phunziro la Baibulo lapanyumba laulere limene limasonyeza bwino lomwe mmene inunso mungapezere chisungiko chotere m’moyo wanu?” Ngati yankho ndi lakuti inde, pitani pa mutu 1.
4 Kuti muwonjezere awo amene munawagaŵira “Galamukani!” wa June 8 panjira yanu yamagazini, mungayese mafikidwe awa:
◼ “Munaoneka kukhala wofunitsitsa kuŵerenga magazini a Galamukani! amene ndinakusiyirani onena za nkhani ya kuvutitsidwa ndi amuna kapena akazi pamalo antchito. Kodi munapeza nkhani yake kukhala yokondweretsa? [Yembekezerani yankho.] Oŵerenga Galamukani! okhazikika kaŵirikaŵiri amanena kuti amayamikira kulankhula kwake kosapita m’mbali ndi kosamalitsa kwa nkhani zofunika zotere. Ndiyesa mudzaonanso zimenezo kukhala zoona ponena za kope ili laposachedwapa. [Mwachidule fotokozani nkhani yapachikuto.] Kodi mungakonde kuliŵerenga?”
5 Mungapemphe mwachindunji kuphunzira nawo paulendo wobwereza mwa kunena kuti:
◼ “Timagaŵira magazini athu padziko lonse lapansi kuti tidziŵitse anthu kulikonse zimene Baibulo limaphunzitsa. Ngati ena aona kuti zimene akuphunzira nzofunika, timapempha kuchita nawo phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. [Sonyani ku bokosi lakuti ‘Kodi Mungakonde Kuchezeredwa?’ kuchikuto chakumbuyo kwa Nsanja ya Olonda.] Timagwiritsira ntchito bukuli lakuti, Knowledge That Leads to Everlasting Life, monga chitsogozo. Tandilolani ndikusonyezeni mwachidule mmene phunziro lamachitikira.”
6 Ngati tipitirizabe kulankhula choonadi, tingatsimikizire kuti padzakhala ena amene adzamvetsera ndi kulabadira.—Marko 4:20.