Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/97 tsamba 7
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu Ingatithandize Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Mmene Mungalinganizire Laibulale Yateokratiki
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Agwiritseni Ntchito, Osati Kungowasunga
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Makonzedwe Atsopano Okhudza Malaibulale a M’nyumba za Ufumu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 4/97 tsamba 7

Bokosi la Mafunso

◼ Kodi ndi zofalitsa zotani zimene ziyenera kuikidwa mu laibulale ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki?

Zofalitsa zauzimu zambirimbiri zaperekedwa kuti anthu a Mulungu apindule nazo. Popeza ofalitsa ambiri alibe zonse zimenezi zawozawo, laibulale ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki pa Nyumba ya Ufumu imawatheketsa kufufuza m’zofalitsa zimene mwina alibe. Ndiye chifukwa chake iyenera kukhala ndi ma Baibulo osiyanasiyana, zofalitsa zatsopano za Sosaite, makope a Utumiki Wathu Waufumu, mabaundi voliyumu a The Watchtower ndi Awake! ndi ma Watch Tower Publications Index. Ndiponso, dikishonale yabwino yamakono iyenera kukhalamo. Mainsaikulopediya, maatilasi, kapena mabuku a galamala ndi mbiri angakhale othandiza ngati alipo. Komabe, tiyenera kusumika kwambiri maganizo pazofalitsa zimene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka.—Mat. 24:45.

Tamva kuti kwina mabuku okayikitsa aikidwa mu laibulale ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Sikungakhale bwino kuikamonso mabuku a nthano, mabuku odzaza ndi maphunziro apamwamba ofufuza Baibulo, kapena mabuku a filosofi kapena kukhulupirira mizimu. Laibulale ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki iyenera kukhala ndi mabuku okhawo amene adzathandiza owagwiritsira ntchito kupitabe patsogolo mwauzimu.—1 Tim. 4:15.

Woyang’anira sukulu ndiye woyang’anira laibulale, ngakhale kuti mbale wina angaikidwe kuti azimthandiza kuisamalira. Iye ayenera kuona kuti laibulale ili ndi zofalitsa zatsopano mwa kuziikamo zimenezi zitangokhalapo. Buku lililonse liyenera kulembedwa moonekera mkati mwake pachikuto dzina la mpingo wake. Chaka ndi chaka, mabuku ayenera kuonedwa ngati pali lililonse lofunika kulikonza kapena kulisintha kuikamo lina.

Aliyense angachitepo kanthu kusamalira laibulale. Tiyenera kusamala mmene tikugwirira mabukuwa ndi kuwagwiritsira ntchito. Sitiyenera kulola ana kuwaseŵeretsa, ndiponso palibe amene ayenera kuwachonga. Chizindikiro chabwino chingaikidwe monga chokumbutsa kuti mabuku sayenera kuchotsedwa m’Nyumba ya Ufumu.

Pokhala kuti mipingo yatsopano ikupangidwa nthaŵi zonse, malaibulale ambiri ayenera kuti alibe zambiri. Ofalitsa ena amene ali ndi zofalitsa zathu zakale kwambiri mwina angafune kuzipereka ku mpingo. Akulu angafune kuoda mabaundi voliyumu a Watchtower osindikizidwanso a Sosaite. Mwa njirazi, laibulale ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki idzathandiza onse kufukula chuma chobisika cha Mawu a Mulungu, chimene chimapatsa chidziŵitso, nzeru, ndi kuzindikira.—Miy. 2:4-6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena