Athandizeni Kuyambanso Kutumikira
1 Pozindikira ngozi yauzimu kwa Akristu anzake, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tsopano ndiyo nthaŵi yabwino yakuuka kutulo; pakuti tsopano chipulumutso chathu chili pafupi koposa pamene tinayamba kukhulupira.” (Aroma 13:11) Paulo anadera nkhaŵa za abale ake amene anali kuwodzera mwauzimu; iye analakalaka kuwatsitsimulanso ku ntchito.
2 Tikhoza kunenanso kuti usiku wa dziko lakaleli wapita ndipo mbandakucha wa dziko latsopano uli pafupi kwenikweni. (Aroma 13:12) Tili ndi chifukwa chabwino chokhalira odera nkhaŵa za abale athu omwe aleka kuyanjana nafe monga alaliki a uthenga wabwino. Chaka chautumiki chathachi, ofalitsa ambiri anayambitsidwanso m’Malaŵi. Kodi tingawathandize motani enanso ofooka kuyambanso kutumikira Yehova?
3 Zimene Akulu Angachite: Ofooka ambiri sanasiye choonadi ayi; angoleka kulalikira chifukwa cha kulefuka, mavuto aumwini, kukondetsa chuma, kapena nkhaŵa zina za moyo. (Luka 21:34-36) Ngati kuli kotheka, ndi bwino kwambiri kuwathandiza asanafooke. Mlembi wa mpingo ayenera kudziŵitsa wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo pamene wofalitsa ayamba kuphonya kuchitira lipoti ntchito yake yautumiki. Makonzedwe angapangidwe a ulendo waubusa. Ayenera kuyesa kudziŵa chochititsa vutolo ndi mmene angathandizire.—Onani Nsanja ya Olonda ya September 15, 1993, masamba 20-3.
4 Mmene Ena Angathandizire: Ambiri a ife timadziŵa munthu amene wafooka. Angakhale munthu amene anali bwenzi lathu kwambiri kumbuyoku. Kodi tingachitenji kuti timthandize? Bwanji osamchezera mwachidule. Muuzeni kuti mukulakalaka kukhala naye. Khalani wachisangalalo ndi wolimbikitsa. Sonyezani nkhaŵa yanu mosasonyeza kuti iye ali wodwala mwauzimu. Simbani zokumana nazo zolimbikitsa kapena zinthu zina zabwino zimene mpingo wachita. Mwachisangalalo, muuzeni za Msonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu,” ndipo mlimbikitseni kudzapezekapo. Kuyambanso kuyanjana ndi mpingo nkumene kungamthandize kwambiri kuposa china chilichonse. Dziperekeni kupita naye pamodzi kumisonkhano. Dziŵitsani akulu za mmene anachitira.
5 Pamene wina wofooka ayambanso kusonkhana, angachite manyazi poonana ndi ena amene anawadziŵa kumbuyoku. Musafunse kuti, “Kodi munali kuti?” M’malo mwake, mchititseni kudzimva wolandiridwa. Mloŵetseni m’makambitsirano. Mdziŵikitseni kwa amene samawadziŵa. Khalani naye pamodzi pamsonkhano, ndi kuona kuti ali ndi buku la nyimbo ndi chofalitsa chimene chikuphunziridwa. Mlimbikitseni kubweranso, ndipo funsirani kupereka chithandizo ngati chili chofunikira.
6 Pokhala ndi chikondi kwa osokera, Yehova ndi Yesu amakondwera pamene oterowo achira mwauzimu. (Mal. 3:7; Mat. 18:12-14) Tingakhale ndi chisangalalo chimodzimodzicho ngati tipambana pakuthandiza ena kuyambanso kutumikira Yehova.