Makonzedwe Atsopano Okhudza Malaibulale a M’nyumba za Ufumu
Kwa zaka zambiri tsopano, mipingo padziko lonse yakhala ikupindula pogwiritsa ntchito laibulale yawo ya m’Nyumba ya Ufumu, imene kale inkatchedwa laibulale ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. M’mbuyomu, mpingo uliwonse umafunikira kukhala ndi laibulale yakeyake. Koma masiku ano, pali Nyumba za Ufumu zambiri zimene zikugwiritsidwa ntchito ndi mipingo iŵiri kapena kuposapo. Choncho, taona kuti ndi bwino kukhala ndi laibulale imodzi yokha yodzaza bwino ndi mabuku imene izigwiritsidwa ntchito ndi mipingo yonse imene imakumana m’Nyumba ya Ufumu imeneyo. Chinenero chilichonse chikhale ndi laibulale yakeyake imodzi.
Tikukhulupirira kuti zimenezi zithandiza kuti tikhale ndi malo ambiri komanso tisamawononge ndalama zambiri. Ndiponso, tikaphatikiza malaibulale a mipingo ingapo, tidzakhala ndi laibulale imodzi yokhala ndi mabuku okwanira bwino. Tikapezeka ndi mabuku ofanana aŵiri kapena kuposerapo pamene tikuphatikiza malaibulale athu, tisunge enawo kuti adzagwiritsidwe ntchito zikadzamangidwa Nyumba za Ufumu zina.
Pa Nyumba ya Ufumu iliyonse asankhe mbale mmodzi woti akhale woyang’anira laibulale. Zingakhale bwino mbale ameneyu atakhala mmodzi wa oyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Nthaŵi ndi nthaŵi, woyang’anira laibulale aziwonjezera mabuku ofunika mu laibulalemo, ndipo azilemba mooneka bwino m’kati mwa buku lililonse kusonyeza kuti ndi buku la ku laibulale ya m’Nyumba ya Ufumu. Kamodzi pa chaka kapena kuposerapo, azifufuza mu laibulalemo nkuona ngati mabuku onse alipo, komanso aziona ngati mabukuwa ali bwino. Mabuku a mu laibulale ya m’Nyumba ya Ufumu sayenera kutulutsidwa kunja.
Onse amene amasonkhana ndi mpingo amayamikira kwambiri pokhala ndi laibulale ya m’Nyumba ya Ufumu. Tiyeni tisonyeze kuti timaiyamikira posamalira mabuku ake komanso powagwiritsa ntchito kuchita kafukufuku wotithandiza “kum’dziŵadi Mulungu.”—Miy. 2:5.