Agwiritseni Ntchito, Osati Kungowasunga
Mipingo yambiri ili ndi mabuku akale ambiri amene anangounjikana. Bwanji osatengako mabuku ena kuti mukaike m’laibulale yanu ya mabuku athu? Mwina muli ndi kompyuta ndipo mukhoza kuwerenga mabuku ena akalewa mu Watchtower Library. Komabe ndi bwino kukhala ndi buku lenileni. Kodi munthu amene mukuphunzira naye Baibulo akupita patsogolo? Ngati ndi choncho, mulimbikitseni kuti apezeko mabuku akalewo kuti awasunge ndi kumawagwiritsa ntchito. Woyang’anira Sukulu ya Utumiki wa Mulungu azionetsetsa kuti waika mabuku akale amenewa mulaibulale ya pa Nyumba ya Ufumu. Mabuku amenewa sanathe ntchito. Kodi si bwino kuti ifeyo tiziwagwiritsa ntchito m’malo moti mpingo uzingowasunga penapake?