Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/06 tsamba 8
  • Achinyamata Amene Akuwala Monga Zounikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achinyamata Amene Akuwala Monga Zounikira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Oonekera Monga Mauniko’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Kuŵalitsa Kuunika Kwathu Mopitiriza
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • ‘Muwalitse Kuunika Kwanu’
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Kuchitira Umboni mwa Khalidwe Labwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
km 1/06 tsamba 8

Achinyamata Amene Akuwala Monga Zounikira

1. Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti Akristu adzakhala osiyana kwambiri ndi anthu ena, ndipo kodi mawu amenewo akugwirizana bwanji ndi Akristu achinyamata masiku ano?

1 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndinu kuunika kwa dziko lapansi.” (Mat. 5:14, 16) Iwo anayenera kuonekera patali ngati mzinda umene uli pamwamba pa phiri, umene umanyezimira dzuwa likawala. Masiku ano, Akristu achinyamata ambiri ‘akuwala monga zounikira za dziko lapansi’ chifukwa cha khalidwe lawo labwino ndi kulalikira kwawo kwakhama.—Afil. 2:15; Mal. 3:18.

2. Kodi ndi njira zina ziti zimene mungathe kulalikira kwa aziphunzitsi ndi anzanu a m’kalasi mwanu?

2 ku Sukulu: Kodi mungalalikire bwanji kusukulu? Achinyamata ena amapezerapo mwayi pa zokambirana za m’kalasi pa nkhani zosiyanasiyana monga za mankhwala osokoneza bongo, zoti zinthu zamoyo zinachita kusandulika kuchokera ku zinthu zopanda moyo, ndi za Edzi. Atapatsidwa chimangirizo chonena za uchigawenga, mlongo wina anapezerapo mwayi wochitira umboni za Ufumu wa Mulungu, kuti ndiwo ungathetsedi mavuto a anthu. Aphunzitsi ake anagoma kwambiri ndi chimangirizo chakecho chomwe anachilemba moganizira bwino, ndipo izi zinam’patsa mwayi winanso wolalikira.

3. Kodi mungatani kuti muwalitse kuunika kwanu kusukulu chifukwa cha khalidwe lanu?

3 Njira ina yowalira monga zounikira ndiyo kukhala ndi khalidwe labwino ndiponso kuvala ndi kudzikongoletsa modzilemekeza. (1 Akor. 4:9; 1 Tim. 2:9) Ana asukulu ndiponso aphunzitsi akaona kuti ndinu wosiyana ndi ana anzanu, ena angathe kuchita chidwi ndi choonadi poona khalidwe lanu labwinolo ndipo angakuloleni kuwauza choonadi cha m’Baibulo. (1 Pet. 2:12; 3:1, 2) Kusonyeza khalidwe labwino kumavuta, koma Yehova angakudalitseni ngati mutasonyeza khalidwe lotere. (1 Pet. 3:16, 17; 4:14) Kuti anthu akhale ndi chidwi ndi uthenga wabwino, mungamawerenge mabuku ofotokoza za m’Baibulo panthawi yopuma kapena mabukuwo mungawasiye penapake pamene ena angathe kuwaona.

4. Kodi kulalikira kusukulu n’kopindulitsa m’njira zotani?

4 Kuwalitsa kuunika kwanu kusukulu kumalimbikitsa chikhulupiriro chanu ndipo mumanyadira kuti mukutumikira Yehova. (Yer. 9:24) Komanso kumakutetezani. Mlongo wina anati, “Phindu limodzi louza anzanga a kusukulu za chikhulupiriro changa n’lakuti iwo sandikakamiza kuchita zinthu zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena.”

5. (a) Kodi achinyamata ena akuwonjezera motani utumiki wawo? (b) Kodi inuyo muli ndi zolinga zotani zauzimu?

5 Kuwonjezera Utumiki: Njira ina imene achinyamata ambiri amawalitsira kuunika kwawo ndiyo kuwonjezera utumiki wawo. Atamaliza sukulu ya sekondale, mbale wina anasamukira ku dera limene kunalibe olengeza Ufumu ambiri. Mpingo umene anapitako unali waung’ono ndipo unali ndi mkulu mmodzi yekha. Mbaleyu analembera kalata mnzake n’kunena kuti: “Kuno ine ndikusangalala kwadzaoneni. Utumiki wa kuno n’ngokoma zedi. Tikafika pa khomo la munthu timatha kukhalapo mphindi 20 chifukwa anthu ambiri kunoko amafuna kuti unene zonse zimene ukufuna.” Mbaleyu anatinso: “Zikanakhala bwino zedi ngati wachinyamata aliyense akanachita zimene ndachita inezi kuti amve mmene ndikumvera inemu. Palibe chinthu china choposa kutumikira Yehova pogwiritsa ntchito china chilichonse chimene tili nacho.”

6. Kodi achinyamata a mumpingo mwanu mumawanyadira chifukwa chiyani?

6 Achinyamata amene mukuwala monga zounikira za dziko lapansi timakunyadirani kwambiri. (1 Ates. 2:20) Mukamatumikira Yehova ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, nzeru zanu zonse, komanso mphamvu zanu zonse, ‘mudzalandira makumi khumi tsopano nthawi ino . . . ndipo nthawi ilinkudza, moyo wosatha.’—Marko 10:29, 30; 12:30.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena