Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/98 tsamba 7
  • Kuchitira Umboni mwa Khalidwe Labwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchitira Umboni mwa Khalidwe Labwino
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Nkhani Yofanana
  • “M’kamwa mwa Makanda”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Ntchito Zabwino Zimene Zimalemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Achinyamata Amene Akuwala Monga Zounikira
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • “Khalani Oyera Mtima”
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
km 6/98 tsamba 7

Kuchitira Umboni mwa Khalidwe Labwino

1 Mwa anthu alero ololera zoipawa, achinyamata ambiri amawononga moyo wawo mosasamala ndi mankhwala osokoneza bongo, chiŵereŵere, kupanduka, ndi chiwawa. Mosiyana ndi zimenezo, khalidwe lopereka chitsanzo la achinyamata abwino mumpingo wachikristu nlokondweretsa kuliona ndipo Yehova amaliona ngati kanthu kena kokongola ndithu. Khalidwelo limakhala umboni wamphamvu umene angakopere ena ku choonadi.—1 Pet. 2:12.

2 Zokumana nazo zambiri zimasonyeza kuti khalidwe labwino la achinyamata achikristu limakopa anthu openyerera. Mphunzitsi wina, ponena za Mboni ina yachinyamata yomwe inali m’kalasi mwake, anauza kalasi yonse kuti Mulungu wa mtsikana ameneyo, Yehova, ndiye Mulungu woona. Ananena zimenezo chifukwa khalidwe la mtsikana ameneyo nlaulemu nthaŵi zonse. Mphunzitsi winanso analembera Sosaite kuti: “Ndikufuna kukuyamikirani chifukwa cha khalidwe labwino la anyamata amene muli nawo m’chipembedzo chanu . . . Anyamata anu alidi chitsanzo chabwino. Amalemekeza anthu akuluakulu, ngaulemu, ndipo amavala modzilemekeza. Ndipotu amadziŵa mabaibulo awo! Tikamati chipembedzo ndiye nchimenecho!”

3 Mphunzitsi winanso anachita chidwi ndi khalidwe labwino la Mboni ina yazaka zisanu ndi ziŵiri, ya m’kalasi mwake. Mphunzitsiyo anakopeka ndi kudekha kwa mnyamatayo ndi umunthu wake wosangalatsa, womwe unamsiyanitsa kutalitali ndi anyamata ena onse. Mphunzitsiyo anachita chidwi ndi mtima wake wotsimikiza kugwiritsitsa chikhulupiriro chake, wosachita manyazi kuti angakhale wosiyana ndi ena chifukwa cha zimene amakhulupirira. Anaona kuti chikumbumtima cha mnyamatayo chinali chitaphunzitsidwa ndi kutinso anali kutha “kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Aheb. 5:14) Potsirizira, amayi wake mnyamatayo anakachezera mphunzitsiyo, ndipo anayamba naye phunziro la Baibulo. Patapita nthaŵi, mphunzitsiyo anabatizidwa ndipo kenako anadzakhala mpainiya wokhazikika!

4 Mnyamata winanso anachita chidwi ndi khalidwe labwino la Mboni ina pasukulu pawo. Mtsikanayo analidi wosiyana ndi ena—wodekha, wokonda kuphunzira, ndipo wovala mwaulemu nthaŵi zonse; ndiponso, anasiyana ndi atsikana ena, iye sankakonda kuseŵera ndi anyamata. Iye anaona kuti mtsikanayo anali kutsatira malamulo a Baibulo. Mnyamatayo anamfunsa mafunso onena za chikhulupiriro chake ndipo anachita chidwi ndi zimene anamva. Mnyamatayo anayamba kuphunzira, anadzabatizidwa, ndipo potsirizira anachita utumiki waupainiya mpaka utumiki wa pa Beteli.

5 Ngati muli Mkristu wachinyamata yemwe mukufuna kuchitira umboni wabwino kwa ena, muzisamala khalidwe lanu m’njira iliyonse. Musadzaleke kusamala khalidwe lanu mwa kutsanzira khalidwe ndi malingaliro olakwika a dzikoli, kapena njira yake ya moyo. Sonyezani chitsanzo chabwino mwa mawu anu, kavalidwe kanu, ndi kapesedwe kanu, osati kokha pamene muli mu utumiki wakumunda kapena pamisonkhano yampingo iyayi, komanso pamene muli kusukulu ndi pamenenso muli pamaseŵera. (1 Tim. 4:12) Mudzakhala ndi chifukwa chabwino chosangalalira pamene wina ayamba kukondwerera choonadi chifukwa chakuti mwakhala ‘mukuwalitsa kuunika kwanu’ mwa khalidwe lanu labwino.—Mat. 5:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena