Mtsatireni Yesu Mosaleka
1 Panthaŵi ina Yesu anati: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake [“mtengo wake wozunzirapo,” NW], nanditsate Ine [mosaleka, NW]” (Mat. 16:24) Inde, tiyenera kulabadira mawu a Yesuwo. Tiyeni tipende zimene liwu lililonse la chiitano chakecho likuphatikizapo.
2 “Adzikane Yekha”: Pamene tipatulira moyo wathu kwa Yehova, timadzikana. Tanthauzo lenileni la liwu lachigirikilo lotembenuzidwa kuti “kudzikana” ndilo “kunena kuti iyayi.” Zimenezo zikutanthauza kuti timasiya mwaufulu zolinga zathu zaumwini, zikhumbo zathu, maubwino ndi zosangalatsa zadyera—tili otsimikiza kukondweretsa Yehova kwamuyaya.—Aroma 14:8; 15:3.
3 “Atenge Mtengo Wake Wozunzirapo”: Moyo wa Mkristu ndiwo moyo wonyamula mtengo wozunzirapo ndi wotumikira Yehova modzimana. Njira ina imene munthu angasonyezere mzimu wodzimana ndiyo mwa kugwira ntchito mwamphamvu mu utumiki. Pano tafikapa chaka chino, ofalitsa ambiri akhala akusangalala ndi ntchito yaupainiya wothandiza. Mwinamwake ndinu mmodzi wa iwo ndipo mungavomereze kuti madalitso omwe mumapezamo amaposa kwambiri kudzimana kumene mumachita. Aja amene samakwanitsa kutumikira monga apainiya othandiza kaŵirikaŵiri amalinganiza kuthera nthaŵi yochuluka pantchito yolalikira monga ofalitsa a mpingo. Ndi cholinga chimenecho, mipingo ina ikuyamba kukumana kwawo kwa utumiki wakumunda mofulumirapo ndi mphindi zoŵerengeka kuposa mmene anali kuchitira kale. Ena apeza zotulukapo zabwino kwambiri pamene asankha kufika ‘panyumba ina imodzi chabe’ kapena ‘kungowonjezera mphindi zoŵerengeka basi.’
4 Njira ina yosonyezera mzimu wodzimana ndiyo kudziikira nokha zolinga. Ena akhala apainiya okhazikika atalinganiza mosamala ndi kuwongolera ndandanda yawo. Ena asintha zochita zawo kuti adzipereke pautumiki wa pa Beteli kapena kuloŵa Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Ena asamukira kumalo ena kumene kukufunika kwambiri ofalitsa Ufumu.
5 “Nanditsate Ine Mosaleka”: Ngakhale kuti ophunzira a Yesu anakumana ndi ziyeso zambiri, changu ndi chipiriro chake mu utumiki chinawalimbikitsa. (Yoh. 4:34) Iwo anatsitsimuka mumzimu wawo mwa kungokhala nawo iyeyo ndiponso chifukwa cha uthenga wake. Nchifukwa chake aja amene anamtsatira anali ndi chimwemwe chenicheni. (Mat. 11:29) Mofananamo tiyeni tilimbikitsane wina ndi mnzake kuti tipirire pantchito yofunika kwambiri imeneyi yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira.
6 Tiyenitu tonsefe tilabadire chiitano cha Yesu choti tipitirize kumtsatira mwa kukulitsa mzimu wodzimana. Tikatero, tidzakhala ndi chimwemwe chachikulu tsopano ndiponso tingayembekezere kulandira madalitso aakulu kwambiri mtsogolomu.