Misonkhano Imafulumiza ku Ntchito Zabwino
1 Mbali ziŵiri zofunika za kulambira kwathu ndizo kupezeka pamisonkhano yampingo ndi kutengamo mbali mu utumiki wakumunda. Ziŵirizi nzogwirizana. Imodzi imalimbikitsa inzake. Misonkhano yachikristu imafulumiza ku ntchito zabwino, ndipo yabwino kopambana zonse ndiyo ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Aheb. 10:24) Titati tileke kupezeka pamisonkhano, mwamsanga tingalekenso kulalikira chifukwa palibe chimene chidzatifulumiza kutero.
2 Pamisonkhano ya mlungu ndi mlungu, timalandirapo malangizo auzimu okonzedwa kuti atisonkhezere kulalikira. Nthaŵi zonse imatikumbutsa za kufulumira kwa nthaŵi, kutisonkhezera kukauza ena uthenga wa Baibulo wopatsa moyo. Imatilimbikitsa ndi kutipatsa nyonga yopirira pantchito yolalikira. (Mat. 24:13, 14) Mwa kupeza mipata yoyankha pamisonkhano, timazoloŵera kwambiri kusonyeza ena chikhulupiriro chathu. (Aheb. 10:23) Mwa kulembetsa Sukulu Yautumiki Wateokratiki, timaphunzira kukhala atumiki ogwira mtima ndi kuwongolera maluso athu ophunzitsa.—2 Tim. 4:2.
3 Mmene Misonkhano Yautumiki Imatisonkhezerera Kulalikira: Tonsefe timalimbikitsidwa kuŵerenga nkhani za mu Utumiki Wathu Waufumu pasadakhale. Ndiyeno chidziŵitsocho chimaloŵa m’maganizo athu pamene tili pa Msonkhano Wautumiki ndi kuona maulaliki akusonyezedwa pa pulatifomu. Pamene tili mu utumiki wakumunda, timaganiza za Utumiki Wathu Waufumu uja, ndi kukumbukira maulaliki amene anasonyezedwa aja, ndiyeno timapereka umboni wogwira mtima. Ofalitsa ambiri akhala akuchita zimenezo.
4 Pambuyo pa Misonkhano Yautumiki, ena amapangana ndi anzawo kuyendera limodzi muutumiki. Ofalitsa amakhala akuzikumbukirabe mfundo zakumundazo ndipo amasonkhezereka kuyesa kuzigwiritsira ntchito chifukwa misonkhano imeneyi yawalimbikitsa kutengamo mbali m’ntchito yolalikira mlungu uliwonse.
5 Palibe chimene chingaloŵe m’malo mwa misonkhano yathu yachikristu, kumene timakumana ndi olambira anzathu ndi kusonkhezerana ku ntchito zabwino. Ngati tifuna kuti utumiki wathu uziyenda bwino, tiyenera kumapezeka pamisonkhano yampingo nthaŵi zonse. Tiyenitu tisonyeze kuti tikuyamikira makonzedwe abwino a Yehova ameneŵa mwa ‘kusaleka kusonkhana kwathu pamodzi.’—Aheb. 10:25.